Surah Nooh

Surah Nooh - Chewa Aya count 28

Adanena (Nuh): “E inu anthu anga! Ndithu ine ndimchenjezi kwa inu woonekera poyera (wolongosola za uthenga wa Mbuye wanu m’chiyankhulo chimene mukuchidziwa).”
“Mpembedzeni Allah ndipo rnuopeni ndikutinso mundimvere (pazimene ndikukulangizani).”
“(Ngati mutero) adzakukhululukirani machimo anu ndi kukutalikitsirani moyo wanu kufikira m’nthawi imene yaikidwa (kuti ndiwo malire a kutalika kwa moyo). Ndithu nthawi ya Allah ikabwera siyichedwetsedwa (ngakhale pang’ono) mukadakhala mukudziwa.”
Adanena (Nuh): “E Mbuye wanga! Ndithu ine ndaitanira anthu anga (ku chikhulupiliro) usiku ndi usana (popanda kufooka).”
“Kuitana kwanga sikudaonjezere (chilichonse) koma kuthawa basi (kuchikhulupiliro Chanu).”
Ndipo ine nthawi iliyonse ndikawaitanira (ku chikhulupiliro Chanu) kuti mwakhululukire, akuika zala zawo m’makutu mwawo (kuti asamve uthenga Wanu), ndipo akudziphimba ndi nsalu zawo (kuti asaone nkhope yanga), ndipo akupitiriza kukana kwawo ndi kudzikweza kwakukulu.
Choncho ndidati (kwa anthu anga): Pemphani kwa Mbuye wanu chikhululuko (pa kukana kwanu ndi kutonza kwanu), ndithu Iye ali Wokhululuka kwambiri.
Ndikukupatsani chuma ndi ana, (zomwe ndi zokongoletsa za dziko lapansi), ndi kukupangirani minda (yokongola) ndi kukupangirani mitsinje (yothilira mbewu zanu ndi kumwetsa ziweto zanu).
Kodi chifukwa ninji simupereka ulemu kwa Allah (woyenera Umulungu Wake kuti akakuchitireni chifundo ndi kukupulumutsani ku chilango)?
Pomwe Iye adakulengani mnjira zosiyanasiyana; (madzi a umunthu, kenako magazi, kenako magazi ochindikala, kenako mafupa ndipo kenako mnofu),
Kenako adzakubwezerani momwemo ndikudzakutulutsaninso (popanda cholepheretsa).
Adanena Nuh: “Mbuye wanga! Ndithu anthu anga andinyoza (pa zimene ndawalamula kuti akhulupirire Inu ndi kupempha chikhululuko chanu), ndipo (ofooka mwa iwo) amtsatira yemwe chuma chake ndi ana ake sizidzamuonjezera (chilichonse chabwino) koma kutaika (ndi kuonongeka pa tsiku lachimaliziro).
Ndipo (eni chuma ndi ana) awatchera (otsatira awo) ndale zazikulu (ndi zopyola muyeso kuti asakhulupirire).”
Ndipo adanena (kwa owatsatira awo): “Musasiye kupembedza milungu yanu; musamusiye Wadda, Suwaa’, Yaghutha, Ya’uqa ndi Nasra” (maina a mafano awo).
Ndipo ndithu iwo asokeretsa (anthu) ambiri; ndipo musawaonjezere ochita zoipa (china chake) koma kusokera basi.”
Ndipo adanena Nuh (atataya mtima za anthu ake): “Mbuye wanga! Musasiye aliyense mwa osakhulupirira kukhala pa dziko.”
“Ndithu Inu Mbuye wanga ngati muwasiya (popanda kuwaononga ndi kuwathetsa) asokeretsa akapolo anu (kunjira yolungama). Ndipo sangabereke (ana abwino) koma oipa; osakhulupirira (okhala kutali ndi choonadi, ndiponso onyoza Inu).”
“Mbuye wanga! Ndikhululukireni ndi makolo anga, ndi aliyense walowa m’nyumba yanga ali okhulupirira ndi okhulupirira amuna ndi okhulupirira akazi. Ndipo musawaonjezere anthu achinyengo chinachake koma kuwaononga basi.”
Share