Surah At-Tur ( The Mount )

Surah At-Tur ( The Mount ) - Chewa Aya count 49

Ndikulumbilira phiri la Turi (ku Sinai pamene Mûsa adalankhulana ndi Allah).
M’mipukutu yazikopa zotambasuka (zosavuta kuwerenga).
Ndi nyumba yopitako kawirikawiri (pochitamo mapemphero).
Ndi thambo limene latukulidwa (popanda mzati).
Ndithu chilango cha Mbuye wako (chimene wawalonjeza nacho osakhulupirira) chiwapeza (popanda chipeneko).
Pa tsikulo thambo lidzagwedezeka; kugwedezeka kwamphamvu.
Ndipo mapiri adzayenda mwamphavu (kuchoka m’malo mwake).
Kuonongeka koopsa pa tsiku limenelo kuzakhala pa otsutsa choonadi.
Tsiku limene adzakankhidwira mwamphamvu ku Jahannam (ku Moto Woopsa).
(Kudzanenedwa kwa iwo): “Uwu ndi Moto uja umene mudali kuutsutsa (pa dziko lapansi)
Ndithu oopa Allah adzakhala m’Minda yamtendere ndi chisangalalo chachikulu.
(Kudzanenedwa kwa iwo): “Idyani (chakudya chamtendere); ndipo imwani mosangalala kukhala malipiro pazimene munkachita (pa dziko lapansi).”
Uku atakhala moyadzamira pa makama ondandika bwino ndi kuyalidwa bwino; ndipo tidzawakwatitsa akazi ophanuka maso mokongola.
Azikalandirana m’menemo (mwachikondi wina ndi mnzake) chikho chodzaza ndi zakumwa; sipakakhala kwa iwo zolankhula zachabe ngakhale zochita zamachimo.
Azidzatembenukirana wina ndi mnzake uku akufunsana (za kukula kwa mtendere umene adzakhala nawo ndi kuti adaupeza chotani).
Adzanena: “Ife tidali oopa chilango cha Allah pakati pa maanja athu (tisadalandire mtenderewu).
Ndithu ife timampembedza (kalero pa dziko lapansi) ndithu Iye Yekha Ngwabwino, Ngwachifundo.”
Kodi akunena kuti: “Wadzipekera (Mtumiki {s.a.w} Qur’an)?” Iyayi, koma iwo sakukhulupirira.
Tero abwere ndi nkhani yofanana ndi iyo (Qur’an) ngati ali owona m’kuyankhula kwawo (koti Mtumiki{s.a.w} wapeka Qur’an.)
Kapena adalengedwa popanda Mlengi kapena iwo adadzilenga okha (nchifukwa sakuvomereza za Mlengi Wopembedzedwayo?)
Kapena ndiwo adalenga thambo ndi nthaka? Koma satsimikiza (zoyenera kumchitira Mlengi).
Kapena nkhokwe (za zabwino) za Mbuye wako zili ndi iwo (kotero kuti akuzigwiritsa ntchito mmene angafunire?) Kapena iwo ngopambana?
Nanga kapena ali nawo makwelero (amene akukwelera kumwamba) kotero kuti akumvetsera zimene Allah akulamula? Choncho, omvetsera awo abwere nawo umboni owonekera (osonyeza kuona kwawo pa zimene akunenazi).
Kapena Iye (Allah) ndiye ali ndi ana akazi ndipo inu muli ndi ana amuna?
Kapena ukuwapempha malipiro alionse (pofikitsa uthenga); kotero kuti iwo akulemedwa ndi kulipira (uthengawu)?
Kapena iwo amadziwa zamseri kotero kuti iwo akumalemba (zimene afuna)?
Kapena akufuna kukuchitira chiwembu (ndikuononga uthenga wako?) Koma amene sadakhulupirire ndiwo omwe chiwabwelere chiwembu (chawo.)
Kodi ali naye wompembedza, osati Allah (amene angawateteze ku chilango cha Allah)? Allah wapatukana ndi zimene akumuphatikiza nazo.
Koma akaona gawo lathambo likugwa (kuti liwalange) akunena (mwamakani ndi kunyada): “Uwu ndi mtambo umene wasonkhanitsa madzi a mvula.”
Choncho asiye; (usalabadire za iwo) mpaka pomwe adzakumana ndi tsiku lawo limene adzaonongedwa.
Ndipo ndithu amene achita zosalungama ali nacho chilango china chosakhala chimenecho (chisanawapeze chilango cha ku Âkhira)! Koma ambiri a iwo sadziwa (zimenezi).
Ndipo pirira ndi lamulo la Mbuye wako ndithu iwe ndiwe wosungidwa ndi kuyang’aniridwa ndi Ife; ndipo lemekeza ndi kumuyamika Mbuye ako pamene ukuimilira (kupemphera).
Share