Surah Al-An'am ( The Cattle ) - Aya 138
Surah Al-An'am ( The Cattle ) - Chewa - Aya 138 Aya count 165
وَقَالُوا۟ هَٰذِهِۦٓ أَنْعَٰمٌۭ وَحَرْثٌ حِجْرٌۭ لَّا يَطْعَمُهَآ إِلَّا مَن نَّشَآءُ بِزَعْمِهِمْ وَأَنْعَٰمٌ حُرِّمَتْ ظُهُورُهَا وَأَنْعَٰمٌۭ لَّا يَذْكُرُونَ ٱسْمَ ٱللَّهِ عَلَيْهَا ٱفْتِرَآءً عَلَيْهِ ۚ سَيَجْزِيهِم بِمَا كَانُوا۟ يَفْتَرُونَ ﴿١٣٨﴾
Iwo akuti: “Ziweto izi ndi mbewu izi, nzoletsedwa; palibe angazidye koma amene tawafuna (kuti adye),” zonsezi mkuyankhula kwawo kwachabe. Ndipo (amanenanso): “Ziweto izi, misana yake njoletsedwa (kukwerapo).” Ndipo pa ziweto zina satchula dzina la Allah pozizinga; kungompekera bodza Iye. Ndipo posachedwa adzawalipira pa zomwe adali kupeka.