Surah At-Taghabun ( Mutual Loss & Gain )

Surah At-Taghabun ( Mutual Loss & Gain ) - Chewa Aya count 18

Zonse zakumwamba ndi zam’dziko lapansi zikulemekeza Allah (ndi kumyeretsa ku zinthu zosayenerana ndi ulemelero Wake; ufumu Ngwake ndipo kutamandidwa kwabwino Nkwake. Ndipo Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse.
Iye ndiamene adakulengani (nonsenu popanda kuchokera ku chilichonse) choncho mwa inu alipo wosakhulupirira ndiponso mwa inu alipo wokhulupirira. Ndipo Allah Ngopenya zonse zimene mukuchita (ndipo adzakulipirani nazo).
(Allah) akudziwa za kumwamba ndi za m’dziko lapansi, ndiponso akudziwa zimene mukuzibisa ndi zimene mukuzilengeza (zochita ndi zoyankhula); Allah Ngodziwa za m’zifuwa.
Kodi siidakufikeni nkhani ya omwe sadakhulupirire kale? Adalawa (zowawa) za zoipa za zinthu zawo (pa dziko lapansi). Ndipo chilango chowawa chidzakhala pa iwo (tsiku lachimaliziro).
Zimenezo nchifukwa chakuti atumiki awo amawadzera ndi zozizwitsa koma iwo amanena (mwachipongwe): “Ha! Anthu anzathu (onga ife) angationgole?” Choncho sadakhulupirire (utumiki wawo) ndipo adanyoza (choonadi) potero Allah adawasiya (ndi kupanda chikhulupiliro kwawo) ndipo Allah Ngokwanira ndiponso Ngoyamikidwa.
Amene sadakhulupirire akumazinamiza kuti sadzaukitsidwa ku imfa. Nena (kwa iwo iwe Mtumiki{s.a.w}): “Sizili choncho pali Mbuye wanga, ndithu mudzaukitsidwa ku imfa, ndipo mudzauzidwa zimene mumachita (pa dziko lapansi). Zimenezo kwa Allah nzosavuta (kuzichita).”
(Kumbukirani) tsiku limene adzakusonkhanitsani chifukwa cha tsiku lakusonkhana (zolengedwa zonse), limenelo ndi tsiku lolephera; ndipo amene akhulupirira mwa Allah ndi kuchita zabwino, amfafanizira zoipa zake, ndipo akamulowetsa m’minda momwe pansi pake pakuyenda mitsinje; adzakhala m’menemo muyaya; kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.[365]
Koma amene sadakhulupirire natsutsa zozizwitsa Zathu (zimene zidaperekedwa kwa Aneneri Athu;) iwowo ndi anthu a ku Moto; adzakhala mmenemo nthawi yaitali, amenewo ndiwo mabwelero oipa.
Palibe vuto lililonse lingapezeke pokhapokha Allah atafuna; ndipo amene akhulupirira Allah, (Allah) aongola mtima wake (kuti ukhale wokhutira ndi chiweruzo cha Allah). Ndipo Allah Ngodziwa chinthu chilichonse.
E inu amene mwakhulupirira! Ndithu ena mwa akazi anu ndi ana anu ndiadani anu (chifukwa chakuti amakuchotsani kumbali yomvera Allah pofuna kuti mukwaniritse zofuna zawo). Chenjerani nawo. Ngati muwakhululukira ndi kunyalanyaza ndi kubisa zolakwa zawo ndibwino kwambiri, ndithu Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.[366]
Ndithu chuma chanu ndi ana anu ndimayesero (kwa inu); koma kwa Allah kuli malipiro akulu (kwa yemwe wasankha kumvera Allah).
Choncho muopeni Allah mmene mungathere, mverani (zophunzitsa Zake) ndipo tsatirani (malamulo Ake) komanso perekani zimene wakupatsani zikhala zabwino kwa inu. Dzichitireni nokha zabwino. Ndipo amene watchinjirizidwa ku umbombo wa mtima wake, iwowo ndiwo opambana.
Ngati mungamkongoze Allah ngongole yabwino aiwonjezera kwa inu (malipiro ake) ndipo akukhululukirani (zolakwa zanu.) Ndipo Allah Ngolandira kuthokoza, Ngoleza.
Share