Surah Al-Mu'minoon ( The Believers )

Surah Al-Mu'minoon ( The Believers ) - Chewa Aya count 118

۞ Ndithu apambana okhulupirira (mwa Allah).
Amene amakhudzumuka pa mapemphero awo (poipereka mitima yawo kwa Allah modzichepetsa).
Kupatula kwa akazi awo ndi adzakazi omwe manja awo akumanja apeza. Choncho iwo (pakukumana ndi amenewo) saali odzudzulidwa.
Koma omwe angafune zosemphana ndi izi (kulumikizana ndi mkazi posiya njira ziwirizi) iwowo ndiwo opyola malire (a Allah).
Ndi omwe akusunga mapemphero awo (popemphera mu nthawi zake ndi kutsata malamulo ake uku ali odzichepetsa).
Amene adzalandira Munda wamtendere (wotchedwa) Fir’dausi (Munda wapamwamba kwambiri). M’menemo iwo adzakhala nthawi yaitali.
Kenako tidalenga ana ake ndi dontho lamadzi (ambewu ya munthu) lomwe lidaikidwa pamalo osungidwa.
Ndipo ndithu tapanga njira zisanu ndi ziwiri (mitambo) pamwamba panu, ndipo ndithu (Ife) sitisiya kulabadira zolengedwa.
Ndipo tatsitsa madzi mwamuyeso kuchokera kumwamba, ndi kuwakhazikitsa m’nthaka; ndipo ndithu Ife ndi okhoza kuwachotsa (kuti musathandizike nawo, koma sitidachite zimenezo chifukwa chokuchitirani chifundo).
Ndipo (tidakupangirani) mtengo womera pa phiri la Sinai, womwe umatulutsa mafuta; ndipo ndindiwo kwa amene amadya. (Mtengo wake ndi mzitona).
Ndipo pa msana pa izo ndi pamwamba pa zombo, mumanyamulidwa.
(Nuh) adati: “Mbuye wanga ndipulumutseni pazomwe anditsutsa!”
Choncho tidamuvumbulutsira (mawu akuti): “Panga chombo moyang’aniridwa ndi kudziwitsidwa ndi Ife.” Ndipo lamulo Lathu likadza ndi kufwamphuka madzi mu uvuni, lowetsa mkati mwake (mwa chombocho) chilichonse ziwiriziwiri, chachimuna ndi chachikazi ndi banja lako, kupatula yemwe liwu latsogola pa iye kuti aonongeke mwa iwo. Ndipo usandilankhule za omwe adzichitira (okha) zoipa ndithu iwo amizidwa (m’madzi).
Ndipo (potsika), nena: “E Mbuye wanga! Nditsitseni; kutsitsa kwa madalitso, pakuti Inu ndinu wotsitsa bwino kwambiri kuposa otsitsa.”
Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo. Ndithu Ife tili (ndi udindo) wowayesa ndi mayeso osiyanasiyana.
Sizingachitike, sizingachitike, zimene mukulonjezedwazi!
Palibe (moyo wina) koma moyo wathu wapadziko lapansiwu basi! Tikufa ndiponso kukhala ndi moyo! Ndipo sitidzaukitsidwa m’manda.
Uyu saali kanthu (amene akudzitcha kuti ndi Mtumiki) koma ndi munthu basi, akupekera Allah bodza, ndipo ife sitimkhulupirira.”
(Mtumikiyo) adati: “E Mbuye wanga! Ndipulumutseni pachifukwa chakuti anditsutsa.”
Choncho, mkuwe wa (chilango) choonadi udawaononga, ndipo tidawachita ngati zinyalala (zongotengedwa ndi madzi). Choncho, kuonongeka kudatsimikizika pa anthu osalungama.
Kenaka tidatuma atumiki Athu motsatizana; (wina pambuyo pa mnzake). Ndipo mbadwo uliwonse pamene adaufikira mtumiki wake, udamtsutsa; ndipo tidawaononga motsatana; ndipo tidawachita kukhala nkhani (za anthu.) Ndipo kuonongeka kudatsimikizika pa anthu osakhulupirira.
Choncho adawatsutsa onse awiri, ndipo adali m’gulu la oonongedwa.
Ndipo tidamchita mwana wa Mariya ndi mayi wake kukhala chisonyezo (choonetsa kukhoza kwathu). Ndipo tidawapatsa malo othawirapo, pachikweza, chokhazikika pomwenso padali akasupe.
(Tidauza mibadwo yawo): “Ndithu mpingo wanuwu ndi mpingo umodzi, ndipo Ine Ndine Mbuye wanu; choncho ndiopeni.”
Koma adadula chinthu chawochi (chipembedzo chawo) pakati pawo mipatukomipatuko; gulu lililonse limasangalalira chimene lili nacho.
Choncho, asiye mu umbuli wawo kufikira nthawi (yakufa kwawo).
Ndithu amene amakhala amantha chifukwa choopa Mbuye wawo, (ndi m’mene mathero awo adzakhalire);
Ndi omwenso amapereka (Zakaat ndi sadaka kuchokera m’chuma) chimene apatsidwa, uku mitima yawo ili yoopa kuti adzabwerera kwa Mbuye wawo;
Amenewa ndiamene akuchita changu pa zinthu zabwino, ndipo iwo akutsogolera (ena) pa zimenezo.
Ndipo sitikakamiza munthu, koma chimene angathe (kuchichita). Ndipo tili naye kaundula (wosunga chilichonse) yemwe adzayankhula choonadi ndipo iwo sadzaponderezedwa.
Kufikira tikadzawaika m’chilango amene ali opeza bwino awo, pompo adzakuwa (ndi kupempha chipulumutso).
(Kudzanenedwa kwa iwo): “Musalire lero (ndi kupempha chipulumutso)! Ndithu inu simupulumutsidwa ndi Ife.”
Uku mukudzikweza; nkumakambirana usiku za chabechabe zoinyoza (Qur’an).”
Kodi kapena sadam’dziwe Mtumiki wawoyu (makhalidwe ake) kotero kuti iwo akum’kana?
Kodi kapena ukuwapempha malipiro (nchifukwa chake akuchikana chipembedzochi)? Koma malipiro a Mbuye wako ndiwo abwino; ndipo Iye ndi Wopereka Wabwino kuposa opereka.
Ndipo ndithu iwe ukuwaitanira ku njira yolunjika; (supempha malipiro kwa iwo pa kuitanako).
Nena: “Kodi nthaka njayani ndi zomwe zili m’menemo, ngati inu mukudziwa (kanthu)!”
Adzanena kuti: “Nza Allah!” Nena: “Nanga bwanji simukumkumbukira (kuti Iye Ngokhoza chilichonse)?
Nena: “Kodi ndani Mbuye wa thambo zisanu ndi ziwiri, ndi Mbuye wa Arsh (Mpando wachifumu) yaikulu?”
Anena (kuti): “Nza Allah.” Nena: “Nanga bwanji simukumuopa?”
Nena: “Kodi ndani yemwe m’manja mwake muli mphamvu yolamulira chinthu chilichonse? Ndipo Iye amateteza zonse. Ndipo palibe chimene chingatetezedwe kuchilango Chake. Ngati inu mukudziwa.”
Anena (kuti): “Ndi Allah.” Nena: “Nanga mukulodzedwa bwanji (ndi satana)?”
Koma tawabweretsera choonadi; ndithu iwo ngabodza (potsutsana ndi choonadicho).
Allah sadadzipangire mwana, ndipo padalibe pamodzi ndi Iye mulungu (wina), ngati zikadakhala choncho ndiye kuti mulungu aliyense akadatenga zimene adalenga, ndipo milungu ina ikadaipambana milungu inzawo (polimbanirana ufumu), Allah wapatukana nazo kwambiri zimene akusimbazo.
Nena: “E Mbuye wanga! Ngati mungandionetse zomwe akulonjezedwa (ndikadali ndi moyo),
Ndipo nena: “E Mbuye wanga! Ndikudzitchinjiriza ndi Inu kumanong’onong’o a satana.”
“Ndiponso ndikudzitchinjiriza ndi inu Mbuye wanga kuti asandidzere.”
Kufikira m’modzi wawo ikam’dzera imfa, amanena: “Mbuye wanga! Ndibwezereni (ku moyo wa pa dziko),”
“Kuti ndikachite zabwino pa zimene ndidasiya.” (Angelo amayankha kuti): “Iyayi! Ndithu awa ndi mawu basi amene iye akuyankhula (imfa ikamfika).” Ndipo patsogolo pawo pali chiyembekezo; (moyo wamasautso kwa oipa; ndipo wamtendere kwa abwino) kufikira tsiku limene adzaukitsidwa.
Mbuye wathu! Titulutseni umu (m’moto ndikutibwezera ku dziko lapansi kuti tikachite ntchito yabwino); ngati titabwerezanso kuchita zoipa, ndiye kuti tidzakhaladi oipa (odziononga tokha).”
(Allah) adzati: “Khalani chete m’menemo, monyozeka! Ndipo musandilankhule!”
Ndithu mwa akapolo anga lidalipo gulu lomwe linkanena: “Mbuye wathu! Takhulupirira; choncho tikhululukireni ndi kutichitira chifundo; ndipo inu Ngabwino kwambiri kuposa (ena onse) ochita chifundo.”
“Ndithu Ine lero ndawalipira (Munda wamtendere) chifukwa cha kupirira kwawo; kuti ndithu iwo ndiwo opambana.”
Adzanena: “Kodi mudakhala nthawi yotani padziko pa chiwerengero cha zaka?”
Adzayankha: “Tidakhala tsiku limodzi kapena gawo la tsiku; afunse owerengera.” (Adzatero poyerekeza ndi kutalika kwa moyo wamasautso ku Moto).
Adzanena: “Inu simudakhale (kudzikoko) koma pang’ono basi, mukadakhala mukudziwa (chilango chomwe chakufikanichi, sibwenzi mukuchita zoipa).”
Watukuka Allah, Mfumu ya choonadi; palibe wompembedza mwachoonadi koma Iye, Bwana wa Arsh (Mpando wachifumu) yolemekezeka (kwambiri).
Choncho nena: “Mbuye wanga! Ndikhululukireni ndikundichitira Chifundo! Inu Ngabwino kuposa achifundo.”
Share