Surah Al-Ankaboot ( The Spider )

Surah Al-Ankaboot ( The Spider ) - Chewa Aya count 69

Alif-Lâm-Mîm.
Kodi anthu akuganiza kuti adzasiyidwa popanda kuyesedwa ndi masautso pakungonena kuti: “Takhulupirira?” (Iyayi, ayenera kuyesedwa ndithu ndi masautso osiyanasiyana pa matupi pawo ndi pachuma chawo kuti adziwike woona ndi wachiphamaso).
Ndipo ndithu tidawayesa amene adalipo patsogolo pawo. Ndithu Allah awaonetsera poyera amene ali olankhula zoona, ndithu Allah awaonetsera poyera amene ali olankhula zabodza.
Kodi amene akuchita zoipa akuganiza kuti atipambana (kotero kuti sitingawalange)? Ndichiweruzo choipa chimene akuweruzacho.
Amene akuyembekezera kukumana ndi Allah, (agwire ntchito yabwino pamoyo wake kuti akakumane Naye ndi zabwino), pakuti ndithu nthawi ya Allah (tsiku la chimaliziro) ikudza (popanda chikaiko). Ndipo Iye Ngwakumva (zonena za akapolo Ake), Ngodziwa (zachinsinsi chawo).[299]
Ndipo amene akuchita khama (polimbana ndi Akafiri, kapena pogonjetsa mtima wake kuti utsatire malamulo a Allah), ndithu zabwino za khamalo zili pa iye mwini. Ndithu Allah siwosaukira chilichonse kwa zolengedwa Zake.
Ndipo alipo ena mwa anthu omwe akunena: “Takhulupirira mwa Allah.” Koma akavutitsidwa chifukwa cha Allah, amawachita masautso a anthu monga chilango cha Allah, (sapirira; iwowa ndi achinyengo (achiphamaso). Ndipo chikadza chipulumutso chochokera kwa Mbuye wako amanena: “Ndithu ife tidali pamodzi ndi inu.” (Koma chikhalirecho akunena zonama). Kodi Allah sadziwa zomwe zili m’zifuwa za zolengedwa?[301]
Ndipo ndithu Allah awaonetsera poyera amene akhulupirira (moona), ndiponso awaonetsera poyera achiphamaso (achinyengo).
Ndipo amene sadakhulupirire adanena kwa okhulupirira: “Tsatani njira yathu; (musatsate njira ya Muhammad). Ife tidzakusenzerani machimo anu (kuti chilichonse chisakupezeni). Koma sadzasenza chilichonse cha machimo awo, ndithu iwo ngabodza.
Ndipo ndithudi, adzasenza mitolo ya machimo ndi mitolo yina yamachimo (ya omwe adawasokeretsa) poiphatikiza ku mitolo yawo ya machimo. (Nawonso osokezedwa, adzasenzanso mitolo ya machimo chifukwa cha kutsatira kwawo anthu owasokezawo). Ndipo pa tsiku la Qiyâma (chimaliziro,) ndithu adzafunsidwa pa zimene amapeka.
Ndipo ndithu tidamtuma Nuh kwa anthu ake ndipo adakhala nawo zaka chikwi chimodzi kupatulapo zaka makumi asanu. (Koma m’nthawi yonseyi sadatsatire ulaliki wake). Choncho chigumula chidawapeza (ndipo adamira onse), uku ali odzichitira zoipa.[302]
Ndipo (akumbutse nkhani ya) Ibrahim pamene adawauza anthu ake: “Mpembedzeni Allah ndi kumuopa. Zimenezo nzabwino kwa inu ngati mukudziwa (kusiyana kwa chabwino ndi choipa).”
Ndipo ngati mutsutsa, ndithu mibadwo ya omwe adalipo patsogolo panu idatsutsanso. Ndipo kwa Mtumiki kulibe udindo wina koma kufikitsa uthenga woonekera poyera, (womveka bwino).
“Amamlanga yemwe wamfuna ndipo amamchitira chifundo amene wamfuna, ndipo kwa Iye nonse mudzabwezedwa.”
Choncho yankho la anthu ake silidali lina koma adangoti: “Mupheni kapena mtentheni ndi moto.” Koma Allah adampulumutsa ku moto. Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo (zosonyeza mphamvu za Allah) kwa anthu okhulupirira.
Ndipo adanena: “Ndithu inu mwasankha mafano kukhala milungu kusiya Allah, ndipo mukukondana pakati panu m’moyo wa pa dziko; (pokhalirana pamodzi ndi kupitiriza kupembedza mafanowo mwachimvano). Koma tsiku la Qiyâma, mudzakanana wina ndi mnzake, komanso mudzatembelerana wina ndi mnzake, malo anu adzakhala ku Moto, ndipo simudzapeza okupulumutsani.”
Choncho (Mneneri) Luti adamkhulupirira iye. Ndipo (Mneneri Ibrahim) adanena: “Ndithu ine ndikusamukira kwa Mbuye wanga (ku dziko lomwe wandilamulira). Ndithu Iye Ngwamphamvu zoposa Ngwanzeru zakuya.”
Ndipo (akumbutse nkhani ya Mneneri) Luti pamene adawauza anthu ake: “Ndithu inu mukuchita zadama; palibe amene adakutsogolerani kuzichita (zadamazo) mwa zolengedwa.”
(Mneneri Ibrahim) adati: “Koma mmenemo muli Luti.” Iwo adati: “Ife ndife odziwa kwambiri za omwe ali m’menemo; ndithu timpulumutsa iye ndi banja lake kupatula mkazi wake; iye ndi mmodzi wa otsalira (woonongeka).”
Koma adamutsutsa. Ndipo kugwedezeka kwa nthaka kudawachotsa moyo wawo, ndipo kudawachera ali gwadegwade m’nyumba zawo (atafa).
Momwemonso Kaaruni, Farawo ndi Hamana (adaonongedwa). Ndithu adawadzera Mûsa ndi zozizwitsa (zooneka), koma adadzikweza pa dziko. Komatu sadathe kumpambana (Allah pomulepheretsa kuwalanga).
Fanizo la amene adzipangira milungu yabodza kusiya Allah, lili ngati fanizo la kangaude (yemwe) wadzipangira nyumba (kuti imsunge, pomwe nyumbayo siingathe kumsunga m’nyengo yozizira kapena yotentha), ndithu nyumba yomwe ili yofooka kwambiri ndi nyumba ya kangaude, akadakhala akudziwa.[304]
Werenga zimene zavumbulutsidwa kwa iwe (za) m’buku, ndipo pemphera Swala moyenera; ndithu Swala (ikapempheredwa moyenera) imamtchinjiriza (woipempherayo) ku zinthu zauve ndi zoipa. Ndipo kukumbukira Allah, ndi chinthu chachikulu. Ndipo Allah akudziwa zimene mukuchita.
Ndipo umo ndimomwe takuvumbulutsira buku (ili la Qur’an). Choncho amene tidawapatsa buku, (ili lisadadze, monga Taurat ndi Injili), akulikhulupirira; akulikhulupiriranso ena mwa awa (Arabu omwe sitidawapatse buku). Ndipo sangawakane ma Ayah Athu kupatula osakhulupirira.
Ndipo iwe sumawerenga buku lililonse, ili lisanadze; ndipo sudalilembe ndi dzanja lako lakumanja. Zikadatero ndiye kuti anthu achabe akadakaikira.[305]
Ndipo akunena: “Kodi bwanji sizinatsitsidwe kwa iye zozizwitsa kuchokera kwa Mbuye wake?” Nena: “Zozizwitsa zili kwa Allah; ndipo ine ndine mchenjezi woonekera, (ndilibe mphamvu zokudzetserani zozizwitsa koma pokhapo Allah atafuna).”
Tsiku limene chidzawavindikira chilango kuchokera pamwamba pawo ndi pansi pa miyendo yawo; ndipo adzanena: “Lawani (chilango cha) zomwe munkachita.”
E inu akapolo Anga amene mwakhulupirira! Ndithu nthaka Yanga njophanuka; (mukhoza kupita dziko lina ngati m’dziko lanulo simukupeza mwayi wopembedza Allah mokwanira); ndipo Ine ndekha ndipembedzeni.
Ndipo amene akhulupirira ndi kumachita zabwino ndithudi tidzawakhazika m’zipinda za ku Munda wamtendere, momwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje; adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Taonani kukhala bwino malipiro a ochita zabwino!
Ndipo ngati utawafunsa (kuti): “Kodi ndani amene akutsitsa madzi kuchokera ku mitambo ndi kuiukitsa nthaka ndi madziwo pambuyo pakufa kwake?” Ndithu anena: “Ndi Allah.” Nena: “Kuyamikidwa konse nkwa Allah.” Koma ambiri a iwo sazindikira.
Ndipo akakwera m’chombo (ndi kukumana ndi zoopsa), amampempha Allah modzipereka ndikumuyeretsera pempho. Koma akawapulumutsa ndi kuwafikitsa ku ntunda, iwo amayambanso kumuphatikiza ndi mafano.
Ndipo amene akulimbikira m’njira yathu, (polimbana ndi satana, ndi mzimu woipa ndi zilakolako zoipa zam’thupi, ndi cholinga chofuna kukondweretsa Allah) ndithu tiwaongolera ku njira Zathu. Ndipo ndithu Allah ali pamodzi ndi ochita zabwino.
Share