فَلَمَّا رَءَا ٱلْقَمَرَ بَازِغًۭا قَالَ هَٰذَا رَبِّى ۖ فَلَمَّآ أَفَلَ قَالَ لَئِن لَّمْ يَهْدِنِى رَبِّى لَأَكُونَنَّ مِنَ ٱلْقَوْمِ ٱلضَّآلِّينَ ﴿٧٧﴾
Pamene adaona mwezi ukutuluka, adati: “Uyu ndiye mbuye wanga.” Koma pamene udalowa, adati: “Ngati Mbuye wanga sandiongolera, ndithudi, ndikhala m’gulu la anthu osokera.”