Surah Al-An'am ( The Cattle ) - Aya 148
Surah Al-An'am ( The Cattle ) - Chewa - Aya 148 Aya count 165
سَيَقُولُ ٱلَّذِينَ أَشْرَكُوا۟ لَوْ شَآءَ ٱللَّهُ مَآ أَشْرَكْنَا وَلَآ ءَابَآؤُنَا وَلَا حَرَّمْنَا مِن شَىْءٍۢ ۚ كَذَٰلِكَ كَذَّبَ ٱلَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ حَتَّىٰ ذَاقُوا۟ بَأْسَنَا ۗ قُلْ هَلْ عِندَكُم مِّنْ عِلْمٍۢ فَتُخْرِجُوهُ لَنَآ ۖ إِن تَتَّبِعُونَ إِلَّا ٱلظَّنَّ وَإِنْ أَنتُمْ إِلَّا تَخْرُصُونَ ﴿١٤٨﴾
Amene akuphatikiza (Allah ndi mafano) anena: “Ngati Allah akadafuna, sitikadam’phatikiza, ife ngakhale makolo athu. Ndipo sitikadaletsa chilichonse. (Choncho, izi zomwe tikuchita, Allah akuziyanja). Momwemonso adatsutsa omwe adalipo patsogolo pawo kufikira adalawa chilango chathu. Nena: “Kodi muli nako kudziwa (kokutsimikizirani zimenezi), koti mungatitulutsire (umboni wake wotsimikizira kuti Allah adakulamulani zimenezi)? Inu simutsatira china, koma zongoganizira basi. Ndipo Simukunena china koma zabodza basi.”