Surah At-Talaq ( The Divorce )

Surah At-Talaq ( The Divorce ) - Chewa Aya count 12

E iwe Mneneri (s.a.w) ngati mufuna kusudzula akazi ukwati, asudzuleni mnyengo yowerengera Edda yawo (kuwerengera Edda kumayambika mkazi akakhala ndi Twahara akachira matenda akumwezi), ndipo werengerani nyengo ya Edda. Ndipo muopeni Allah Mbuye wanu. Ndipo musawatulutse m’nyumba zawo ndiponso asatuluke kupatula akachita tchimo lalikulu loonekera (loyenera chilango, apo atha kutulutsidwa). Ndipo amenewa ndiwo malire a Allah (amene wawakhazikitsa kwa anthu Ake). Ndipo amene apyola malire a Allah wadzichitira yekha zoipa. Sukudziwa (cholinga cha malamulo amenewa) mwina Allah adzadzetsa chinthu pambuyo pake (chosonyeza kuyanjana).
Choncho pamene iwo (osiyidwawo) nyengo yawo (Edda) itayandikira kutha, abwelereni mwa ubwino kapena asiyeni mwaubwino (polekelera nyengoyo kuti ithe); ndipo (powabwerera) funani mboni ziwiri zolungama zochokera mwa inu (zimene zichitire umboni kuti inu mukubwererana) ndipo perekani umboni chifukwa choopa Allah. Zimenezo ndizo akulangizidwa nazo amene akhulupirira mwa Allah ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo amene akumuopa Allah (potsatira malamulo Ake), amkonzera njira yotulukira (m’mavuto).
Ndipo ampatsa rizq kuchokera momwe samayembekezeramo. Ndipo amene akutsamira kwa Allah (pa zinthu zake zonse), ndiye kuti Allah ali wokwana kwa iye (kumkonzera chilichonse), ndithu Allah Ngokwaniritsa cholinga Chake ndi chofuna Chake. Ndithu chinthu chilichonse Allah wachipatsa mlingo wake woyenera (ndipo sichingaupyole).
Limenelo ndilamulo la Allah (lomwe) walikhazikitsa kwa inu. Ndipo amene aopa Allah (posunga malamulo ake), amam’fafanizira zoipa zake, ndiponso amamkulitsira malipiro ake.
Akhazikeni (osiyidwawo) m’mene mukukhala inumo monga momwe kulili kupeza kwanu (ndi mphamvu zanu ngakhale kuti mwawasiya ukwati). Musawavute ndi cholinga chowapana (kuti athawe okha). Ngati ali ndi pakati, apatseni zonse zofunika pa moyo mpaka adzabereke. Ngati akukuyamwitsirani ana anu apatseni malipiro awo mokwanira; gwirizanani pakati panu mwa ubwino ndi mofatsa. Ngati wina apereka mavuto kwa mnzake (ndiye kuti mwanayo) adzamuyamwitsira (mkazi) wina.
Ndipo ndimidzi ingati yomwe idanyoza lamulo la Mbuye wawo ndi Atumiki Ake, ndipo tidawawerenga ndi chiwerengero chokhwima (posanthula zochita zawo zonse). Ndiponso tidawalanga ndi chilango chaukali.
Choncho adalawa kuipa kwa zinthu zawo ndipo mapeto azinthu zawo adali kutayika (kuonongeka kwakukulu).
Share