Surah Ad-Dukhan ( The Smoke )

Surah Ad-Dukhan ( The Smoke ) - Chewa Aya count 59

Ndikulumbilira buku lofotokoza momveka.
Mu (usiku) umenewu chinthu chilichonse chanzeru chimaweruzidwa ndi kulongosoledwa.
Mwa chilamulo chochokera kwa Ife. Ndithu Ife ndife otumiza atumiki (kuti achenjeze anthu).
(Chifukwa cha) chifundo chochokera kwa Mbuye wako. Ndithu Iye Ngwakumva zonse, Wodziwa kwabasi.
Koma iwo (okanira) ali mchikaiko akungosewera, (potsatira zilakolako zawo zoipa).
Udzawaphimba anthu onse (ndipo adzakhala akunena:) “Ichi ndi chilango chowawa.
(Kodi lero) kukumbukira kuwapindulira chiyani iwo? Chikhalirecho mtumiki wolongosola chilichonse adawadzera.
Koma sadamlabadire uku akumnena kuti: “Waphunzitsidwa (ndi anthu), ndiponso wopenga.”
(Kumbuka, iwe Mtumiki), tsiku limene tidzawalanga chilango chachikulu; ndithu Ife ndife olanga.
“Ndipo Ine ndadzitchinjiriza ndi Mbuye Wanga ndiponso Mbuye wanu (ku chiwembu chofuna kundipha) pondigenda (ndi miyala).”
“Ndipo ngati simundikhulupirira, ndipatukeni (musandivutitse).”
“(Koma adamchitira mtopola). Ndipo iye adaitana Mbuye wake kuti: “Awa ndithu ndi anthu oipa.”
(Allah adamuuza kuti): “Pita ndi akapolo Anga usiku; ndithu inu mulondoledwa.”
“Ndipo isiye nyanja ili momwemo, zii. ndithu iwo ndikhamu (lankhondo) limene limizidwa.”
Kodi ndi minda ingati ndi akasupe zomwe adazisiya atamizidwa!
Ndi mtendere (waukulu) umene adali kusangalala nawo mmenemo.
Ndipo ndithu tidawasankha (Ayuda nthawi imeneyo) pa mitundu ina m’kudziwa Kwathu,
Ndipo tidawapatsa zisonyezo (kupyolera m’dzanja la Mûsa) momwe mudali mayeso oonekera poyera kwa iwo.
“Choncho tibweretsereni makolo athu (amene adafa), ngati mukunena zoona (kuti kuli kuuka).”
Kodi iwo ndi abwino (ndi kupambana pa nyonga), kapena anthu a Tubba (mafumu a kudziko la Yemen) ndi amene adalipo kale iwo asadadze? Tidawaononga. Ndithu iwo adali oipa.
Ndithu tsiku lachiweruziro ndiyo nthawi yawo onse (imene alonjezedwa).
Tsiku limene m’bale sadzathandiza m’bale wake pa chilichonse (ku chilango cha Allah), ngakhale iwo sadzapulumutsidwa.
Kupatula amene Allah adzawachitira chifundo. Ndithu Iye Ngwamphamvu zoposa, Ngwachisoni chosatha.
(Kutentha kwake) ngati mtovu wosungunulidwa, (wotentha kwambiri;) udzakhala ukuwira mmimba.
Monga kuwira kwa madzi otentha kwambiri.
(Kudzanenedwa): “Mgwireni; mkokereni (ndi kumponya) pakatikati pa Jahena!”
(Adzauzidwa mwachipongwe): “Lawa! Ndithu iwe ndiwe wamphamvu zambiri, wolemekezeka, (monga momwe udali kudzitamira muja).”
Adzavala (nsalu) za silika wopyapyala ndi silika wokhuthala uku atayang’anizana (nkhope).
Umo ndi mmene zidzakhalire; ndipo tidzawakwatitsa ndi akazi okongola amaso aakulu.
Mmenemo adzakhala akuitanitsa mtundu uliwonse wa zipatso, mwamtendere;
Choncho yembekeza; iwonso akuyembekezera, (kodi ndani chimtsikire chilango pakati panu).
Share