Surah Al-Qasas ( The Stories )

Surah Al-Qasas ( The Stories ) - Chewa Aya count 88

Tâ-Sîn-Mîm.
Izi ndi Ayah (ndime) za m’buku (la Qur’an) lofotokoza (chilichonse chofunika pa Chipembedzo).
Tikukulakatulira (iwe Mtumiki) nkhani za Mûsa ndi Farawo m’njira yoona kwa anthu okhulupirira. (Koma osakhulupirira sangapindule kanthu ndi nkhanizi).
Ndithu Farawo adadzikuza pa dziko, ndipo adawakhazika (anthu a m’dzikolo) m’magulumagulu; gulu lina la mwa iwo adalifooketsa (poliyesa akapolo) ndi kupha ana awo achimuna, ndi kuwasiya a moyo ana awo achikazi. Ndithu iye adali mmodzi wa oononga kwambiri.[297]
Ndipo tidafuna kuwachitira zabwino amene adafooketsedwa m’dziko (la Iguputo), ndi kuwachita kukhala atsogoleri ndi kuwachitanso kukhala amlowa mmalo ( a Baiti Al-Makadasi).[298]
Ndi kuwapatsa mphamvu za pa dziko (kuti azichita mmene angafunire) ndi kuti timuonetse Farawo ndi Hamana ndi magulu awo ankhondo kuchokera kwa iwo (ana a Israel), zomwe amaziwopa (kuti zingawathetsere ufumu wawo).
Ndipo mkazi wa Farawo adati: “(Musamuphe, akhale) chosangalatsa diso langa ndi lako; musamuphe mwina angatithandize, kapena tingam’chite kukhala mwana (wathu.” Adanena izi) iwo asakudziwa (kuti adzakhala m’dani wawo).
Ndipo mu mtima mwa mayi wa Mûsa mudali mopanda kanthu (mudalibe maganizo ena koma maganizo a mwana wake). Padatsala pang’ono kuti aonetse (chinsinsi cha mwanayo ponena kuti adali mwana wake), tikadapanda kulimbitsa mtima wake, kuti akhale mmodzi mwa okhulupirira (lonjezo la Allah).
Ndipo (mayi wa Musayo) adauza mlongo wake (wa Mûsa): “Mtsatire, (komwe madzi akupita naye).” Choncho iye ankamuyang’ana chapatali pomwe iwo samadziwa (za ichi).
Ndipo poyamba tidamuletsa kuti asayamwe mawere a woyamwitsa, (kufikira pomwe mlongo wake) adati: “Kodi ndikusonyezeni eni nyumba omwe angakulelereni ndi kukhala naye momteteza bwino mwanayo?”
Adati: “E Mbuye wanga! Ndithu ndadzichitira zoipa ndekha! Choncho ndikhululukireni!” Tero (Allah) adamkhululukira (chifukwa sadalinge kupha). Ndithu Iye (Allah) Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.
Choncho kudamuchera mu mzindamo (m’mawa mwake) uku ali wodzazidwa ndi mantha akuyembekezera (kuti chiyani chimpeze pa zimene zidachitika); pompo munthu uja adampempha dzulo chithandizo ankamuitana (kuti amthandize kumenyana ndi m’dani wake wina). Mûsa adamuuza: “Ndithudi ndiwe wopotoka owonekera.”
Choncho pamene adafuna kumpanda, yemwe ndi mdani wa awiriwo, (uja wofuna chithandizo kwa Mûsa adaganiza kuti Mûsa afuna kuti ampande iye), ndipo adati: “E iwe Mûsa! Kodi ukufuna kundipha monga momwe udaphera munthu uja dzulo? Iwe sufuna china koma kukhala wodzitukumula (wankhanza) pa dziko, ndipo sukufuna kukhala mmodzi mwa ochita zabwino (oyanjanitsa okangana ndi kukonza zinthu).”
(Farawo zitamfika mphekesera kuti Mûsa wapha munthu pothangata mu Israyeli, adalamula kuti Mûsa paliponse pomwe angapezeke, agwidwe ndi kuphedwa). Choncho munthu adadza akuthamanga kuchokera kumalekezero a m’zindawo. Adati: “E iwe Mûsa! Akuluakulu akukuchitira upo kuti akuphe choncho choka (m’dziko muno). Ndithu ine ndine mmodzi mwa okufunira iwe zabwino.”
Ndipo adachoka mu mzindawo ali woopa uku akuyembekezera (kumpeza choipa kuchokera kwa adani ake). Adati: “E Mbuye wanga! Ndipulumutseni kwa anthu ochita zoipa.”
Ndipo pamene adawafika madzi a ku Madiyan (pomwe anthu kumeneko ankatungapo madzi), adapeza gulu la anthu likumwetsa (ziweto zawo), ndipo pambali (pa gululo) adapeza akazi awiri akuletsa (ziweto zawo kuti zisapite kukamwa ndi ziweto zinazo). (Mûsa) adati: “Kodi mwatani? (Bwanji simukuzimwetsa ziweto zanu?)” Iwo Adati: “Sitingamwetse (ziweto zathu) mpaka abusa atachotsa (ziweto zawo, chifukwa sitingathe kulimbana nawo). Ndipo bambo wathu ndinkhalamba yaikulu kwabasi.”
Choncho (Mûsa) adawamwetsera (ziweto zawo); kenako adapita pamthunzi, ndipo adati: “E Mbuye wanga! Ndithu ine ndiwosaukira chabwino chimene munditsitsire.”
Kenako mmodzi mwa asungwana aja adadza kwa iye uku akuyenda mwa manyazi. (Msungwanayo) adati: “Ndithu tate wanga akukuitana kuti akakupatse malipiro pakutimwetsera (ziweto zathu).” Choncho pamene adamdzera, (mneneri Shuaib) ndikumulongosolera nkhani, adati: “Usaope; wapulumuka kwa anthu oipa.”
Mmodzi wa iwo (asungwana aja) adanena: “E bambo wanga mulembeni ntchito (kuti akhale woweta ziweto m’malo mwa ife). Ndithu amene alibwino kuti mumulembe ntchito ndi yemwe ali wamphamvu wokhulupirika (zonse ziwiri mwa iyeyu zirimo.)
(Shuaib) adati (kwa iye): “Ine ndikufuna kukukwatitsa mmodzi mwa asungwana anga awiriwa, chiongo chake ndikundigwilira ntchito zaka zisanu ndi zitatu; ngati utakwaniritsa zaka khumi ndiye kuti nkufuna kwako. Sindikufuna kukuvutitsa (pokuchulukitsira zaka); undipeza, Allah akafuna, kuti ndine mmodzi wa anthu abwino, (wokwaniritsa lonjezo).”
(Mûsa) adati: “Zimene mwandilonjezazi zili pakati pa ine ndi inu. Nyengo iriyonse imene ndikwaniritse pa ziwirizi (pogwira ntchitoyo, ndiye kuti ndakwaniritsa lonjezo lanu) musandichitire mtopola. Ndipo Allah ndiye Muyang’aniri pa zomwe tikukambazi.”
“Ndipo ponya (pansi) ndodo yakoyo.” Choncho pamene adayiona ikugwedezeka monga kuti iyo ndi njoka, adatembenuka kuthawa ndipo sadachewuke. (Adauzidwa): “E iwe Mûsa! Bwera kuno, usaope. Ndithu iwe ndiwe mmodzi wokhala ndi mtendere.”
Lowetsa dzanja lako m’thumba mwako (palisani la mkanjo wako), lituluka lili loyera, popanda choipa. Ukachita mantha, fumbata dzanja lako chakukhwapa; (ukatero mantha akuchokera). Izi zidzakhala zizindikiro ziwiri zochokera kwa Mbuye wako kwa Farawo ndi nduna zake. Ndithu iwo ndianthu olakwa.”
(Mûsa) adanena (moopa) “E Mbuye wanga! Ine ndidapha munthu mwa iwo, ndipo ndikuopa kuti akandipha.”
“Ndipo m’bale wanga (Haaruni) ndikatswiri pakuyankhula kuposa ine. Mutumizeni pamodzi ndi ine monga mnthandizi, azikandivomereza (pa zimene ndizikanena). Ndithu ine ndikuopa kuti akanditsutsa.”
(Allah) adati: “Tilimbitsa dzanja lako ndi m’bale wakoyo ndipo tikupatsani kupambana, iwo sangafikitse masautso pa inu; chifukwa cha zozizwitsa zathuzo inu awiri ndi amene akutsatireni, ndinu opambana.”
Tidawatsatiziranso matembelero padziko lino lapansi. Ndipo tsiku la chimaliziro iwo adzakhala oyipitsitsa (ndi kuthamangitsidwa ku chifundo cha Allah).
Koma ife tidaumba mibadwo yambiri (pambuyo pa Mneneri Mûsa) kotero kuti zaka zidapitapo zambiri pakati pawo. Ndipo sudakhale nawo anthu a Madiyan ndi kumawawerengera Ayah (ndime) Zathu; koma Ife tidali kutuma (atumiki ndi kuwafotokozera zomwe zidachitika patsogolo ndi pambuyo pawo, monga momwe takutumira iwe ndi kukudziwitsa nkhani zakale ndi zimene zikudza pambuyo).
Ndipo sudali kumbali kwa phiri pamene tidamuitana (Mneneri Mûsa). Koma (kutumidwa kwako) ndimtendere wochokera kwa Mbuye wako kuti uwachenjeze anthu omwe mchenjezi sadawadzere (mnthawi yaitali) iwe usadadze, kuti akumbukire.
Koma choona pamene chidawadzera kuchokera kwa Ife, adati: “Bwanji sadapatsidwe zonga zomwe adapatsidwa Mûsa? (Monga kutembenuza ndodo kukhala njoka, ndi zina zotero).” Kodi kalelo sadazikane zomwe adapatsidwa Mûsa? Nkunena (za Taurati ndi Qur’an): “Ndimatsenga awiri amene akuthandizana.” Ndipo adati: “Ndithu ife tikuwakana onse.”
Nena: “Bwerani nalo buku lochokera kwa Allah lomwe lili ndi chiongoko chabwino kuposa awiriwa (Taurati ya Mneneri Mûsa, ndi iyi Qur’an), kuti ndilitsate ngati inu mukunena zoona.”
Iwo adzapatsidwa malipiro awo kawiri (chifukwa chotsatira Mneneri Mûsa Ndi Mneneri Isa (Yesu), kale; ndipo tsopano ndikumtsatira Mneneri Muhammad{s.a.w}) nchifukwa chakuti adapirira; amachotsa choipa (pochita) chabwino, ndipo m’zimene tawapatsa akupereka chopereka (Sadaka).
Ndipo akunena (akafiri a m’ Makka, kuuza Mtumiki): “Ngati titsatira chiongoko (ichi chimene wadza nacho) pamodzi ndi iwe, tifwambidwa m’dziko lathu (potimenya nkhondo mafuko ena a Arabu).” Kodi sitidawakhazike pamalo opatulika ndi pa mtendere pomwe zipatso za mitundumitundu zikudza pamenepo mwaulere (monga rizq) zochokera kwa Ife? Koma ambiri a iwo sadziwa.
Kodi ndimidzi ingati imene tidaiononga yomwe inkanyadira za moyo wawo (wosavutika ndi wodya bwino)! Umo m’malo mwawo simudakhalidwebe pambuyo pawo koma mochepa basi; ndipo ife tidalowa chokolo m’zimenezi.
Ndipo Mbuye wako sali owononga midzi pokhapokha akatuma mtumiki mu mzinda wawo waukulu ndi kuwawerengera mawu a m’ndime Zathu, (akakana ndi pamene timawaononga); ndiponso sitili owononga midzi pokhapokha anthu ake atakhala achinyengo.
Ndipo chilichonse chimene mwapatsidwa nchosangalatsa cha moyo wa pa dziko, ndiponso chokometsera chake (chomwe sichikhalira kutha); koma chomwe chili kwa Allah ndicho chabwino, chamuyaya; kodi bwanji simukuzindikira?
Kodi munthu yemwe tamulonjeza lonjezo labwino (kuti akalowa ku Munda wamtendere) kotero kuti iye akakumana nalo (lonjezolo), angafanane ndi yemwe tamsangalatsa ndi zosangalatsa za moyo wa pa dziko basi, kenako iye nkukhala mmodzi okaponyedwa (ku Moto) tsiku la chiweruziro (Qiyâma)?
Ndipo (akumbutse) tsiku limene (Allah) adzawaitana, adzati: “Ali kuti anzanga aja omwe mumanena (kuti ndianzananga)?”
Ndipo kudzanenedwa: “Itanani aphatikizi anu.” Choncho adzawaitana koma sadzawayankha. Ndipo azawawona mavuto (pa nthawiyo azakhumba) akadakhala oongoka (pa dziko lapansi kotero kuti akadapeza mtendere pa tsiku la chimaliziro).
Ndipo (akumbutse) tsiku limene adzawaitana, nkudzati: “Kodi mudawayankha chiyani Atumiki?”
Ndipo Mbuye wako amalenga chimene wafuna ndi kuchisankha (chimene wafuna). Iwo alibe chifuniro. Allah wapatukana ndi zonse zochepetsa ulemelero Wake, ndipo watukuka ku zomwe akumphatikiza nazo.
Ndiponso Mbuye wako akudziwa zimene zifuwa zawo zikubisa (maganizo awo) ndi zimene akuwonetsera (poyera).
Ndipo Iye ndi Allah; palibe wopembedzedwa m’choonadi koma Iye. Kuyamikidwa konse (kwabwino) pachiyambi ndi kumapeto nkwake; ndipo kulamulanso nkwake, ndipo inu mudzabwerera kwa Iye.
Ndipo amene adapatsidwa kuzindikira adanena: “Tsoka lanu! Malipiro a Allah ngabwino kwa yemwe wakhulupirira ndi kuchita zabwino, (kuposa izi ali nazo Qaruni); ndipo sadzapatsidwa zimenezi koma okhawo ali opirira.”
Ndipo amene ankalakalaka ulemelero wake dzulo adayamba kunena: “E zoonadi Allah amamuonjezera chuma amene akumfuna mwa akapolo Ake (chingakhale ali oipa wosayanjidwa ndi Iye), ndipo amamuchepetsera chuma (amene wamfuna kotero ngakhale ali woyanjidwa ndi Iye.) Pakadapanda Allah kutimvera chisoni. (Mkukhumbira kwathu pa zimene adampatsa Qaruna akadatikwilira m’nthaka. Ha! Zoonadi osakhulupirira sangapambane.”
Ndithudi yemwe wakulamula kuitsata Qur’an, mwachoonadi adzakubwezera pa malo pobwerera. Nena! “Mbuye wanga ndi yemwe akudziwa amene wadza ndi chiongoko ndi yemwe ali m’kusokera koonekera poyera.’’
Ndipo iwe sudali kulakalaka kuti ungapatsidwe buku (pamodzi ndi uneneri) koma izi zidachitika pa chifundo chochokera kwa Mbuye wako; choncho usakhale m’thandizi wa anthu osakhulupirira (Allah).
Ndipo asakutsekereze kutsatira ndime za (mawu a) Allah pa mbuyo povumbulutsidwa pa iwe, ndipo aitanire anthu kwa Mbuye wako, komatu usakhale m’gulu la anthu omphatikiza Allah ndi mafano.
Ndipo usapemphe mulungu wina pa modzi ndi Allah. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye Yekha. Chinthu chilichonse chidzaonongeka kupatula Nkhope Yake. Ulamuliro (wazinthu zonse) uli kwa Iye ndipo kwa Iye ndi kumene mudzabwerera nonsenu.
Share