وَهُوَ ٱلَّذِى يَتَوَفَّىٰكُم بِٱلَّيْلِ وَيَعْلَمُ مَا جَرَحْتُم بِٱلنَّهَارِ ثُمَّ يَبْعَثُكُمْ فِيهِ لِيُقْضَىٰٓ أَجَلٌۭ مُّسَمًّۭى ۖ ثُمَّ إِلَيْهِ مَرْجِعُكُمْ ثُمَّ يُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ ﴿٦٠﴾
Iye ndiyemwe amakupatsani imfa (yatulo) nthawi yausiku, ndipo amadziwa zimene mwachita masana, kenako amakudzutsani mmenemo kuti ikwane nthawi yanu yoikidwa (yofera); kenako kwa Iye ndiko kobwerera kwanu, nadzakuuzani zimene munkachita.