Surah Al-An'am ( The Cattle ) - Aya 111
Surah Al-An'am ( The Cattle ) - Chewa - Aya 111 Aya count 165
۞ وَلَوْ أَنَّنَا نَزَّلْنَآ إِلَيْهِمُ ٱلْمَلَٰٓئِكَةَ وَكَلَّمَهُمُ ٱلْمَوْتَىٰ وَحَشَرْنَا عَلَيْهِمْ كُلَّ شَىْءٍۢ قُبُلًۭا مَّا كَانُوا۟ لِيُؤْمِنُوٓا۟ إِلَّآ أَن يَشَآءَ ٱللَّهُ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَهُمْ يَجْهَلُونَ ﴿١١١﴾
۞ Ndipo ngati tikadawatumizira angelo (kuti adzaikire umboni za uneneri wako), ndipo akufa nkuwayankhula, (naonso nkuvomereza kuti izi nzoona; kuonjezera apo) nkuwasonkhanitsira chinthu chilichonse pamaso pawo, sakadakhulupirira pokhapokha Allah akadafuna koma ambiri a iwo sazindikira.