Surah An-Najm ( The Star )

Surah An-Najm ( The Star ) - Chewa Aya count 62

Ndikulumbira nyenyezi pamene zikulowa.
Sadasokere m’bale wanu (Mtumiki panjira ya choonadi) ndipo sadakhulupirire zonama.
Iyoyi (Qur’an imene akuinena), sichina, koma ndichivumbulutso chovumbulutsidwa.
Adamphunzitsa (chivumbulutsochi) (Jibril) wanyonga zambiri.
Wanzeru zakuya; ndipo adakhazikika (m’maonekedwe ake).
Kenako (Jibril) adamuyandikira (Mtumiki {s.a.w}) ndikuonjezera kumuyandikira.
(Kumuyandikira kwake) kudali ngati (mpata wa) nsonga ziwiri za uta, kapena kuyandikira kuposa apo.
(Choncho Jibril) adavumbulutsira kapolo wake (wa Allah) zimene adazivumbulutsa.
Kodi mukutsutsana naye (Mthenga wa Allah) pazimene adaziona?
Ndipo ndithu adamuona (Jibril) m’kuona kachiwiri mkaonekedwe kake.
Pa ‘Sidratil Muntaha’ (mtengo wamasawu pothera zinthu zonse).
Pafupi pake pali Janatu Ma’awa, (munda wokhalamo).
Maso ake sadaphonye kapena kupyola malire (oikidwa).
Ndithu (Mneneri Muhammad {s.a.w}) adaona zina mwa zizindikiro zikuluzikulu za Mbuye wake (zosonyeza mphamvu Zake)
Ndi Manata; (fano lanu) lina lachitatu, (kuti iwowa ndi milungu)?
Kodi mwadzisankhira ana aamuna (kukhala anu), ndi aakazi nkukhala a Iye (Allah)?
Choncho kugawa kumeneko nkopanda chilungamo (pompatsa Allah zimene mumazida).
Sali (mafanowo) chilichonse koma ndi maina basi omwe mudawatcha inu ndi makolo anu, (molingana ndi zilakolako zanu zachabe); Allah sadatsitse umboni pazimenezo (wotsimikiza pamawu anuwo). Sakutsatira koma zoganizira basi ndi zimene ikufuna mitima (yawo yopotoka). Ndithu chidawadzera chiongoko kuchokera kwa Mbuye wawo (chomwe m’kati mwake mudali kuongoka kwawo akadachitsatira).
Kodi munthu akuganiza kuti adzapeza chilichonse chimene akuchilakalaka?
Moyo wa tsiku lachimaliziro ndi wadziko lapansi ngwa Allah Yekha.
Choncho apewe (osakhulupirirawa) amene anyozera chikumbutso Chathu (Qur’an); ndipo palibe chimene akufuna koma moyo wa padziko lapansi basi.
Ndipo zonse za kumwamba ndi zadziko lapansi nza Allah Yekha, (pozilenga ndi kuziyang’anira), kuti adzawalipire amene adaipitsa pa zimene adachita ndi kutinso adzawalipire zabwino amene adachita zabwino.
Amene akuwapewa machimo akuluakulu ndi zadama, kupatula timachimo tating’onoting’ono (timene Allah amatikhululuka); ndithu Mbuye wako ndiwokhululuka kwakukulu. Iye akudziwa chikhalidwe chanu kuyambira pomwe adakulengani kuchokera m’nthaka ndi pamene inu mudali makanda m’mimba mwa amayi anu (mosinthasintha; mosiyanasiyana). Choncho musadzitame nokha kuyera mtima; Iye Ngodziwa kwambiri za yemwe akumuopa (Allah).
Kodi wamuona yemwe wadzipatula (pakusiya kutsatira choonadi)?
Ndipo wapereka (chuma) chochepa nasiyanso kuperekako.
Kodi akudziwa zamseri, kotero kuti akuziwona (zomwe wadza nazo (Mtumiki {s.a.w) kuti sizoona)?
Ndi Ibrahim amene adakwaniritsa (lonjezo la Allah)?
Kenako (munthu) adzalipidwa malipiro okwanira (pa ntchito zake zimene amachita).
Ndipo ndithu kwa Mbuye wako yekha ndiwo malekezero (a chilichonse).
Ndithu Iye ndiAmene amapereka chisangalalo ndi zoliritsa.
Ndipo Iye yekha ndi Amene amapereka imfa ndi moyo.
Ndipo Iye ndiAmene adalenga mitundu iwiri: chachimuna ndi chachikazi, (anthu ndi zamoyo zina).
Kuchokera m’mbewu ya moyo pamene imafwamphukira (m’chiberekero).
Ndipo ndithu ndi udindo Wake kuukitsa kwina (pambuyo pa imfa).
Ndipo Iye ndiAmene amapatsa chokwanira ndipo ndi amene amapatsa chosunga.
Ndipo ndithu Iye ndi Mbuye wa nyenyezi yotchedwa Shiira;
Ndipo Iye ndi amene adaononga Âdi oyamba; (anthu a Mneneri Hûd).
Ndi Samudu; (anthu a Mneneri Swaleh;) choncho sadasiye (ndi mmodzi yemwe wa iwo).
Ndipo (adawaononganso) anthu a Nuh, kale (asadaononge Âdi ndi Samudu). Ndithu iwo adali osalungama ndi olumpha malire kwambiri (kuposa Âdi ndi Samudu).
Ndi midzi yotembenuzidwa kumwamba kukhala pansi, pansi kukhala kumwamba, (ya anthu a Luti) adaigwetsa.
Tero chidaivindikira (midziyo) chomwe chidaivindikira (chilango).
Kodi ndimtendere uti (mumtendere) wa Mbuye wako umene ukuukaikira?
Uyu (Mtumiki) ndimchenjezi mwa achenjezi oyamba (amene adachenjezedwa nawo anthu a mibadwo yakale)
Chayandikira choyandikira (Qiyâma).
Mungoseka (mwachipongwe) ndipo simukulira (pamene mukuimva monga momwe akuchitira okhulupirira).
Mlambireni ndi kumpembedza Allah (amene wavumbulutsa Qur’an kuti ikhale chiongoko cha anthu).
Share