Surah Ash-Shura (Consultation ) - Aya 15
Surah Ash-Shura (Consultation ) - Chewa - Aya 15 Aya count 53
فَلِذَٰلِكَ فَٱدْعُ ۖ وَٱسْتَقِمْ كَمَآ أُمِرْتَ ۖ وَلَا تَتَّبِعْ أَهْوَآءَهُمْ ۖ وَقُلْ ءَامَنتُ بِمَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ مِن كِتَٰبٍۢ ۖ وَأُمِرْتُ لِأَعْدِلَ بَيْنَكُمُ ۖ ٱللَّهُ رَبُّنَا وَرَبُّكُمْ ۖ لَنَآ أَعْمَٰلُنَا وَلَكُمْ أَعْمَٰلُكُمْ ۖ لَا حُجَّةَ بَيْنَنَا وَبَيْنَكُمُ ۖ ٱللَّهُ يَجْمَعُ بَيْنَنَا ۖ وَإِلَيْهِ ٱلْمَصِيرُ ﴿١٥﴾
(Chifukwa cha umodzi wa zipembedzo ndikuti pasakhale kugawikana pa chipembedzo) choncho aitanire (ku chipembedzo chimodzi); ndipo lungama (poitanapo) monga momwe walamulidwira. Ndipo usatsatire zofuna zawo. Ndipo nena: “Ndakhulupirira mmabuku onse omwe adawavumbulutsa Allah; ndipo ndalamulidwa kuchita chilungamo pakati panu. Allah ndiye Mbuye wathu ndiponso Mbuye wanu; ife tili ndi ntchito zathu (zomwe tidzalipidwa nazo); inunso muli ndi ntchito zanu (zomwe mudzalipidwa nazo). Palibe kukangana pakati pa ife ndi inu (chifukwa chakuonekera poyera choona). Allah adzatisonkhanitsa (kuti atiweruze); kwa Iye yekha ndiko kobwerera.