Surah Ash-Shura (Consultation ) - Aya 22
Surah Ash-Shura (Consultation ) - Chewa - Aya 22 Aya count 53
تَرَى ٱلظَّٰلِمِينَ مُشْفِقِينَ مِمَّا كَسَبُوا۟ وَهُوَ وَاقِعٌۢ بِهِمْ ۗ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ وَعَمِلُوا۟ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فِى رَوْضَاتِ ٱلْجَنَّاتِ ۖ لَهُم مَّا يَشَآءُونَ عِندَ رَبِّهِمْ ۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلْفَضْلُ ٱلْكَبِيرُ ﴿٢٢﴾
Udzawaona (tsiku la Qiyâma) amene adadzichitira okha zoipa (popembedza mafano) akuopa chifukwa cha (zoipa) zomwe adachita, ndipo (chilangocho) chidzawapezabe. Koma amene adakhulupirira ndi kuchita zabwino (udzawaona akusangalala) m’Madimba abwino a ku Minda ya mtendere. Iwo akapeza chilichonse chimene akafune kwa Mbuye wawo. Umenewo ndiwo ulemelero wawukulu.