Surah Al-Hujurat ( The Dwellings )

Surah Al-Hujurat ( The Dwellings ) - Chewa Aya count 18

E inu amene mwakhulupirira! Musamatsogoze (kulamula chinthu chapachipembedzo kapena cham’dziko) patsogolo pa (mawu a) Allah ndi Mthenga Wake. Ndipo muopeni Allah, ndithu Allah Ngwakumva, Ngodziwa.
Ndipo iwo akadapirira ndi kuyembekeza (kuti) mpaka utuluke ndi kudza kwa iwo, zikadakhala zabwino kwa iwo; koma Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha.
E inu amene mwakhulupirira! Ngati atakudzerani munthu wosakhulupirika ndi nkhani (iliyonse, musamuvomereze); ifufuzeni (kaye) kuopa kuti mungachitire anthu (mtopola) mwa umbuli, ndikuti mungazanong’oneze bondo pa zomwe mwachita.
Ndipo dziwani kuti ndithu mwa inu muli Mtumiki wa Allah, (mumvereni iye zimene akukuuzani) kukadakhala kuti iye akukumverani pa zinthu zambiri (zimene mukumuuza), mukadavutika. Koma Allah wachichita chikhulupiliro kukhala chokondeka kwa inu ndipo wachikometsa m’mitima mwanu ndipo wakuchitani kuti mukude kusakhulupirira ndi ufasiki (kutuluka m’malamulo a Allah) ndi kunyoza (Allah.) Iwowo ndiwo oongoka.
(Chifukwa cha) ubwino wochokera kwa Allah ndi mtendere (Wake, mwapeza zimenezi); ndipo Allah Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya.
Ndithu okhulupirira onse ndi pachibale choncho yanjanitsani pakati pa abale anu; (musanyozere lamulo la kuyanjanitsa) ndipo muopeni Allah kuti akuchitireni chifundo.
E inu amene mwakhulupirira! Amuna asanyoze amuna anzawo; mwina (onyozedwa) nkukhala abwino (kwa Allah) kuposa iwo (onyoza). Nawonso akazi asanyoze akazi anzawo; mwina onyozedwa nkukhala abwino (kwa Allah) kuposa iwo (onyoza). Ndipo musatukwanizane pokumbana mitundu kapena kuitanana ndi maina oipa. Taonani kuipa kumuyitanira munthu ndi dzina loti fasiki (wotuluka m’malamulo a Allah) atakhulupirira kale; ndipo amene salapa (ku zimenezi), iwo ndiwo (ochimwa) odzichitira okha chinyengo.
E inu amene mwakhulupirira! Dzitalikitseni kuwaganizira kwambiri zoipa (anthu abwino). Ndithu kuganizira (anthu) maganizo (oipa) nditchimo. Ndipo musafufuzefufuze (nkhani za anthu) ndiponso musajedane pakati panu. Kodi mmodzi wa inu angakonde kudya minofu ya m’bale wake wakufa? Simungakonde zimenezo ndipo muopeni Allah. Ndithu Allah Ngolandira kulapa, Ngwachisoni chosatha.
E inu anthu! Tidakulengani (nonse) kuchokera kwa mwamuna (m’modzi; Adam) ndi mkazi (m’modzi; Hawa), ndipo tidakuchitani kukhala a mitundu ndi mafuko (osiyanasiyana) kuti m’dziwane (basi). Ndithu wolemekezeka kwambiri mwa inu kwa Allah, ndi yemwe ali woopa. Ndithu Allah Ngodziwa, ndipo Ngodziwa kwambiri nkhani zonse.
Arabu akumidzi adanena (kuti): “Takhulupirira.” Nena, Simudakhulupirire (kwenikweni); koma nenani (kuti): “Tagonjera (Allah).” Ndipo mpaka pano chikhulupiliro sichidalowe m’mitima mwanu (ndi kukhazikika bwinobwino). Koma ngati mumvera Allah ndi Mtumiki Wake, sakuchepetserani chilichonse m’zochita zanu. Ndithu Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachifundo chambiri.
Akukukumba iwe chifukwa cha kulowa kwawo m’Chisilamu (ngati kuti akuchitira ufulu). Nena: “Kulowa kwanu m’Chisilamu musakuyese kuti mwandichitira ine ubwino, koma Allah ndiAmene wakuchitirani ubwino pokuongolerani ku chikhulupiliro, ngati muli owona.”
Share