Surah Al-Jathiya ( Crouching )

Surah Al-Jathiya ( Crouching ) - Chewa Aya count 37

Chivumbulutso cha buku (ili) chochokera kwa Allah Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya.
Ndithu kuthambo ndi m’nthaka muli zisonyezo (zazikulu zosonyeza kuti Allah alipo) kwa okhulupirira.
Ndiponso mkalengedwe kanu ndi zimene wazifalitsa mmenemo, mu zamoyo ndizisonyezo kwa anthu amene akutsimikiza.
Izi ndi Ayah (ndime) za Allah; tikukuwerengera iwe mwachoonadi. Kodi ndi nkhani yanji adzaikhulupirire atapanda kulabadira nkhani ya Allah ndi Ayah Zake?
Kuonongeka kuli pa aliyense wopeka zinthu, wamachimo ambiri.
Amene akumva Ayah za Allah zikuwerengedwa kwa iye kenako nkumapitiriza (zochita zake zosalungama) uku akudzikweza ngati kuti sadazimve ayazo; muuze nkhani ya chilango chowawa.
Ndipo akadziwa chinthu chochepa chochokera mma Ayah athu, amachichitira chipongwe; amenewa ndi amene adzakhala ndi chilango chosambula.
Jahannam ili (kuwayembekezera) kuseri kwawo; ndipo zimene adachita sizidzawathandiza chilichonse, ngakhale atetezi amene adadzipangira kusiya Allah (sadzawathandiza); ndipo adzapeza chilango chachikulu.
Kenako tidakuika iwe pa malamulo a zinthu za chipembedzo (Chathu). Choncho tsatira malamulo (Athu), ndipo usatsate zilakolako za amene sadziwa (njira yoona).
Ndithu iwo (amene akutsata njira zonama) sangakuthandize chilichonse kwa Allah; ndithu achinyengo ena a iwo amatetezana wina ndi nzake; koma Allah ndi Mtetezi wa oopa (Iye potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa).
Iyi (Qur’an imene yavumbulutsidwa kwa iwe), ndizisonyezo kwa anthu chiongoko ndi chifundo kwa anthu omwe akutsimikiza (kuti lilipo tsiku la chiweruziro).
Kodi wamuona amene wachichita chilakolako chake kukhala mulungu wake wompembedza? Ndipo Allah wamlekelera kuti asokere, kupyolera mkudziwa Kwake; ndipo wamdinda (chidindo) mmakutu mwake ndi mu mtima mwake ndi kumuika chivindikiro mmaso mwake. Choncho ndani angamuongole pambuyo pa Allah? Kodi simukumbukira?
Ndipo (okanira kuuka ku imfa) adanena: “Kulibe (moyo wina) koma moyo wathu womwewu wa padziko lapansi; timafa ndi kukhala ndi moyo; palibe chikutiononga koma nthawi basi.” Koma iwo alibe kudziwa pa zimene akunenazo; akungoganizira chabe.
Ndipo Ayah Zathu zikawerengcdwa kwa iwo zolongosola chilichonse momveka, alibe mtsutso wina koma kunena kuti: “Tibweretsereni makolo Athu (aukitseni akhale ndi moyo) ngati inu muli owona!”
Ndipo udzaliona gulu lililonse litagwada (uku nkhope zili zyoli); gulu lililonse lidzaitanidwa ku kaundula wake (kukamuwerenga): “Lero mulipidwa zimene mudali kuchita!”
Kudzanenedwanso kwa iwowa: “Lero tikuiwalani (pokusiyani mchilango) monga momwe inu mudaiwalira kukumana ndi tsiku lanu ili. Ndipo malo anu ndi ku Moto, ndipo mulibe wokupulumutsani.”
Tero kutamandidwa konse ndi kwa Allah, Mbuye wakumwamba ndi Mbuye wa pa dziko lapansi; Mbuye wazolengedwa.
Share