Surah Sad ( The Letter Sad )

Surah Sad ( The Letter Sad ) - Chewa Aya count 88

Sad, ndikulumbira Qur’an (iyi) ya ulaliki (wothandiza).
Kodi ndimibadwo ingati taiwononga patsogolo pawo? Adakuwa kuitana (panthawi imeneyo), koma nthawi yopulumuka idali itatha.
Ndipo anadabwa atawadzera mchenjezi wochokera mwa iwo. Ndipo osakhulupirira adati: “Uyu ndiwamatsenga; ngwabodza lamkunkhuniza!”
Ha! Waichita milungu yambirimbiri ija kuti ikhale Mulungu Mmodzi Yekha? Ndithu ichi nchinthu chodabwitsa.”
Ndipo adanyamuka akuluakulu a mwa iwo nati: “Nyamukani muzikapitiriza kupembedza milungu yanu. Ndithu chinthu ichi (nchoipa); chikulinga ife (kuti tisiyane ndi milungu yathu).”
“Sitidamve zimenezi (zakuti Mulungu Ndimmodzi ngakhale) m’chipembedzo chakale (Chikhrisitu). Ichi sikanthu, koma ndibodza lopeka.”
“Kodi uthengawo (wakuti Mulungu Ndimmodzi) wavumbulutsidwa kwa iye pakati pathu?” Koma iwo akukaika ndi ulaliki Wanga. Koma sadalawebe chilango Changa.
Kodi iwo ali nazo nkhokwe za chifundo cha Mbuye wako, Wamphamvu zoposa, Wopatsa mochuluka?
Kapena ufumu wa kumwamba ndi pansi ndi zapakati pake, ngwawo. Ngati zili choncho atakwera makwelero (kuti akafike pamalo poti akalamulire zimene akufuna, ngati angathe kutero).
Awa (Aquraish kuonjezera pa kudzitama kwawo), nkagulu kochepa ndi kofooka. Kagonjetsedwa monga makamu ankhondo (omwe adagonjetsedwa kale omwe amatsutsana ndi aneneri akale).
Patsogolo pawo, anthu a Nuh, Âdi ndi Farawo, mwini nyumba zitalizitali (Pyramid), adatsutsa (aneneri awo).
Onsewa adatsutsa atumiki; basi chilango Changa chidatsimikizika (pa iwo).
Ndipo awa (Aquraish), sayembekeza china koma mkuwe umodzi wosabwereza. (Ndipo ukadzachitika, onse adzafa).
Ndipo akunena (mwachipongwe): “E Mbuye wathu! Tipatsirenitu gawo la chilango chathu lisanafike tsiku lachiwerengero.”
Pirira (iwe Mtumiki) ku zimene akunena (kwa iwe), ndipo kumbuka kapolo wathu Daud, wamphamvu (pa chipembedzo ndi za m’dziko lapansi). Ndithu iye ngotembenukira kwa Allah kwambiri.
Ndipo tidaulimbikitsa ufumu wake ndi kumpatsa uneneri ndi kuyankhula kwa luntha (kosiyanitsira choona ndi chonama).
Kodi yakufika nkhani ya okangana pamene adakwera chipupa mpaka kuchipinda (cha Daud chochitira mapemphero)?
“Ndithu uyu m’bale wanga ali ndi nkhosa makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi (99), pomwe ine ndili ndi imodzi.” Ndipo akuti: “Ndipatse nkhosa imodziyo kuti ndizikusungira.” Ndipo wandiposa pakuyankhula.
(Daud) adati: “Zoona, wakuchitira zosalungama pokupempha nkhosa yako imodzi kuti aiphatikize ndi nkhosa zake. Ndithu ambiri mwa ophatikizana nawo zinthu, ena amachenjelera ena kupatula amene akhulupirira ndi kumachita zabwino; ndipo iwo ngochepa.” Basi pamenepo Daud adaona kuti tamuyesa mayeso (ndipo sadapambane). Choncho adapempha chikhululuko kwa Mbuye wake; adagwa ndi kulambira ndi kubwerera kwa Mbuye wake.
“E iwe Daud! Ndithu ife takuchita iwe kukhala woyang’anira pa dziko; choncho weruza pakati pa anthuwa mwachilungamo; ndipo usatsatire zilakolako kuopa kuti zingakusokeretse ku njira ya Allah.” Ndithu amene akusokera ku njira ya Allah (potsatira zilakolako zawo), chilango chaukali chili pa iwo chifukwa cha kuiwala kwawo tsiku la chiwerengero.
(Ili), ndibuku lochuluka madalitso lomwe talivumbulutsa kwa iwe kuti (anthu) azame kwambiri pomvetsetsa ndime zake; ndi kuti apeze nalo phunziro eni nzeru.
Ndipo Daud tidampatsa (dalitso lobereka) Sulaiman, amene adali munthu wabwino. Ndithu iye adali wochulukitsa kutembenukira kwa Allah (ndi kudzichepetsa m’chikhalidwe chake chonse).
(Kumbuka) pamene adasonyezedwa kwa iye nthawi yamadzulo akavalo ofatsa akaima; othamanga kwambiri, akayenda.
Ndipo adati: “Ndikukonda zinthu zabwino chifukwa chokumbukira Mbuye wanga,” kufikira pomwe (akavalowo) adabisika kuseri kwa chotsekereza (poikidwa m’makola mwawo pomwe iye amafunitsitsa kumawaonabe).
(Ndipo adati): “Abwezeni kwa ine.” Kenako adayamba kuwasisita m’miyendo ndi m’makosi (mwawo).
Adati: “E Mbuye wanga! Ndikhululukireni ndipo ndipatseni ufumu (umene) sangaupeze aliyense pambuyo panga; ndithu inu ndiwopatsa mochulukitsa.”
Kenako tidaichita mphepo yoomba moleza kuti imgonjere, yomwe imayenda mwachifuniro chake (Sulaiman), paliponse pomwe wafuna.
Ndiponso (tidamgonjetsera) asatana; ena mwa iwo omanga zomangamanga ndi obira m’nyanja zakuya.
Ndi ena (mwa asatana) onjatidwa mmagoli ndi unyolo, (kuti asiye kusokoneza ena).
(Ndipo adauzidwa iye): “Izi (zomwc takudalitsa nazo) ndi zopatsa Zathu; choncho mpatse kapena mmane (amene wamfuna). Popanda kuwerengeredwa.”
Ndithu (Sulaiman) ali nawo ulemelero waukulu woyandikira kwa Ife, ndi mabwelero abwino.
(Tidamuyankha kuitana kwake, ndipo tidamuuza): “Menyetsa miyendo yako (panthaka; patuluka madzi) ozizira osamba ndi kumwa (zikuchokera zomwe uli nazo).”
Ndipo tidamubwezera anthu ake, ndi kumpatsanso ena onga iwo (m’kuchuluka kwawo) powaphatikiza ndi omwe adali nawo; (tidachita zimenezi) chifukwa cha chifundo chochokera kwa Ife ndi kuti chikhale chikumbutso kwa eni nzeru.
“Ndipo gwira m’dzanja lako mtolo wa zikoti; menya ndi mtolowo ndipo usaswe lonjezo.” Ndithu Ife tidampeza ali wopirira. Taonani kukhala bwino kapolo! Ndithu iye ngotembenukira kwambiri kwa Allah.[343]
Kumbukira, (iwe Mtumiki {s.a.w}) akapolo athu Ibrahim, Ishâq ndi Ya’qub, eni mphamvu (pa ntchito yachipembedzo) ndi kuyang’ana kozindikira.
Ndithu Ife tidawasankha powapatsa chikhalidwe chabwino (chomwe) ndi kukumbukira Nyumba yomaliza (nthawi zonse).
Ichi ndichikumbutso (kwa iwe ndi anthu ako). Ndipo ndithu oopa Allah ali ndi mabwelero abwino.
(Azidzakhala m’menemo) uku atatsamira (makama amtengo wapatali, ndipo adzakhala akusangalala) akuitanitsa mmenemo zipatso ndi zakumwa zambiri.
Ndipo (ku Munda wamtenderewo) adzakhala ndi akazi oyang’ana amuna awo okha basi, ofanana misinkhu.
Awa ndimalipiro (a oopa Allah)! Koma opyola malire (ndi kunyoza aneneri awo), ali ndi mabwelero oipa.
(Omwe ndi) Jahannam adzailowa (ndi kupseleramo). Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo!
Awa ndimadzi wotentha kwambiri, ndi mafinya (a anthu a ku Moto). Choncho awalaweko!
Ndi zilango zina zambiri zonga zimenezi zamitundumitundu.
(Kudzanenedwa kwa opyola malire, omwe ndiatsogoleri a opembedza mafano): “Gulu ili lalikulu, lilowa nanu ku Moto; (omwe adali okutsatirani. Ndipo atsogoleri adzati): Siolandiridwa (mwamtendere). Ndithu iwo ngolowa ku Moto.”
(Otsatira adzanena): “Ndithu tembeleroli likuyenera inu, (limene mukutitembelera ife) chifukwa inu ndiamene mudadzetsa chilangochi potinyenga ife (ndi kutiitanira kunjira yopotoka), taonani kuipa malo okhazikikamo (Jahannam)!”
(Otsatira) adzanena: “E Mbuye wathu! Muonjezereni chilango ku Moto pamwamba pa chilango amene watidzetsera chilangochi.”
Ndipo (anthu a ku Moto) adzanena: “Kodi nchifukwa ninji sitikuwaona anthu aja omwe timawawerengera kuti ngoipa (pa dziko lapansi)?
Kodi tidawachitira chipongwe (pa dziko lapansi koma taonani sadalowe nafe ku Moto). Kapena kuti maso athu sakuwaona?”
Nena (kwa iwo): “Ndithu ine ndine mchenjezi (wochenjeza za chilango cha Allah). Palibe wopembedzedwa mwachoonadi, koma Allah Mmodzi Yekha Wopambana.
Mbuye wathambo ndi nthaka, ndi zapakati pake; wamphamvu zoposa; Wokhululuka machimo kwambiri (kwa yemwe walapa ndi kumkhulupirira).”
Nena (kwa iwo iwe Mtumiki {s.a.w}): “Ichi (chimene ndakuchenjezani nachochi) ndinkhani yaikulu.”
“Sindimadziwa chilichonse za akuluakulu a pamwamba (angelo) pamene amakangana (za kulengedwa kwa Adam).”
Palibe china chimene chavumbulutsidwa kwa ine, koma (kuti ndikuuzeni mawu awa oti): “Ine ndine mchenjezi (wanu) woonekera.”
(Akumbutse) pamene Mbuye wako adanena kwa angelo: “Ine ndilenga munthu kuchokera ku dothi, (yemwe ndi Adam).”
(Allah) adati: “E iwe Iblis! Nchiyani chakuletsa kugwa pansi ndi kuchilemekeza chimene ndachilenga ndi manja Anga (popanda kutuma wina)? Kodi wadzikweza kapena uli mmodzi wa odziika pamwamba?”
(Iblis) adanena: “Ine ndine wabwino kuposa iye (Adam); chifukwa ine mudandilenga kuchokera ku Moto, ndipo iye mudamulenga kuchokera kudongo.”
(Allah) adanena (kwa Iblis): “Tuluka m’menemo (m’gulu la angelo apamwamba); ndithu iwe ngopirikitsidwa (ku chifundo cha Allah).”
“Ndipo ndithu matembelero Anga akhala pa iwe kufikira tsiku lamalipiro.”
(Iblis) adati: “E Mbuye wanga! Ndipatseni nthawi kufikira tsiku louka ku imfa.”
(Allah) adati: “Ndithu iwe ndiwe mmodzi wa wopatsidwa nthawi.”
“Kufikira tsiku la nthawi yodziwika (imene yaikidwa).”
(Iblis) adati: “Choncho kupyolera mu ulemelero Wanu ndikulumbira kuti ndiwasokoneza onse.”
“Kupatula akapolo Anu omwe ali osankhidwa (oyeretsedwa) mwa iwo. (Pa iwo ndilibe nyonga zilizonse).”
(Allah) adati: “Ndikulumbira mwachoonadi ndipo ndikunena choona.”
“Ndithudi, ndidzazadzitsa Jahannam ndi ochokera ku mtundu wako ndi omwe adzakutsate mwa iwo (ana a Adam) onse.”
Nena (iwe Mtumiki{s.a.w}, kwa anthu ako): “Sindikukupemphani malipiro pa zimenezi ndiponso ine simmodzi wa odzikakamiza (pa zinthu zosandiyenera).
(Qur’an) sichina koma ndichikumbutso ndi chiphunzitso kwa zolengedwa zonse.
Ndipo posachedwa mudziwa, (inu otsutsa, kuona kwa) nkhani zake.”
Share