Surah Al-Mujadilah ( She That Disputeth )

Surah Al-Mujadilah ( She That Disputeth ) - Chewa Aya count 22

۞ Ndithu Allah wamva mawu a (mkazi) amene akubwezeranabwezerana nawe (mawu) pa za mwamuna wake (amene adamsala); ndipo akusuma kwa Allah. Ndipo Allah akumva kukambirana kwanu; ndithu Allah Ngwakumva, Ngopenya (chilichonse).[347]
Ndipo amene akuwafanizira akazi awo (ndi amayi awo) kenako nkubweza zimene adanena, apereke ufulu kwa kapolo asanakhale malo amodzi (ndi mkaziyo). Amenewa ndi malamulo a Allah kwa inu (amene) mukuchenjezedwa nawo. Ndipo Allah akudziwa zimene mukuchita (zoonekera poyera ndi zosaonekera choncho sungani malamulo amene Allah wakhazikitsa pa inu).
Ndipo amene sadapeze (kapolo) asale miyezi iwiri yondondozana asadakhalirane pamodzi (ndi mkaziyo), koma amene sadathe kusala adyetse masikini makumi asanu ndi limodzi (60). Izi (zalamulidwa) kuti mukhulupirire mwa Allah ndi Mthenga Wake. Amenewo ndiwo malire a Allah; (malamulo okhazikitsidwa ndi Allah choncho musawalumphe). Ndipo chilango chopweteka chili pa osakhulupirira.
Ndithu amene akutsutsana ndi Allah kudzanso Mthenga Wake, ayalutsidwa monga momwe adayalutsidwira amene adalipo patsogolo pawo; ndithu tavumbulutsa Ayah zolongosola, momveka (pa zololedwa ndi zoletsedwa). Ndipo chilango choyalutsa chili pa osakhulupirira.
(Kumbuka) tsiku limene Allah adzaukitsa akufa onse ndi kuwafotokozera zimene adachita (pa moyo wa dziko lapansi: zoipa ndi zabwino); Allah adazisunga mozilemba koma iwo adaziiwala. Ndipo Allah ndi mboni wa zonse (palibe chingabisike kwa Iye).
Kodi sukudziwa (iwe, womvera wanzeru) kuti Allah akudziwa zakumwamba ndi zam’dziko lapansi? Sipakhala manong’onong’o a (anthu) atatu koma Iye Ngwachinayi wawo (ndi kudziwa kwake kosabisika chilichonse cha kumwamba ndi m’dziko), ngakhale a (anthu) asanu koma Iye Ngwachisanu ndi chimodzi wawo (mkudziwa Kwake), ngakhale ali ochepera kuposera pamenepa kapena ochulukira koma Iye ali nawo paliponse pomwe ati akhale (Allah ali nawo pamodzi mukudziwa Kwake kosabisika chilichonse), kenako adzawafotokozera pa tsiku la chiweruziro zimene adachita; ndithu Allah Ngodziwa chilichonse (mokwanira).[348]
Kodi siudaone! Kwa amene aletsedwa kunong’onezana zoipa pakati pawo, kenako akubwereza zimene adaletsedwa? Akunong’onezana za machimo, mtopola ndi kunyoza Mtumiki. Akakudzera akukulonjera (ndi malonje achinyengo) amene Allah sadakulonjerepo nawo ndipo akunena m’mitima mwawo: “Kodi nchifukwa chiyani Allah sakutilanga ndi mawu tikunenawa (ngati iyeyu ndi Mtumikidi wa Allah?” Jahannam ikuwakwanira: adzailowa. Ndipo taonani kuipa malo (awo) wobwerera! [349]
Ndithu manong’onong’o oipa amachokera kwa satana kuti adandaulitse amene akhulupirira; koma sangawapweteke nawo chilichonse kupatula Allah atafuna ndipo okhulupirira atsamire kwa Allah Yekha, (asalabadire zonong’onezana zawo).
E inu amene mwakhulupirira! Kukapemphedwa kwa inu kuti perekani malo pabwalo (pokhala), perekani malowo (kuti anzanu apeze pokhala; mukatero) Allah akuphanulirani (chifundo Chake pano pa dziko ndi kumwamba). Ndipo kukanenedwa kuti imilirani, muimilire (musanyozere, apatseni ena malo); Allah awakwezera (ulemelero) mwa inu amene akhulupirira ndi amene apatsidwa nzeru. Ndipo Allah akudziwa bwino zimene mukuchita.[350]
Kulumbira kwawo adakuchita kukhala chodzitetezera (iwo, ana awo ndi chuma chawo); choncho adatsekereza (anthu) ku njira ya Allah; choncho chilango choyalutsa chili pa iwo.[351]
(Alikumbukire) tsiku limene Allah adzawaukitsa (ku imfa) onse, adzayamba kulumbira kwa Iye (zabodza) monga akulumbira (zabodza) kwa inu. Ndipo akuganiza kuti apezapo kanthu (pakulumbira kwawo). Dziwani, ndithudi, iwo ndi abodza.
Allah adalamula (kuti): “Ndithu ndipambana Ine ndi atumiki Anga.” Ndithu Allah ndiwanyonga zokwana, Wopambana (sapambanidwa ndi aliyense).
Share