Surah Ar-Rahman ( The Most Graciouse )

Surah Ar-Rahman ( The Most Graciouse ) - Chewa Aya count 78

(Allah) Wachifundo chochuluka!
Zomera zopanda tsinde ndi mitengo, zikulambira (Allah pachilichonse chimene wafuna mwa izo).
Ndipo thambo adalitukula kumwamba ndipo adakhazikitsa sikelo (ya chilungamo).
Kuti musapyole malire ndi kuchita chinyengo poyesa.
Ndipo nthaka adaiyala (ndi kuikonza) kuti ikhale ya zolengedwa.
M’menemo muli zipatso ndi mitengo ya kanjedza yokhala ndi mapava (a zipatso).
Ndi mbewu zamakoko (kuti chikhale chakudya cha inu ndi ziweto zanu), ndipo mulinso m’menemo mmera wafungo labwino.
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)

Adaika nyanja ziwiri zokumana (yamadzi amchere, ndi yamadzi ozizira).
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
M’menemo mumatuluka ngale zing’onozing’ono ndi ngale zikuluzikulu.
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
Ndipo (Iye) ali nazo zombo (zimene zapangidwa ndi manja anu), zoyenda panyanja, zazikuluzikulu ngati mapiri.
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
(Onse) akumwamba ndi pansi akupempha Iye (zofuna zawo)! Tsiku lililonse Iye ali ndi zochita (monga kupatsa uyu ulemelero, ndi kutsitsa uyu).
(Inu zolengedwa zamitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
Posachedwapa (patsiku la chiweruziro), tidzaikapo mtima pa chiwerengero chanu (cha zochita zanu) inu anthu ndi ziwanda.
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
Mudzathiridwa malawi a moto ndi mtovu wa moto wosungunuka ndipo simungathe kupulumuka (ku chilango chimenechi).
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
(Kumbuka) pamene thambo lidzang’ambika ndi kukhala lofiira ngati chikopa chofiira (kapena ngati mafuta oyaka).
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
Adzadziwika oipa (pakati pa anthu ndi ziwanda) ndi zizindikiro zawo (zowazindikiritsa). Ndipo adzagwidwa maliombo awo ndi mapazi awo (ndi kuponyedwa ku Jahena).
((Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
Adzakhala akuyenda pakati pa moto ndi pakati pa madzi owira, otentha kwambiri.
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
Koma amene waopa kuti adzaimitsidwa kwa Mbuye wake (pa nthawi ya chiweruziro), adzalandira minda iwiri (yaikulu yamtendere).
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
(Minda ya mitengo) yanthambi zofwanthamuka.
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
M’menemo muli zipatso za mtundu uliwonse, mitundu iwiri iwiri.
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
M’mindamo muli akazi oyang’ana amuna awo okha basi, (mawuthu) omwe sadakhalepo malo amodzi ndi munthu kapena chiwanda asadakumane ndi iwo.
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
Kukongola kwake (akaziwo) kuli ngati ngale zikuluzikulu ndi zing’onozing’ono.
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
Ndipo kuonjezera paminda iwiri (ija) palinso minda ina iwiri.
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
M’menemo muli akasupe awiri ofwamphuka madzi mwaphamvu.
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
M’menemo muli akazi amakhalidwe abwino, owala nkhope.
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
Okongola maso, achikhalire m’mahema (m’matenti) awo.
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
Amene sadakhalepo malo amodzi ndi munthu kapena chiwanda asadakumane ndi iwo.
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
Uku atatsamira misamiro yawofuwofu yokutidwa ndi zobiriwira; ndi zoyala zokongola, zakapangidwe kabwino.

Share