Surah Al-An'am ( The Cattle ) - Aya 146
Surah Al-An'am ( The Cattle ) - Chewa - Aya 146 Aya count 165
وَعَلَى ٱلَّذِينَ هَادُوا۟ حَرَّمْنَا كُلَّ ذِى ظُفُرٍۢ ۖ وَمِنَ ٱلْبَقَرِ وَٱلْغَنَمِ حَرَّمْنَا عَلَيْهِمْ شُحُومَهُمَآ إِلَّا مَا حَمَلَتْ ظُهُورُهُمَآ أَوِ ٱلْحَوَايَآ أَوْ مَا ٱخْتَلَطَ بِعَظْمٍۢ ۚ ذَٰلِكَ جَزَيْنَٰهُم بِبَغْيِهِمْ ۖ وَإِنَّا لَصَٰدِقُونَ ﴿١٤٦﴾
(Izi ndi zomwe takuletsani). Naonso Ayuda tidawaletsa kudya nyama iliyonse yokhala ndi zikhadabu, ndipo ng’ombe ndi mbuzi tidawaletsa kudya mafuta ake kupatula mafuta omwe misana yake yasenza, kapena okhala m’matumbo, kapena omwe asakanikirana ndi mafupa. Tidawalipira izi chifukwa cha machimo awo. Ndithu Ife ndioona (pa zomwe tikunenazi).