Surah Al-An'am ( The Cattle ) - Aya 128

Surah Al-An'am ( The Cattle ) - Chewa - Aya 128 Aya count 165

وَيَوْمَ يَحْشُرُهُمْ جَمِيعًۭا يَٰمَعْشَرَ ٱلْجِنِّ قَدِ ٱسْتَكْثَرْتُم مِّنَ ٱلْإِنسِ ۖ وَقَالَ أَوْلِيَآؤُهُم مِّنَ ٱلْإِنسِ رَبَّنَا ٱسْتَمْتَعَ بَعْضُنَا بِبَعْضٍۢ وَبَلَغْنَآ أَجَلَنَا ٱلَّذِىٓ أَجَّلْتَ لَنَا ۚ قَالَ ٱلنَّارُ مَثْوَىٰكُمْ خَٰلِدِينَ فِيهَآ إِلَّا مَا شَآءَ ٱللَّهُ ۗ إِنَّ رَبَّكَ حَكِيمٌ عَلِيمٌۭ ﴿١٢٨﴾
Ndipo (akumbutse) tsiku limene adzawasonkhanitsa onse (nkuwauza): “E inu khamu la ziwanda! Ndithudi, mudatenga okutsatirani ambiri mwa anthu (powasokoneza).” Ndipo abwenzi awo mwa anthu adzati: “Mbuye wathu! Tidali kupindulitsana pakati pathu, ndipo tsopano taifikira nyengo yathu imene mudatiikira.” (Allah) adzati: “Malo anu ndi ku Moto. Mukakhala m’mmenemo nthawi yaitali, pokhapokha Allah akafuna.” Ndithu Mbuye wako Ngwanzeru zakuya, Ngodziwa kwambiri.
Share