Surah Al-Munafiqoon ( The Hypocrites )

Surah Al-Munafiqoon ( The Hypocrites ) - Chewa Aya count 11

Kulumbira kwawo (kwa bodza) akuchita kukhala chotetezera (chuma chawo ndi matupi awo). Tero atsekereza (anthu kuyenda) panjira ya Allah. Ndithu nzoipa zedi zimene amachita.
Zimenezo nchifukwa chakuti iwo adakhulupirira (modzionetsera), kenako adakana (mobisa). Choncho mitima yawo idatsekedwa kotero kuti iwo sangathe kuzindikira (chimene chingawapulumutse ku chilango cha Allah.)
Ndipo ukawaona, akukondweretsa matupi awo; ndipo akayankhula umvetsera zoyankhula zawo (chifukwa chakuthwa kwa malirime awo, pomwe mkati mwawo ndiming’oma yopanda kanthu); iwo ali ngati matsinde a mitengo yomwe yayadzamiritsidwa (ku chipupa); (mwa iwo mulibe moyo). Mkuwe uliwonse (umene akuumva) akuganiza kuti ukulinga iwo, (chifukwa cha kuzindikira chinyengo chawo); iwowa ndiadani; chenjerani nawo. Allah awatembelere! Mwanjira yanji akuchotsedwa (ku choonadi)!
Kukanenedwa kwa iwo kuti: “Bwerani, akupemphereni chikhululuko mthenga wa Allah, akutembenuza mitu yawo (monyoza ndi modzitukumula), ndipo uwaona akunyoza uku akudzikweza (osatsatira langizo).”
Kwa iwowa nchimodzimodzi kuwapemphera kwako chikhululuko, kapena kusawapemphera. Allah sangawakhululukire (chifukwa cha kuzama kwawo m’kusakhulupirira). Ndithu Allah saongola anthu otuluka m’chilamulo (Chake).
Amenewa ndiwo omwe akunena kwa Answari; (Asilamu aku Madina, kuti): “Musawapatse chuma (chanu) amene ali ndi Mtumiki wa Allah kuti abalalikane.” Pomwe nkhokwe zonse (zachuma) za kumwamba ndi dziko lapansi zili m’manja mwa Allah (ndipo amachipereka kwa amene wamfuna); koma achiphamaso sakuzindikira (zimenezo).[364]
Perekani (mwachangu pa njira ya Allah) zina mwa zomwe takupatsani, isanamfikire mmodzi wa inu imfa (mwadzidzidzi) ndi kuyamba kunena (modandaula): “Mbuye wanga! Bwanji osandichedwetsa nthawi pang’ono kuti ndipereke sadaka (ndi kuti ndikonze zina zimene sindinazikwaniritse) ndi kutinso ndikhale mwa anthu anu abwino.”
Ndipo Allah sangauchedwetse mzimu (ngakhale ndi mphindi imodzi) ukaidzera nthawi yake ya imfa; ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene mukuchita, (ndipo adzakulipirani pa zimenezo).
Share