Surah Al-An'am ( The Cattle ) - Aya 91

Surah Al-An'am ( The Cattle ) - Chewa - Aya 91 Aya count 165

وَمَا قَدَرُوا۟ ٱللَّهَ حَقَّ قَدْرِهِۦٓ إِذْ قَالُوا۟ مَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ عَلَىٰ بَشَرٍۢ مِّن شَىْءٍۢ ۗ قُلْ مَنْ أَنزَلَ ٱلْكِتَٰبَ ٱلَّذِى جَآءَ بِهِۦ مُوسَىٰ نُورًۭا وَهُدًۭى لِّلنَّاسِ ۖ تَجْعَلُونَهُۥ قَرَاطِيسَ تُبْدُونَهَا وَتُخْفُونَ كَثِيرًۭا ۖ وَعُلِّمْتُم مَّا لَمْ تَعْلَمُوٓا۟ أَنتُمْ وَلَآ ءَابَآؤُكُمْ ۖ قُلِ ٱللَّهُ ۖ ثُمَّ ذَرْهُمْ فِى خَوْضِهِمْ يَلْعَبُونَ ﴿٩١﴾
Koma (Ayuda) sadamulemekeze Allah monga momwe zikufunikira pomulemekeza pomwe adati: “Allah Sadavumbulutsepo chilichonse kwa munthu aliyense.” (Adanena izi pamene mtumiki adawauza kuti Qur’an ndi buku lomwe Allah wavumbulutsa). Nena: “Kodi ndani adavumbulutsa buku lomwe lidadza ndi Mûsa? Lomwe lidali kuunika ndi chiwongoko kwa anthu, lomwe mwalipanga kukhala magawo-magawo; zimene mwafuna kuonetsa kwa anthu mukuzionetsa. Koma zambiri mukubisa (zomwe sizigwirizana ndi zofuna zanu). Ndipo mwaphunzitsidwa (ndi iyi Qur’an) zomwe simudali kuzidziwa, inu ngakhale makolo anu. Nena: “Allah (ndi Yemwe wavumbulutsa iyi Qur’an ndi mabuku ena.”) Kenako asiye azingosewera m’kubwebweta kwawo (kopanda pake).
Share