Surah Al-Fath ( The Victory )

Surah Al-Fath ( The Victory ) - Chewa Aya count 29

Ndithu takugonjetsera (iwe Mtumiki{s.a.w}mzinda wa Makka) kugonjetsa kwakukulu koonekera poyera.[346]
Iye ndiamene adatsitsa chikhazikiko (kudekha) m’mitima mwa okhulupirira kuti awonjezera chikhulupiliro pachikhulupiro chawo. Makamu ankhondo akumwamba ndi pansi, nga Allah, (monga angelo, ziwanda, nyama ziphaliwali, mphepo yamkuntho ndi zivomerezi ndi zina zotero); ndipo Allah Ngodziwa chilichonse, ndiponso Wanzeru zakuya.
Ndithu takutumiza kuti ukhale mboni ndi wolengeza nkhani zabwino ndiponso mchenjezi.
Ncholinga choti mumkhulupirire Allah ndi Mtumiki Wake, ndi kuti mumtukule ndi kumulemekeza (Mtumiki) ndi kutinso mumtamande (Allah) m’mawa ndi madzulo.
Adzanena kwa iwe Arabu am’midzi otsala (ku nkhondo, amene adalibe zifukwa zomveka m’kutsala kwawo): “Chuma ndi ana athu zidatitangwanitsa; choncho tipemphereni chikhululuko.” Akunena ndi malirime awo (mawu) omwe m’mitima mwawo mulibe. Nena: “Kodi ndani angathe kukuthandizani chilichonse kwa Allah ngati atafuna kukupatsani masautso, kapena atafuna kukupatsani zabwino? Koma Allah Akudziwa zonse zimene mukuchita.”
Ndipo ufumu wakumwamba ndi pansi ngwa Allah. Amakhululukira amene wamfuna (ngati atatembenukira kwa Iye) ndi kumlanga amene wamfuna (ngati sanatembenukire kwa Iye). Ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.
Ndithu Allah adawayanja okhulupirira pamene amagwirana nawe (Mtumiki) chanza pansi pa mtengo pomwe amakulonjeza (kuti adzamenya nkhondo mpaka imfa) Allah adadziwa zomwe zidali m’mitima mwawo ndipo adatsitsa pa iwo kukhazikika (ndi kudekha;) ndipo adawalipira kupambana kwapafupi.
Allah wakulonjezani zofunkha zambiri zapankhondo (zomwe) mudzazitenga, ndipo wachita changu kukupatsani izi, (zinazo asanakupatseni). Ndipo watsekereza manja a anthu pa inu (kuti asakumenyeni). Ndi kuti chikhale chisonyezo cha okhulupirira (amene akudza pambuyo panu), ndi kuti akuongolereni kunjira yolunjika.
Iwowo ndiamene sadakhulupirire, ndipo adakutsekerezani kulowa mu Msikiti Wopatulika pomwe nyama zansembe zidangomangika osakafika pamalo pake. Kukadakhala kuti kulibe amuna okhulupirira ndi akazi okhulupirira omwe simudawadziwe kuti mungawaponde potero inu kukanakupezani kudzudzulidwa kuchokera kwa iwo popanda kudziwa, (Allah akadakulolezani kumenyana nawo. Koma wachita izi) kuti Iye amulowetse ku mtendere Wake amene wamfuna. Akadadzipatula, tikadawalanga ndi chilango chowawa amene sadakhulupirire pakati pawo.
Ndithu Allah adamtsimikizira Mtumiki Wake za maloto ake owona: “Ndithu inu mudzalowa mu Msikiti Wopatulika mwamtendere Allah akafuna; mutameta mitu yanu mpala kapena (ena) kuyepula (tsitsi lawo), simudzaopa (nthawi imeneyo); ndipo Allah amadziwa zimene simumazidziwa, ndipo zisanapezeke zimenezo, akupatsani kupambana kumene kuli pafupi.
Muhammad (s.a.w) ndi Mtumiki wa Allah; ndipo amene ali pamodzi ndi iye ngamphamvu kwa osakhulupirira (Allah), ngachifundo chambiri pakati pawo. Uwaona akugwira m’maondo ndi kugwetsa nkhope zawo pansi ncholinga chofuna zabwino za Allah ndi chikondi (Chake). Zizindikiro zawo zili pa nkhope zawo zosonyeza kulambira kwawo. Ili ndi fanizo lawo m’Chipangano chakale, Ndipo fanizo lawo m’Chipangano chatsopano nkuti iwo ali monga mmera womwe watulutsa nthambi zake; kenako (nthambizo) nkuulimbitsa ndi kukhala waukulu ndi kuima bwinobwino ndi tsinde lake, nkuwasangalatsa omwe adaubzala. (Choncho) zotsatira zake, nkuwakwiyitsa osakhulupirira chifukwa cha iwo. Allah walonjeza chikhululuko ndi malipiro aakulu (kwa) amene akhulupirira ndi kuchita zabwino mwa iwo.
Share