Surah Al-Maidah ( The Table spread with Food )

Surah Al-Maidah ( The Table spread with Food ) - Chewa Aya count 120

E inu amene mwakhulupirira! Kwaniritsani mapangano onse (omwe ali pakati panu ndi anthu anzanu). Kwalolezedwa kwa inu (kudya nyama ya) ziweto (monga ngamira, ng’ombe ndi mbuzi), kupatula chomwe mukuuzidwa (kuti ncholetsedwa). Koma nkosaloledwa kwa inu kuchita ulenje mutalowa m’mapemphero a Hajj, (kapena muli m’nthaka yopatulika ya ku Makka). Ndithudi, Allah akulamula chimene wafuna.[155]
E inu amene mwakhulupirira! Musanyozere kupatulika kwa zizindikiro za Allah (pochiyesa chosapatulika chomwe Allah wachichita kukhala chopatulika; monga kutuluka m’mapemphero a Hajj usadakwaniritse), kapenanso (kunyozera) kupatulika kwa mwezi wopatulika (poyambitsa nkhondo mmenemo), kapena (kupatulika kwa nyama zomwe zatumizidwa ku Makka monga) nsembe, kapena (kuchotsa kupatulika kwa) makoza (omwe nyamazo zimavekedwa monga chizindikiro chosonyeza kuti ndinsembe ya ku Makka), kapena (kupatulika kwa) omwe akulinga kupita kunyumba yopatulika (ku Makka), (omwe akupita kumeneko) ndi cholinga chofunafuna ubwino wa Mbuye wawo ndi chiyanjo Chake. Ndipo ngati mutatuluka m’mapemphero anu a Hajj mukhoza kuchita ulenje (ngati mutafuna); ndipo kusakuchititseni kuwada anthu chifukwa chakuti adakutsekerezani kufika ku Msikiti Wopatulika (wa ku Makka) kuti mulumphe malire (pobwezera mtopola umene adakuchitirani). Koma thandizanani pa zabwino ndikuopa (Allah); musathandizane pa machimo ndi pa chidani. Ndipo muopeni Allah. Ndithu Allah Ngwaukali pokhaulitsa.
Kwaletsedwa kwa inu (kudya) chakufa chokha, liwende, nyama ya nkhumba, chomwe chazingidwa m’dzina osati la Allah, chomwe chafa ndi kubanika, chomwe chafa ndi kumenyedwa, ndi chimene chafa pakugwa kuchokera pamwamba, chimene chafa polasidwa ndi nyanga (yachinzake), chomwe chafa pakujiwa ndi chilombo (cha m’thengo) kupatula chomwe mwachipeza chili rnoyobe nkuchizinga ndi chimene chazingidwa paguwa la mafano; ndiponso (nkoletsedwa kwa inu) kufuna kudziwa zobisika pochita maula. Zonsezi ndi uchimo. Lero amene sadakhulupirire ataya mtima (za kugonjetsa) chipembedzo chanu. Choncho musawaope, koma opani Ine. Lero ndakukwaniritsirani chipembedzo chanu ndipo ndakwaniritsa pa inu chisomo changa. Ndakusankhirani Chisilamu kukhala chipembedzo chanu. Koma amene wasimidwa chifukwa chanjala, popanda kupendekera kumachimo, (nkudya zoletsedwazi, palibe kanthu). Ndithu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.[156]
Akukufunsa (Asilamu) chomwe chaloledwa kwa iwo (kudya). Nena: “Chaloledwa kwa inu chilichonse chabwino. Ndi (chimene chagwidwa ndi) nyama kapena mbalame zaukali zomwe mwaziphunzitsa kusaka. Muziphunzitse zimene Allah wakuphunzitsani. Choncho idyani chimene zakugwilirani, ndipo chitchulireni dzina la Allah pochikhwirizira. Ndipo opani Allah. Ndithudi Allah Ngwachangu pakuwerengera.[157]
“E inu amene mwakhulupirira! Pamene mwaimilira kuti mukaswali, sambitsani nkhope zanu, ndi manja anu mpaka mmagongono; ndipo pakani madzi pa mitu panu ndi kusambitsa mapazi anu mpaka mu akakolo. Ngati muli ndi janaba dziyeretseni (sambani thupi lonse); ndipo ngati muli odwala kapena muli paulendo, kapena mmodzi wanu wachokera kokadzithandiza kapenanso mwakhalira limodzi ndi mkazi, ndiye simudapeze madzi, chitani Tayammamu ndi dothi labwino ndipo pakani ku nkhope zanu ndi mmanja mwanu. Allah sakufuna kukuvutitsani, koma akufuna kukuyeretsani ndi kukwaniritsa chisomo chake pa inu kuti muthokoze.
Choncho chifukwa chakuswa pangano lawo, tidawatembelera; ndipo tidaumitsa mitima yawo. Ankasintha mawu (a Allah omwe adali m’mabuku a Taurat ndi Injili) kuwachotsa m’malo mwake ndipo adasiya kukwaniritsa gawo lalikulu la zomwe adakumbutsidwa. Ndipo ukhala ukuona (iwe Mtumiki {s.a.w}) chinyengo mwa ambiri a iwo, kupatula ochepa a iwo. Choncho akhululukire ndi kuwaleka. Ndithudi, Allah amakonda ochita zabwino.[159]
E inu anthu a buku! Ndithudi wakufikani Mtumiki Wathu yemwe akukufotokozerani poyera zambiri zomwe munkabisa za m’buku. Koma akusiya zambiri (posazilongosola). Ndithudi kwakudzerani kuunika kochokera kwa Allah ndi buku lomwe likufotokoza mwatchutchutchu (chinthu chilichonse).
(Ndipo kumbukirani) pamene Mûsa adauza anthu ake: “Inu anthu anga! Kumbukirani mtendere wa Allah umene uli pa inu, pamene adawachita ena mwa inu kukhala aneneri; ndipo adakuchitani kukhala mafumu (pambuyo poti mudali onyozeka m’dziko la Iguputo m’manja mwa Farawo). Ndipo wakupatsani zomwe sadampatsepo aliyense mwa zolengedwa.” [162]
(Mûsa) adati: “E Mbuye wanga! Ndithudi, ine ndilibe nyonga (yokakamizira aliyense kutsatira lamulo Lanu) koma pa ine ndekha ndi pa m’bale wanga. Choncho tisiyanitseni ndi anthu awa opandukira chilamulo.”
Ndipo awerengere nkhani mwachoonadi ya ana awiri a Adam, pamene adapereka nsembe. Ndipo idalandiridwa ya mmodzi wawo, koma ya winayo siidalandiridwe. (Amene nsembe yake siidalandiridwe) adati (kwa mnzake): “Ndithudi ndikupha.” Mnzakeyo adati: “Ndithudi, Allah amalandira nsembe ya amene akuopa (Allah).”[163]
“Ine ndikufuna kuti usenze machimo anga pamodzi ndi machimo ako, choncho ukakhale m’gulu la anthu a ku Moto. Ndipo awo ndio malipiro a anthu ochita zoipa.”
Ndithu mphoto ya amene akulimbana ndi Allah ndi Mtumiki Wake (pochita zomwe waletsa) ndi kudzetsa chionongeko pa dziko, aphedwe kapena apachikidwe pa mtanda, kapena adulidwe manja awo ndi miyendo yawo mosemphanitsa (dzanja lakumanja ndi phazi lakumanzere, ndipo dzanja lakumanzere ndi phazi lakumanja); kapena apirikitsidwe mdzikomo. Uku ndikuyaluka kwawo pa dziko lapansi. Ndipo iwo pa tsiku lachimaliziro adzalandira chilango chachikulu.[164]
Koma amene walapa pambuyo pakuchita kwake zoipa, namachita zabwino, Allah alandira kulapa kwake. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwabasi Ngwachisoni chosatha.[165]
E iwe Mtumiki! Asakudandaulitse amene akuchita changu kukana Allah mwa omwe akunena ndi pakamwa pawo chabe: “Takhulupirira,” pomwe mitima yawo siikukhulupirira. Namonso mwa Ayuda, alipo amene amamvetsera (zimene ukunena) kuti azikanena bodza, amamvetsera mmalo mwa anthu ena amene sadadze kwa iwe (omwe ndi akuluakulu awo), amasintha mawu (a m’buku la Taurat) m’malo mwake, omwenso amanena (kuuza otsatira awo kuti): “Ngati mukapatsidwe (ndi Muhammad {s.a.w}) izi (takuuzanizi), kalandireni, koma ngati musakapatsidwe zimenezi kachenjereni.” Ndipo munthu yemwe Allah akufuna kuti amuyese mayeso sungathe kumpezera chilichonse kwa Allah. Iwowo ndiomwe Allah sadafune kuyeretsa mitima yawo. Apeza kuyaluka pa dziko lapansi. Ndipo tsiku lachimaliziro adzapeza chilango chachikulu.
Ndipo takuvumbulutsira buku mwa choonadi, lomwe likuikira umboni mabuku omwe adalipo patsogolo pake, ndi kuwateteza, (monga ponena kuti: “Lamulo ili ndiloona; ili iyayi.”) Choncho weruza pakati pawo ndi zomwe Allah wavumbulutsa, ndipo usatsate zofuna zawo kusiya choona chomwe chakufika. Ndipo m’badwo uliwonse mwa inu tidaupangira shariya (malamulo) yake ndi njira yake. Allah akadafuna, akadakuikani kukhala mpingo umodzi (wotsata chilamulo chofanana). Koma akufuna kukuyesani pa zomwe wakupatsani. Choncho pikisanani pa zinthu zabwino. Inu nonse kobwerera kwanu nkwa Allah. Naye adzakuuzani (nonsenu) mu zomwe mudali kusiyana;
Kodi iwo akufuna chiweruzo cha nthawi yaumbuli (chamasiku aumbuli, Chisilamu chisanadze)? Kodi ndani ali wabwino poweruza kuposa Allah kwa anthu otsimikiza (kuti Allah alipo)?
Uwaona omwe m’mitima mwawo muli matenda (a chinyengo) akuthamangira kwa iwo (Ayuda) uku akuti: “Tikuopa lingatigwere tsoka (ngati Asilamuwa atagwa m’tsoka), koma posachedwapa Allah abweretsa lamulo logonjetsa (midzi), kapena chinthu china chochokera kwa Iye (monga kuwaulula achinyengo zomwe akubisa m’mitima mwawo). Choncho adzasanduka odzinena chifukwa cha zomwe adabisa m’mitima mwawo.
Ndipo amene adakhulupirira nayamba kunena (chitaululika chinyengo cha achinyengowo): “Kodi awa si omwe adali kulumbilira dzina la Allah m’kulumbilira kwawo kwamphamvu kuti iwo ali pamodzi ndi inu?” Zochita zawo zaonongeka. Tero akhala otaika.
Ndipo amene achite Allah ndi Mtumiki Wake, ndi omwe akhulupirira kukhala atetezi ake, (ndithu iwo ndi a chipani cha Allah). Ndithu chipani cha Allah ndicho chopambana.
Nena: “E inu anthu a buku! Kodi mukuona cholakwika kwa ife kaamba kakuti takhulupirira Allah ndi zomwe zavumbulutsidwa kwa ife ndi zomwenso zidavumbulutsidwa kale? Ndithudi, ambiri mwa inu ndi opandukira chilamulo (cha Allah).”
Ndipo (achinyengo) akakudzerani, akunena: “Takhulupirira,” pamene alowa kwa inu ali osakhulupirira ndipo atulukanso ali osakhulupirira. Koma Allah Ngodziwa kwambiri zomwe akhala akubisa.
Ndipo Ayuda adati: “Dzanja la Allah lafumbatika (sitikupeza chuma ngati kale). (Koma sichoncho); manja awo ndiwo afumbatika (posachita zabwino ndi kuchenjelera anthu). Ndipo atembeleredwa chifukwa cha zomwe anena. Koma manja ake (Allah) ngotambasuka. Amapatsa mmene wafunira. Ndithudi, zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako, ziwaonjezera ambiri a iwo (Ayuda) kulumpha malire ndi kusakhulupirira. Ndipo taika chidani ndi kusakondana pakati pawo mpaka tsiku la chimariziro. Nthawi iliyonse akayatsa moto wa nkhondo, Allah amauzimitsa. Ndipo amayesetsa kudzetsa chisokonezo pa dziko, (koma Allah sawathandiza). Ndipo Allah sakonda owononga.
Ndithudi, amene akhulupirira ndi amene ali m’chipembedzo cha Chiyuda, ndi Asabayi, ndi Akhrisitu, - amene akhulupirire Allah ndi tsiku lachimaliziro, (monga momwe akulangizira Mtumiki Muhammad {s.a.w}) nachita zabwino, - palibe mantha kwa iwo ndiponso sadzadandaula.
Ndithudi am’kana Allah amene anena kuti, Mulungu ndiye Isa (Yesu) mwana wa Mariya.” Pomwe Mesiya adati: “Inu ana a Israyeli! Pembedzani Allah Yemwe ndi Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu.” Ndithudi, amene aphatikize Allah ndi chinthu china, ndithudi Allah waletsa kwa iye kukalowa ku Munda wamtendere, ndipo malo ake ndi ku Moto. Ndipo anthu ochita zoipa sadzakhala ndi athandizi.
Mesiya mwana wa Mariya sali chilichonse koma ndi Mtumiki wa Allah chabe. Ndithudi, atumiki ambiri adapita kale patsogolo pake. Nayenso mayi wake ndi mkazi wachoonadi, onse awiri adali kudya chakudya, (ndipo chotsatira chake amapita kokadzithandiza. Nanga ndi milungu yotani yopita kukadzithandiza?) Taona momwe tikufotokozera kwa iwo zizindikiro. Taonanso mmene akutembenuziridwa (kusiya choonadi).
Uwaona ambiri a iwo akupalana ubwenzi ndi omwe sadakhulupirire Allah, (opembedza mafano ndi cholinga chomenya nkhondo chipembedzo cha Chisilamu). Nzoipa kwambiri zomwe adadzitsogozera okha. Tero Allah adawakwiira ndipo m’masautso adzakhalamo nthawi yaitali.
(Atadzudzulidwa polowa m’Chisilamu iwo adati): “Chifukwa ninji tisamkhulupirire Allah ndi choonadi chomwe chatifika, pomwe tikuyembekezera Mbuye wathu kukatilowetsa (ku Munda wamtendere) pamodzi ndi anthu abwino?”
Choncho Allah adzawalipira, pa zomwe adanena, Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake mitsinje ikuyenda. M’menemo adzakhalamo nthawi yaitali. Imeneyo ndiyo mphoto ya ochita zabwino.
E inu amene mwakhulupirira! Ndithu Allah akuyesani ndi nyama zina zozichita ulenje, zomwe manja anu ndi mikondo yanu ingazifikire, kuti Allah amuwonetsere poyera amene akumuopa mwanseri. Ndipo amene alumphe malire (posaka nyamayo ndi kupha) pambuyo pa zomwe mwauzidwazo, adzapeza chilango chopweteka.
E inu amene mwakhulupirira! Musaphe nyama ya mtchire pomwe inu muli m’mapemphero a Hajj kapena Umrah. Ndipo mwa inu amene angaphe mwadala nyama ya mtchireyo, dipo (lake likhale kuzinga) yofanana ndi yomwe waphayo, mu mtundu wa nyama zowetedwa, (monga mmene) angaweruzire olungama awiri a mwa inu, kukhala nsembe yoperekedwa ku Ka’aba (kuti ikazingidwe kumeneko ndi kuwagawira osauka); kapena alipe dipo la chakudya kudyetsa masikini; kapena m’malo mwake asale kuti alawe kupweteka kwa chinthu chakecho. Ndipo Allah afafaniza zomwe zidapita kale. Koma amene achitenso, Allah amukhaulitsa ndi chilango chochokera kwa Iye. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Wokhaulitsa koopsa
Nkololezedwa kwa inu kusaka nyama za m’nyanja ndi chakudya chake (chomwe chapezeka m’nyanjamo chitafa chokha). Chimenecho ndi kamba wanu (inu amene simuli pa ulendo) ndiponso a pa ulendo. Kwaletsedwa kwa inu kusaka za pamtunda pomwe muli m’mapemphero a Hajj kapena Umrah. Opani Allah Yemwe kwa Iye mudzasonkhanitsidwa.
Allah wapanga Ka’aba kukhala nyumba yopatulika, ndikukhala pamalo popezera zosowa za anthu. Ndipo adapanganso miyezi (inayi) yopatulika, ndi kupereka nyama zansembe ku Makka zovekedwa makoza monga zisonyezo (kusonyeza kuti zikupita ku Makka). Zonsezi nkuti mudziwe kuti Allah akudziwa za kumwamba ndi pansi, ndikuti Allah Ngodziwa chilichonse.
Dziwani kuti ndithudi, Allah Ngolanga mwaukali. Ndikutinso Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha.
Pa mtumiki palibe china koma kufikitsa chabe (uthenga). Ndipo Allah akudziwa zimene mukuzionetsera poyera ndi zimene mukuzibisa.
Anthu amene adalipo kale inu musanadze, adazifunsapo zotere. Ndipo pachifukwa chimenecho adasanduka osakhulupirira.
Allah sadaike (kuletsedwa kwamtundu uliwonse) pa nyama yotchedwa Bahira[166], ngakhale Saiba[167], ngakhale Wasila[168], ngakhalenso Hami[169]. Koma amene sadakhulupirire akumpekera Allah bodza. Ndipo ambiri a iwo sagwiritsa ntchito nzeru zawo.
Ndipo akauzidwa: “Tadzani kuchilamulo cha zomwe Allah wavumbulutsa ndi (zomwe akunena) Mtumiki.” Akunena: “Tikukwaniritsidwa ndi zomwe tidawapeza nazo makolo athu.” Kodi ngakhale kuti makolo awowo sadali kudziwa chinthu chilichonse ndipo sadali oongoka, (awatsatirabe)?
E inu amene mwakhulupirira! Pamene chamfikira mmodzi wa inu chisonyezo cha imfa, ndipo akufuna kusiya chilawo (wasiya) funani mboni ponena mawuwo. Aikire umboni awiri olungama mwa inu (Asilamu) kapena apadera ngati muli pa ulendo, ndipo zisonyezo za imfa zitaonekera. Ngati mutazikaikira zitsekerezeni (kuti zisachoke) mboni ziwiri pambuyo pa Swala (yomwe amasonkhana anthu ambiri), ndipo zilumbilire m’dzina la Allah kunena (kuti): “Sitikusinthanitsa malumbirowa ndi china chake ngakhale chitakhala chothandiza kwa ife kapena mmodzi mwa abale athu. Sitikubisa umboni umene Allah watilamula kuti tiupereke moona. Ife ngati titabisa umboni (kapena kuyankhula chonama), ndithudi tikhala mwa anthu ochimwa.”
Koma ngati kutaoneka kuti mboni ziwiri zija zanama pa umboni wawo, kapena zabisa chinthu, apo awiri achibale a wakufayo aimiire m’malo mwa mboni ziwirizo, (pambuyo pa Swala kuti aulule za bodza lawo). Choncho alumbilire m’dzina la Allah kuti: “Ndithu kulumbira kwathu nkoyenera kuvomerezedwa kuposa kulumbira kwawo; ndipo sitinapyole malire (mukulumbira kwathu). Ndipo sitikuzipekera mbonizo bodza. Ndithudi, ngati ife titachita zotere, ndiye kuti tikhala mwa ochita zoipa, (oyenera kulandira chilango cha Allah).”
Chilamulochi ndi njira yapafupi kuti mboni zikwaniritse umboni wawo mnjira yoyenera, (ndikuti zisamalire kulumbira Allah kwawo); kapena kuopa kuyaluka bodza lawo likaonekera poyera, pambuyo polumbira enawo (izi zili polumbira amlowa mmalo pokana umboni wawo). Ndipo opani Allah (mkulumbira kwanu ndi kukhulupirika kwanu), ndipo mverani malamulo Ake. Allah satsogolera anthu opandukira chilamulo Chake.
(Kumbukirani) tsiku lomwe Allah adzasonkhanitsa, atumiki ndikuwafunsa kuti: “Kodi mudayankhidwa chiyani?” Iwo adzati: “Ife sitidziwa. Ndithudi, Inuyo ndiye Wodziwa zamseri.”
Kumbukiraninso pamene Allah adzati: “Iwe Isa (Yesu) mwana wa Mariya! Kumbuka chisomo Changa pa iwe ndi pa mayi wako, pamene ndinakuthandiza ndi mzimu woyera (Gabriel), (kotero kuti) udalankhula kwa anthu (mawu omveka) pamene udali mchikuta ndiponso pamene udali wamkulu. Ndipo (kumbuka) pamene ndidakuphunzitsa kulemba, nzeru; (ndinakuzindikiritsanso buku la) Taurat ndi Injili. (Kumbukanso) pamene udaumba dongo chithunzi chambalame mwa lamulo Langa. Utatero udauziramo ndipo zidasanduka mbalame mwa lamulo Langa. Ndipamene udali kuchiza akhungu ndi achinawa, mwa lamulo Langa. Ndipamene unkawatulutsa (m’manda) ena mwa akufa mwa lamulo Langa. Ndipamene ndinawatsekereza ana a Israyeli kwa iwe (kuti asakuzunze) pamene udawadzera ndi zisonyezo zooneka, ndipo aja mwa iwo omwe sadakhulupirire, adati: “Ichi sichina, koma ndi matsenga owonekera.”
Ndipo (kumbukira) pamene ndidawaululira ophunzira ako kuti: “Ndikhulupirireni Ine ndi Mtumiki Wanga (uyu Isa {Yesu}).” Iwo adati: “Takhulupirira; ndipo khalani mboni kuti ife ndife Asilamu (ogonjera mwa Inu).”
(Kumbukira) pamene ophunzira ako adati: “E iwe Isa (Yesu) mwana wa Mariya: Kodi Mbuye wako angathe kutitsitsira chakudya kuchokera kumwamba?” (Isa {Yesu}) adati: “Opani Allah, ngati inu mulidi okhulupirira. (Musamangopempha zozizwitsa).”
Isa (Yesu) mwana wa Mariya adati: “Inu Allah Mbuye wathu! Titsitsireni chakudya kuchokera kumwamba kuti chikhale chikondwelero cha oyambilira ndi omalizira mwa ife, komanso chikhale chisonyezo chochokera kwa Inu; choncho tipatseni ndithu inu ndinu Abwino popatsa kuposa opatsa.”
Ndipo (kumbukirani) pamene Allah adzanena: “Iwe Isa (Yesu) mwana wa Mariya: Kodi iwe udauza anthu kuti: ‘Ndiyeseni ine ndi mayi wanga monga milungu iwiri m’malo mwa Allah?” (Mneneri Isa {Yesu}) adzaati: “Ulemelero ukhale pa Inu. Sikoyenera kwa ine kunena zomwe sizili zoyenera (kwa ine mawu amenewa ngabodza). Ngati ndikadanena, ndiye kuti mukadadziwa. Inu mukudziwa zomwe zili mu mtima mwanga, pomwe ine sindidziwa zomwe zili mwa Inu. Ndithudi, Inu ndinu Wodziwa zamseri.”
Share