Surah Al-Mumtahanah ( The Woman to be examined )

Surah Al-Mumtahanah ( The Woman to be examined ) - Chewa Aya count 13

E inu amene mwakhulupirira! Musawachite adani Anga ndi adani anu kukhala athandizi anu ndi kumawauza (nkhani zanu) mwa chikondi, pomwe iwo sanakhulupirire choonadi chimene chakudzerani. Adamtulutsa Mtumiki ndi inu nomwe (m’nyumba zanu) chifukwa chakuti mumakhulupirira Allah, Mbuye wanu, (palibe cholakwa chilichonse chimene mudawachitira,) ngati mwatuluka kukachita Jihâd pa njira Yanga ndi kufunafuna chikondi Changa (musapalane nawo ubwenzi). Mukuwatumizira chinsinsi (chanu cha nkhondo) chifukwa cha chikondi (chanu ndi iwo); (musachitenso zimenezi) pomwe Ine ndikudziwa zimene inu mukubisa ndi zimenene mukuzisonyeza (poyera); amene akuchita zimenezi mwa inu, ndiye kuti wataya njira yoongoka.[355]
Akakumana nanu (pankhondo) akukhala adani anu ndipo akukutambasulirani manja ndi malirime awo moipa (pokumenyani ndi kukutukwanani); ndipo akulakalaka mukadakhala osakhulupirira (kuti mufanane nawo).
Ndithu inu muli ndi chitsanzo chabwino cha (mtumiki) Ibrahim ndi amene adali naye pamene adawauza anzawo (osakhulupirira kuti): “Ndithu ife tapatukana nanu pamodzi ndi milungu yanu imene mukuipembedza kusiya Allah; takukanani, ndipo chidani ndi kusakondana zaonekera poyera pakati pa inu ndi ife mpaka muyaya, kufikira, mutakhulupirira mwa Allah mmodzi (inunso chitani chimodzimodzi, muwakane abale anu amene ali akafiri), kupatula mawu a Ibrahim pamene adamuuza tate wake (kuti): “Ndithu ndikupempherani chikhululuko. Palibe chimene ndingakutetezereni nacho kwa Allah (ngati mutamuphatikiza Allah ndi zina.”) E Mbuye wathu! Kwa Inu tatsamira. Ndipo kwa Inu tatembenukira ndiponso kobwerera nkwa Inu.[356]
E Mbuye wathu! Musatichite kukhala mayeso kwa amene sadakhulupirire, tikhululukireni Mbuye wathu! Ndithu Inu, Ndinu Amphamvu zopambana ndiponso Anzeru zakuya.
Ndithu muli nacho inu kwa iwo (Ibrahim ndi omtsatira) chitsanzo chabwino kwa amene akuyembekezera kukumana ndi Allah ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo amene anyozere ndithu Allah Ngolemera (ndiponso) Ngotamandika.
Mwina Allah angaike chikondi pakati panu ndi ena mwa amene mumawada (poiongolera mitima yawo kukhulupirira mwa Allah), ndipo Allah Ngokhoza chilichonse ndiponso Allah Ngokhululuka; Ngwachisoni chosatha.
E inu amene mwakhulupirira! Akakudzerani okhulupirira aakazi osamuka, ayeseni mayeso (kuti mudziwe chikhulupiliro chawo); Allah ali wodziwa kwambiri za chikhulupiliro chawo; ngati mutawadziwa kuti ndiokhulupirira musawabwezere kwa osakhulupirira. Akaziwo saloledwa kukwatiwa ndi osakhulupirira, iwonso saloledwa kuwakwatira. Abwezereni chiwongo chimene adapereka amuna osakhulupirirawo. Ndipo palibe tchimo kwa inu kuwakwatira, (ngakhale adasiya amuna awo achikafiri (ku Makka) ngati muwapatsa chiwongo chawo. Musakakamire maukwati ndi akazi achikafiri (osakhulupirira amene adatsalira ku Makka). Itanitsani zimene mudapereka kwa akazi anu (achikafiriwo), naonso Akafiri aitanitse zimene adapereka (kwa akazi awo akalowa m’Chisilamu). Limeneli ndi lamulo la Allah limene akulamula pakati panu. Allah ndiwodziwa kwambiri ndiponso Ngwanzeru (poika malamulo).
Ndipo ngati mmodzi mwa akazi anu atakuthawani kupita kwa Akafiri, ndipo (mwadzidzidzi) mwakachita nkhondo (ndi kupeza chuma chosiya adani anu), apatseni amene awathawa akazi awo chofanana ndi chimene adapereka (pokwatira). Ndipo muopeni Allah amene inu mukumkhulupirira.
E inu amene mwakhulupirira! Musagwirizane ndi anthu amene Allah wawakwiyira. Ndithu iwo ataya mtima wopeza mphoto tsiku lachimaliziro (chifukwa cha machimo awo ochuluka) monga momwe atayira mtima akafiri za kuuka kwa amene ali m’manda.
Share