Surah Luqman

Surah Luqman - Chewa Aya count 34

Alif-Lâm-Mîm.[310]
(Lomwe ndi) chiongoko ndi chifundo kwa ochita zabwino,
Koma alipo ena mwa anthu amene akusankha nkhani ya bodza (ndi kumaifotokoza kwa anthu) ndi cholinga choti awasokeretse ku njira ya Allah popanda kuzindikira. Ndipo akuichitira zachipongwe (njira ya Allah yi). Iwo adzapeza chilango chowasambula.
Adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Ili nlonjezo la Allah lomwe lili loona. Ndipo Iye Ngwamphamvu, Ngwanzeru zakuya.
Adalenga thambo popanda mizati yomwe mukuiona. Ndipo adaika mapiri m’nthaka kuti isakugwedezeni. Ndipo (Iye) adafalitsa nyama m’menemo zamitundu yosiyanasiyana. Ndipo tidatsitsa madzi kuchokera ku mitambo, choncho tidameretsa m’menemo (m’nthaka) mmera wokongola wamitundu yosiyanasiyana.[311]
Ndipo ndithu tidampatsa Luqmân nzeru (ndipo tidati kwa iye): “Thokoza Allah (pazimene wakupatsa).” Ndipo, amene athokoze, ndithu kuthokozako kumthandiza yekha, ndiponso amene akana (mtendere wa Allah pakusiya kuthokoza), ndithu Allah Ngwachikwanekwane, Ngotamandidwa.
Ndipo (akumbutse) pamene Luqmân adauza mwana wake akumulangiza: “E iwe mwana wanga! Usaphatikize Allah ndi mafano. Ndithu kumuphatikiza (Allah), ndi kuipitsa kwakukulu.”
Ndipo tamulangiza munthu kwa makolo ake (kuwachitira zabwino), mayi wake adatenga pathupi pake mofooka pamwamba pakufooka. (Adamuyamwitsa) ndi kumusiyitsa patapita zaka ziwiri, kuti: “Ndithokoze Ine ndi makolo ako, kwa Ine nkobwerera.” [312]
“E iwe mwana wanga! Ndithu icho (chabwino ndi choipa cha munthu) ngakhale chitakhala cholemera ngati njere ya mpiru ndi kukhala mkati mwa thanthwe kapena m’kati mwa thambo, kapena mkati mwa nthaka, Allah adzachibweretsa (ndi kumulipira amene adachita). Ndithu Allah Ngodziwa zinthu zobisika, (ndiponso) Ngodziwa zinthu zoonekera.”
“Ndipo lingana m’kuyenda kwako (popanda kufulumira kwambiri kapena kuyenda pang’onopang’ono); ndipo tsitsa mawu ako, ndithu mawu oyipitsitsa ndi mawu a bulu.”
Koma amene sadakhulupirire (Allah ndi mtima wake) choncho kusakudandaulitse kusakhulupirira kwake. Kobwerera kwawo nkwa Ife basi. Kumeneko tidzawauza zimene adachita. Ndithu Allah Ngodziwa zonse zam’zifuwa.
Tikuwasangalatsa pang’ono (apo pa dziko lapansi). Kenako tidzawakankhira ku chilango chokhwima.
Ndipo ndithu ngakhale mitengo yonse ili m’nthaka ikadakhala zolembera, ndipo nyanja (nkukhala inki), ndipo pambuyo pake ndikuionjezeranso (madzi ake) ndi nyanja zisanu ndi ziwiri, mawu a Allah sakadatha. Ndithu Allah Ngwamphamvu, Wanzeru zakuya.[314]
Kulengedwa kwanu, ngakhale kuukitsidwa kwanu m’manda sikuli kanthu koma kuli ngati (kulenga kapena kuukitsa kwa) munthu mmodzi. (Palibe chokanika kwa Allah). Ndithu Allah Ngwakumva, Ngopenya chilichonse.
Ndithu kudziwa kwa nthawi (yakutha kwa dziko) kuli ndi Allah (Yekha). Iye ndiamene amavumbitsa mvula (nthawi imene wafuna); ndipo akudziwa zimene zili m’ziberekero. Ndipo aliyense sadziwa chomwe apeze mawa; (chabwino kapena choipa); ndiponso sadziwa aliyense kuti ndi dziko liti adzafera. Ndithu Allah Ngodziwa zedi, Ngozindikira kwambiri.
Share