Surah Qaf ( The Letter Qaf )

Surah Qaf ( The Letter Qaf ) - Chewa Aya count 45

Koma akudabwa chifukwa chowadzera Mchenjezi wochokera mwa iwo. Ndipo osakhulupirira adanena: “Ichi nchinthu chodabwitsa.”
Kodi tikadzafa ndi kukhala fumbi (tidzaukanso?) Kubwerera kumeneko nkwakutali kwambiri, (nkosatheka).”
Ndithu tikudziwa chimene nthaka ikuchepetsa m’matupi mwawo (akalowa m’manda). Ndipo kwa Ife kuli kaundula wosungidwa.
(Kuti zimenezi zikhale) chotsekula maso ndi chikumbutso kwa munthu aliyense wotembenukira (kwa Allah).
Ndipo tatsitsa madzi odalitsidwa kuchokera ku mitambo, ndipo kupyolera m’madziwo, tameretsa (mmera) m’minda ndi mbewu zokololedwa.
Ndi mitengo italiitali ya kanjedza yokhala ndi mikoko yazipatso zothothana.
(Kuti chikhale) chakudya cha akapolo (a Allah); ndi madziwo taukitsa dziko lakufa (louma). Momwemo ndimmene kudzakhalira kutuluka m’manda (muli moyo).
Ndi anthu a m’mitengo (ya Aika), ndi anthu a Tubba; onsewo adatsutsa Aneneri; choncho chenjezo Langa lidatsimikizika (pa iwo).
Ndithu tidamulenga munthu, ndipo Ife tikudziwa zimene mtima wake ukumunong’oneza; ndipo Ife tili pafupi ndi iye kuposa mtsempha wam’khosi mwake (wolumikizana ndi mtima).
Ndipo pamene amalandira olandira awiri (angelo), wina amakhala kudzanja lamanja, wina kudzanja lamanzere.
Palibe chilichonse chimene amayankhula koma pafupi ndi iye pali mlonda amene wakonzekera (kulemba).
Ndipo kuledzera kwa imfa kukam’dzera mwa choona, (pamenepo adzauzidwa): “Ichi ndi chomwe mumachithawa chija.”
Ndipo lipenga lidzaimbidwa; limenelo ndilo tsiku lamavuto (tsiku lachiweruziro).
(Adzauzidwa): “Ndithu udali wosalabadira zinthu izi; basi takuvundukulira (chomwe) chimakuphimba, ndipo kuyang’ana kwako lero nkwakuthwa!”
Ndipo (Mngelo) yemwe adali naye (pamodzi ndikumalemba zochita zake) adzanena (kwa Mngelo wachilango): “Izi ndizimene zidakonzedwa ndi ine.”
Mnzake (satana) adzanena: “E Mbuye wathu! Sindidamsokeretse, koma iye mwini adali wosokera kutali kwambiri ndi choonadi”.
“Izi ndizimene mumalonjezedwa, za aliyense wotembenukira kwa Allah, Wosunga (malamulo Ake).
Amene adaopa (Allah), Wachifundo chambiri, pomwe samamuona ndi maso, ndipo adadza ndi mtima wotembenukira (kwa Iye).”
(Adzauzidwa): “Uloweni mwamtendere.” Limeneli ndi tsiku lokhazikika mpaka muyaya.
M’menemo adzapeza chilichonse (chimene) adzafune, ndipo kwa Ife kuli zoonjezera.
Ndithu m’zimenezi muli chikumbutso kwa yemwe ali ndi mtima ndi yemwe akutchelera khutu (uku) iye ali pompo (ndi maganizo ake).
Choncho, pirira nazo zomwe akunenazo, ndipo lemekeza Mbuye wako pomutamanda dzuwa lisadatuluke, (Swala ya Subh), ndi (dzuwa) lisadalowe, (Swala ya Asr),
Ndi gawo lausiku, (Swala ya Maghrib ndi Isha); ndiponso (mulemekeze) pambuyo pa mapemphero (popemphera Swala za Sunna).
Ndithu Ife ndi amene timapereka moyo ndi kupereka imfa; ndipo kobwerera Nkwathu.
(Akumbutse za) tsiku limene nthaka idzang’ambike kwa iwo mwachangu; kusonkhanitsa kumeneko nkosavuta kwa Ife.
Share