Surah Ghafir ( The Forgiver God )

Surah Ghafir ( The Forgiver God ) - Chewa Aya count 85

Kuvumbulutsidwa kwa buku (ili) kwachokera kwa Allah Wamphamvu zoposa, Wodziwa kwambiri.
Wokhululuka machimo, Wolandira kulapa (kwa yemwe walapa), Wolanga mwaukali (kwa yemwe wapitiriza kunyoza Allah), Mwini kupereka mtendere. Palibe wopembedzedwa mwa choona koma Iye; kobwerera nkwa Iye.
Sangatsutsane pa zisonyezo za Allah kupatula amene akanira. Choncho kusakunyenge kuyendayenda kwawo pa dziko (kunka nachita malonda ndi kupeza phindu lalikulu ndi malondawo popanda chovuta; posachedwa tiwalanga).
Iwo kulibe, anthu a Nuh adakaniranso pamodzi ndi makamu a anthu omwe adali kuda aneneri, m’badwo wa Nuh utatha; ndipo m’badwo uliwonse udaikira mtima kuchita choipa pa mneneri wawo kuti am’gwire (ndi kumupha). Adali kutsutsana poteteza chachabe kuti ndi uwo (mtsutso wawowo) achotse choona. Ndipo ndidawaononga kotheratu. Tayang’ana, chidali bwanji chilango Changa (pa iwo!)
Chonchonso latsimikizika liwu la chilango pa amene akanira (iwe Mtumiki {s.a.w}) chifukwa iwo ndi anthu a ku Moto (kamba kosankhakukanira ndi kusiya kukhulupirira).
Amene akusenza Arsh (Mpando wachifumu) ndi amene ali mmphepete mwake, akulemekeza ndi kutamanda Mbuye wawo, ndiponso akumkhulupirira Iye; ndipo akupemphera chikhululuko amene akhulupirira (ponena kuti): “E Mbuye wathu! Chifundo ndi kudziwa kwanu kwakwanira pa chinthu chilichonse. Khululukirani amene alapa ndi kutsatira njira Yanu; ndipo apewetseni ku chilango cha Jahena!”
“Ndipo apewetseni ku zoipa; tsono amene mudzampewetsa ku zoipa tsiku limenelo, ndiye kuti mwamchitira chifundo. Ndipo kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.”
Ndithu amene akanira adzaitanidwa (ndi kuuzidwa kuti): “Mkwiyo wa Allah pa inu udali waukulu kuposa mkwiyo wanu pa mitima yanu (yomwe yakulowetsani ku chilango) pamene mudali kuitanidwa ku chikhulupiliro, (ku Chisilamu); ndipo mudali kukanira.”
Adzanena: “E Mbuye wathu! Mudatipatsa imfa kawiri; (imfa yoyamba tisanabadwe, ndipo imfa ya chiwiri pa dziko). Ndipo mudatipatsa moyo kawiri; (moyo woyamba wa pa dziko lapansi, ndipo moyo wachiwiri wakuuka kwa akufa). Choncho tavomereza machimo athu. Kodi pali njira yotulukira (ku chilango kuno)?”
Iye ndi Yemwe akukuonetsani zisonyezo Zake (zosonyeza mphamvu Yake yoposa), ndipo akukutsitsirani madzi kumwamba chifukwa cha inu kuti abweretse zokupatsani moyo (monga chakudya ndi zina). Koma palibe amene akukumbukira kwenikweni kupatula amene watembenukira (kwa Allah).
Choncho mpempheni Allah pomuyeretsera mapemphero Ake ngakhale (kumuyeretsera kwanu kwa mapempheroko) kuwaipire okanira.
Iye Ngotukuka ulemelero, Mwini Arsh (Mpando wachifumu); amapereka chivumbulutso (Chake) mwa lamulo lake kwa yemwe wamfuna mwa akapolo Ake kuti achenjeze (anthu za) tsiku lokumana (anthu onse).
Tsiku lomwe iwo adzaonekera poyera (kwa Allah). Ndipo palibe chilichonse chidzabisidwa kwa Allah (mzinthu zawo). (Ndipo adzamva kufunsa koopsa ndi yankho loopsa): “Kodi ufumu ngwayani lero? Ngwa Allah, Mmodzi yekha, Wogonjetsa, (woweruza mmene akufunira kwa anthu Ake).”
Mzimu uliwonse lero, ulipidwa zimene udachita; palibe kupondereza lero (pochepetsa mphoto kapena kuonjeza chilango). Ndithu Allah Ngwachangu (pa) chiwerengero Chake.
Achenjeze (iwe Mtumiki {s.a.w}) za tsiku lomwe lili pafupi (Qiyâma), pamene mitima idzakhala ku mmero (chifukwa cha mantha oopsa) atadzadzidwa ndi nkhawa. Wodzichitira chinyengo sazakhala ndi bwenzi ngakhale mpulumutsi womveredwa (powateteza iwo).
Iye (Allah ) akudziwa kuyang’ana kwa maso a chinyengo ndi zimene zifuwa zikubisa (mzobisika zonse).
Ndipo Allah amaweruza mwa chilungamo. Koma omwe akuwapembedza kusiya Allah, saweruza chilichonse (chifukwa cha kufooka ndi kulephera kwawo). Ndithu Allah Yekha ndiye Wakumva, Woona (chilichonse).
Ndipo pamene (Mûsa) adawadzera ndi choona chochokera kwa Ife, (Farawo pamodzi ndi omtsatira) adati: “Iphani ana achimuna a amene akhulupirira naye limodzi; ndipo siyani ana awo achikazi.” Koma ndale za okanira sizakanthu, nzotaika.
Ndipo Mûsa adati (kwa Farawo pa modzi ndi anthu ake): “Ine ndadzitchinjiriza ndi Mbuye wanga amenenso ali Mbuye wanu (ku chiwembu) chochokera kwa aliyense wodzikweza, wosakhulupirira za tsiku la chiwerengero.
Ndipo munthu wokhulupirira, wochokera kubanja la Farawo yemwe adali kubisa chikhulupiliro chake, adawalankhula (anthu ake): “Kodi muphe munthu chifukwa chakuti iye akunena kuti: ‘Mbuye wanga ndi Allah,’ chikhalirecho wakubweretserani zisonyezo zoonekera poyera, zochokera kwa Mbuye wanu? Ndipo ngati ali wabodza pa zomwe akunena ndiye kuti kuipa kwa bodzalo kum’bwerera yekha. Koma ngati ali woona (pazomwe akukulonjezani), ndiye kuti gawo lina la zomwe (chilango) akukulonjezani likupezani; ndithu Allah saongola munthu wopyola malire, wabodza la mkunkhuniza!”
“E inu anthu anga! Ufumu walero ngwanu: mwagonjetsa dziko (la Iguputo). Ndani amene angatipulumutse ku chilango cha Allah ngati chitatidzera?” Farawo adati: “Sindikukupatsani maganizo koma okhawo ndikuwaona (kuti ndi abwino) ndiponso sindikukuwongolerani koma kunjira yoongoka.”
Ndipo munthu wokhulupirira uja adanena: “E inu anthu anga! Ine ndikukuoperani (za tsiku la masautso) monga tsiku la magulu (omwe adaukira aneneri awo).”
“Tsiku limene mudzathawa ndi kutembenuza misana yanu; pomwe simudzakhala ndi mtetezi ku chilango cha Allah; ndipo amene Allah wamulekelera kusokera (chifukwa cha zochita zake zoipa), ndiye kuti sangapeze muongoli.”
Ndithu adakudzerani kale Yûsuf ndi zisonyezo zoonekera poyera (Mûsa asadadze). Koma simudaleke kuzikaikira zimene adadza nazo kwa inu, kufikira pamene adamwalira, mudati: “Allah sadzatumiza mneneri wina pambuyo pake.” Motero Allah amamulekelera kusokera yemwe ali opyola malire poononga, wokaikira kwambiri.
Ndipo uja adakhulupirira adati: “E inu anthu anga! Nditsatireni; ndikuongolerani ku njira yoongoka.”
“E inu anthu anga! Ndithu moyo wa pa dziko lapansi ndichisangalalo (chakutha). Ndithu tsiku lachimaliziro ndiye nyumba yokhazikikamo.”
“Amene akuchita choipa sadzalipidwa chinachake koma chofanana ndi chomwe adachita. Ndipo yemwe akuchita zabwino, mwamuna kapena mkazi, uku iye ali okhulupirira, iwowo adzalowa ku Minda ya mtendere. Adzapatsidwa zopatsidwa mmenemo zopanda chiwerengero.”
“Mukundiitanira kuti ndimkane Allah, ndi kuphatikiza ndi milungu yonama yomwe ine sindikuidziwa, pomwe ine ndikukuitanirani kwa Mwini mphamvu zoposa, Wokhululuka kwambiri?”
“Palibe chikaiko, ndithu zomwe mukundiitanirazo (kuti ndizipembedze) zilibe (kuyankha) pempho lililonse pano pa dziko lapansi ngakhale tsiku lachimaliziro. Ndipo kobwerera kwathu nkwa Allah basi. Ndipo, wopyola malire (a Allah) iwowo ndiwo anthu a ku Moto.”
Choncho Allah adam’teteza ku zoipa zomwe adam’tchera. Ndipo chilango choipa chidawazungulira anthu a Farawo (pamodzi ndi iye mwini.)
Zilango za kumoto zikusonyezedwa kwa iwo mmawa ndi madzulo. Ndipo tsiku lomwe Qiyâma idzafika (kudzanenedwa): “Alowetseni anthu a Farawo ku chilango cha ukali kwambiri (choposa chomwe adalandira mmanda mwawo).”
Awo amene adadzikweza adzati: “Ndithu ife tonse tili mommuno. Ndithu Allah waweruza kale pakati pa akapolo (Ake). (Choncho palibe chilichonse chimene tingaphulepo).”
(Alonda aja) adzati: “Kodi sadakudzereni aneneri anu ndi umboni oonekera poyera?” Iwo adzati: “Inde, (adatidzera. Koma ife tidanyoza).” (Ndipo) adzawauza: “Choncho pemphani nokha. Koma pempho la okanira silili la kanthu, ndi lotaika basi.”
Tsiku limene achinyengo sadzawathandiza madandaulo awo, ndipo matembelero adzakhala pa iwo, ndipo pokhala pawo padzakhala poipa kwambiri.
Choncho pirira, ndithu lonjezo la Allah ndi loona. Ndipo pempha chikhululuko cha machimo ako (ukachimwa), ndipo lemekeza Mbuye wako ndi kumtamanda madzulo ndi m’mawa.
Iyeyo ndiye Allah, Mbuye wanu; Mlengi wa chilichonse palibe wina wopembedzedwa mwa choona, koma Iye. Nanga kodi mukutembenuzidwa chotani (kuchoka ku zoona)!
Allah ndi Amene adakupangirani nthaka kukhala pamalo anu okhalapo, ndi thambo kukhala ngati denga (losagwa); ndipo adakujambulani maonekedwe ndikukongoletsa maonekedwe anu; ndipo adakupatsani zinthu zabwino. Ameneyo ndiye Allah, Mbuye wanu. Choncho walemekezeka Allah, Mbuye wa zolengedwa.”
Iye Ngwamoyo Wamuyaya; palibe wopembedzedwa wina, koma Iye. Choncho mpembedzeni momuyeretsera chipembedzo. (Musapembedze milungu ina mophatikiza ndi Iye). Kuyamikidwa konse nkwa Allah, Mbuye wa zolengedwa.
Iye ndi Amene adakulengani kuchokera ku dothi, kenako kuchokera ku dontho la umuna, kenako kuchokera mmagazi; kenako ndikukutulutsani muli khanda; ndipo kenako (adakusiyani) kuti mufike nthawi yanyonga zanu. Ndipo kenako (adakulekani) kuti mukhale nkhalamba. Ndipo ena a inu amapatsidwa imfa asadaifike (nthawi ya ukalamba) nkuti muifikire nthawi imene yaikidwa; (zoterezi nkuti inu) mukhale ndi nzeru.
Iye ndi Yemwe amapereka moyo ndi kupereka imfa; ndipo akafuna kuchita chinthu ndithu amanena kwa chinthucho: “Chitika,” ndipo chimachitika.
Kenako adzauzidwa: “Ili kuti (milungu) imene mudali kuiphatikiza (ndi Allah),”
“Mmalo mopembedza Allah?” Adzanena: “Yatisowa, koma chiyambire kale sitidali kupembedza chilichonse (kupatula Inu).” Umo ndi momwe Allah akuwalekelera kusokera okanira.
“Izi, (zimene zakupezani ku Moto kuno), nchifukwa chakuti mudali kudzikweza pa dziko mosayenera. Ndiponso chifukwa chakuti mudali kunyada.
Chonco pirira, ndithu lonjezo la Allah ndiloona. Mwina tikusonyeza zina mwa zomwe tawalonjeza, kapena tikupatsa imfa (usadazione. Basi, palibe chikaiko, zichitika chifukwa chakuti onse) adzabwezedwa kwa Ife.
Ndithu tidawatuma atumiki patsogolo pako; ena mwa iwo tidakusimbira (nkhani zawo ndi maina awo). Ena mwa iwo sitidakusimbire. Sikudali kotheka kwa mtumiki aliyense kudzetsa chozizwitsa mwa yekha, koma ndi chifuniro cha Allah. Ndipo lamulo la Allah likadzadza, kudzaweruzidwa mwa choonadi. Ndipo ochita zachabe panthawi imeneyo adzataika; (adzaluza).
Ndipo (Iye) amakuonetsani zisonyezo Zake. Kodi ndi ziti m’zisonyezo za Allah zimene mukuzikana?
Koma pamene atumiki awo adawadzera ndi zisonyezo zoonekera, adakondwera ndi kudziwa komwe adali nako, (ndipo sadalabadire zomwe atumiki adadza nazo). Choncho zidawazinga zimene adali kuzichitira chipongwe.
Koma chikhulupiliro chawo sichidali chowathandiza panthawi imeneyo, pomwe adali atachiona kale chilango Chathu. Ichi ndi chizolowezi cha Allah chomwe chidapita pa akapolo (Ake onse kuti chilango chikadza, kulapa sikuvomerezedwa). Choncho pamenepo, okanira adaluza.
Share