Surah An-Noor ( The Light )

Surah An-Noor ( The Light ) - Chewa Aya count 64

Iyi ndi Sura; taivumbulutsa, ndipo taikamo malamulo. Ndipo m’menemo tatumizamo Ayah (ndime) zomveka kuti mukumbukire (malamulo ndi kuchita nawo m’njira yoyenera).
Mwamuna wa chiwerewere sakwatira mkazi (wabwino) koma wachiwerewere mnzake, kapena mkazi wopembedza mafano. Nayenso mkazi wachiwerewere sakwatiwa ndi mwamuna (wabwino) koma wachiwerewere mnzake, kapena wopembedza mafano. Ndipo zimenezi zaletsedwa kwa okhulupirira.
Kupatula amene alapa pambuyo pa zimenezo, ndipo nkukonza (zochita zawo), ndithu Allah Ngokhululuka; Ngwachisoni, (awakhululukira).
Ndipo amene akunamizira akazi awo (kuti achita chiwerewere) ndipo iwo nkukhala opanda mboni, koma (iwo) okha, choncho umboni wa mmodzi wa iwo (umene ungamchotsere chilango chomenyedwa zikoti 80), ndikupereka umboni kanayi polumbilira Allah kuti ndithu iye ndi mmodzi mwa onena zoona.
Ndipo kachisanu (alumbire) kuti matembelero a Allah akhale pa iye ngati (iye) ali m’modzi mwa onama.
Ndipo kachisanu (alumbire) kuti mkwiyo wa Allah ukhale pa iye ngati (mwamuna wake) ali mmodzi mwa onena zoona.
Ndipo pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo Chake pa inu (mukadavutika). Ndipo ndithu Allah Ngolandira kulapa;. Wanzeru zakuya.
Ndithu amene adza ndi bodza (ponamizira Mayi Aisha {r.a}, yemwe ndi Mkazi wa Mtumiki {s.a.w}, kuti wachita chiwerewere), ndi gulu la mwa inu. Musaganizire zimenezo kuti nzoipa kwa inu, koma kuti zimenezo nzabwino kwa inu. Ndipo munthu aliyense wa iwo apeza (chilango) pa machimo amene wawachitawo. Ndipo yemwe wasenza gawo lalikulu la uchimowo mwa iwo, adzapeza chilango chachikulu.
Allah akukulangizani kuti: “Musabwerezenso kuchita zonga zimenezi mpaka kalekale, ngati inu muli okhulupirira enieni.”
Ndipo Allah akukufotokozerani Ayah (ndime) Zake mwatsatanetsatane. Ndipo Allah Ngodziwa; Ngwanzeru zakuya.
Ndipo pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo Chake pa inu, (pakadapezeka zauve). Koma ndithu Allah Ngoleza; Ngwachisoni chosatha.
Ndithu amene akunamizira akazi oyera (kumachitidwe achiwerewere), odziteteza kumachitidwe oipa, okhulupirira, atembeleredwa pa dziko lapansi ndi patsiku la chimaliziro. Ndipo chilango chachikulu chili pa iwo.
Auze okhulupirira achimuna kuti adzolitse maso awo (asayang’ane zoletsedwa), ndipo asunge umaliseche wawo. Ichi nchoyera kwambiri kwa iwo. Ndithu Allah akudziwa nkhani za zonse zomwe achita.
Ndipo auze okhulupirira achikazi kuti adzolitse maso awo, ndikusunga umaliseche wawo, ndipo asaonetse (poyera) zomwe amadzikongoletsa nazo kupatula zimene zaonekera poyera (popanda cholinga chotero). Ndipo afunde kumutu mipango yawo mpaka m’zifuwa zawo; ndipo asaonetse poyera zodzikongoletsa nazo koma kwa amuna awo, kapena atate awo, kapena apongozi awo, kapena ana awo, kapena ana a amuna awo, kapena abale awo, kapena ana a abale awo, kapena ana a alongo awo, kapena akazi anzawo (achisilamu). Kapena yemwe wapatidwa ndi dzanja lamanja (monga kapolo), kapena otsatira (antchito) omwe ndi amuna opanda zilakolako za akazi ndi ana omwe sadziwa za akazi. Ndipo asamenyetse miyendo yawo (pansi) kuti zidziwike zimene akubisa mwa zomwe amadzikongoletsa nazo. Ndipo tembenukirani kwa Allah, nonse inu okhulupirira kuti mupambane.
Ndipo zikwatitseni mbeta za mwa inu (mfulu), ndi akapolo anu amene ali abwino (achimuna) ndi adzakazi anu. Ngati ali osauka Allah awalemeletsa kuchokera m’zabwino Zake. Ndipo Allah za ufulu Zake nzambiri (zopanda muyeso, ndiponso) Ngodziwa kwabasi.
Ndipo ndithu tatumiza kwa inu Ayah (ndime) zofotokoza (zofunika zonse) mwatsatanetsatane, ndi mafanizo (okuphanulani maso) pa za amene adamuka patsogolo panu, ndi phunziro kwa oopa (Allah).
Allah ndiye Kuunika kwa kuthambo ndi nthaka. Fanizo la kuunika Kwake (powaongolera akapolo Ake) lili ngati “Mishikati” (chibowo cha pa khoma choikapo nyali) yomwe mkati mwake mwaikidwa nyali. Nyali ili m’galasi. Ndipo galasilo lili ngati nyenyezi yowala. Nyali imeneyo imayatsidwa ndi mafuta ochokera ku mtengo wodalitsidwa wa mzitona, womwe suli mbali yakuvuma ngakhale kuzambwe; (umamenyedwa kwambiri ndi dzuwa pamene likutuluka, ndi parnene likulowa). Mafuta ake ngoyandikira kuwala okha (chifukwa champhamvu yake) ngakhale moto usanawakhudze. Kuunika pamwamba pa kuunika! Allah amamuongolera ku kuunika Kwake amene wamfuna. Allah amaponya mafanizo kwa anthu (kuti aganizire ndi kupeza phunziro), ndipo Allah Ngodziwa chilichonse.
(Apezeke akupemphera kasanu) m’nyumba zomwe Allah walamula kuti zilemekezedwe; ndipo m’menemo dzina Lake litchulidwe; azimulemekeza m’menemo (m’misikiti) kum’mawa ndi kumadzulo;
Ndipo amene sadakhulupirire, ntchito zawo (zimene akuziona ngati zabwino) zidzakhala ngati zideruderu m’chipululu chamchenga; waludzu nkumaganizira kuti ndimadzi; ndipo akapita pamenepo, osapezapo chilichonse. (Nawonso pomwe adzadza kuzochita zawo zabwino patsiku la Qiyâma sadzapeza mphotho iliyonse, chifukwa chakuti adachimenya nkhondo Chisilamu). Ndipo adzapeza Allah kumeneko, ndipo adzamkwaniritsira chiwerengero chake ndipo Allah Ngwachangu powerengera.
Kapena (ntchito zawo zoipazo) zili ngati m’dima mkati mwa nyanja yamadzi ochuluka yomwe yaphimbidwa ndi mafunde, ndipo pamwamba pa mafundewo pali mafundenso. Ndiponso pamwamba pake (mafundewo) pali mitambo. M’dima uwu pamwamba pa m’dima uwu. Akatulutsa mkono wake, sangathe kuuona (chifukwa cha kuchindikala kwa m’dima). Ndipo amene Allah sadampatse kuunika, sakhala nako kuunika.
Kodi suona kuti zonse zopezeka kumwamba ndi pansi zikumulemekeza Allah, kudzanso mbalame zikatambasula mapiko ake (ngakhalenso zikapanda kutambasula). Chilichonse (mwa zimenezo) chikudziwa pemphero lake ndi m’mene chingamulemekezere (Mlengi wake). Ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene akuchita.
Allah amasintha usiku ndi usana (pambuyo pa usiku, umadza usana, ndipo pambuyo pa usana, umadza usiku). Ndithu m’zimenezo muli phunziro kwa anthu ozindikira (zinthu).
Ndithu tavumbulutsa Ayah (ndime) zofotokoza momveka (chilichonse chofunika pa chipembedzo). Ndipo Allah amamuongolera ku njira yolunjika amene wamfuna.
Ndipo akawaitanira kwa Allah ndi Mtumiki Wake kuti awaweruze pakati pawo, ena a iwo akukana zimenezo (akadzizindikira okha kuti ngolakwa).
Koma akaona kuti chilungamo chili kwa iwo, amam’dzera (Mtumiki mwachangu) uku akusonyeza kumvera.
Ndipo akulumbilira dzina la Allah, kulumbira kwakukulu kuti ukawalamula (kupita ku nkhondo), ndithu apita. Nena: “Musalumbire; kumvera kwanu nkodziwika (kuti nkwabodza); ndithu Allah akudziwa nkhani zonse zomwe muchita.
Nena: “Mverani Allah, ndiponso Mverani Mtumiki. Koma ngati mutembenuka, iye ali nazo zimene wasenzetsedwa (kuti azifikitse kwa inu), (ndipo) inunso muli nazo zimene mwasenzetsedwa (kuti muzitsate). Ndipo mukamumvera, muongoka. Ndipo pa Mtumiki palibe china chake koma kufikitsa (uthenga) momveka.
Palibe kulakwa pa akhungu (osapenya) ndiponso palibe kulakwa pa olumala; palibenso kulakwa pa odwala, ngakhalenso pa inu eni ngati muli kudya m’nyumba zanu kapena m’nyumba za atate anu, kapena m’nyumba za amayi anu, kapena m’nyumba za abale anu, kapena m’nyumba za alongo anu, kapena m’nyumba za abambo anu ang’ono kapena akulu, kapena m’nyumba za azakhali anu, kapena m’nyumba za atsibweni anu, kapena m’nyumba za amayi anu akulu kapena ang’ono, kapena m’nyumba za omwe mukuwasungira makiyi, kapena (m’nyumba za) anzanu; palibe kulakwa pa inu ngati mukudyera limodzi kapena payekhapayekha. Ndipo mukamalowa m’nyumba dziperekereni nokha salaamu. (lonjero ili) ndi malonje ochokera kwa Allah amadalitso, abwino. Umo ndi momwe Allah akukulongosolerani Ayah (ndime) Zake kuti muzindikire.
Share