Select surah 1- Al-Fatihah ( The Opening ) 2- Al-Baqarah ( The Cow ) 3- Al-Imran ( The Famiy of Imran ) 4- An-Nisa ( The Women ) 5- Al-Maidah ( The Table spread with Food ) 6- Al-An'am ( The Cattle ) 7- Al-A'raf (The Heights ) 8- Al-Anfal ( The Spoils of War ) 9- At-Taubah ( The Repentance ) 10- Yunus ( Jonah ) 11- Hud 12- Yusuf (Joseph ) 13- Ar-Ra'd ( The Thunder ) 14- Ibrahim ( Abraham ) 15- Al-Hijr ( The Rocky Tract ) 16- An-Nahl ( The Bees ) 17- Al-Isra ( The Night Journey ) 18- Al-Kahf ( The Cave ) 19- Maryam ( Mary ) 20- Taha 21- Al-Anbiya ( The Prophets ) 22- Al-Hajj ( The Pilgrimage ) 23- Al-Mu'minoon ( The Believers ) 24- An-Noor ( The Light ) 25- Al-Furqan (The Criterion ) 26- Ash-Shuara ( The Poets ) 27- An-Naml (The Ants ) 28- Al-Qasas ( The Stories ) 29- Al-Ankaboot ( The Spider ) 30- Ar-Room ( The Romans ) 31- Luqman 32- As-Sajdah ( The Prostration ) 33- Al-Ahzab ( The Combined Forces ) 34- Saba ( Sheba ) 35- Fatir ( The Orignator ) 36- Ya-seen 37- As-Saaffat ( Those Ranges in Ranks ) 38- Sad ( The Letter Sad ) 39- Az-Zumar ( The Groups ) 40- Ghafir ( The Forgiver God ) 41- Fussilat ( Explained in Detail ) 42- Ash-Shura (Consultation ) 43- Az-Zukhruf ( The Gold Adornment ) 44- Ad-Dukhan ( The Smoke ) 45- Al-Jathiya ( Crouching ) 46- Al-Ahqaf ( The Curved Sand-hills ) 47- Muhammad 48- Al-Fath ( The Victory ) 49- Al-Hujurat ( The Dwellings ) 50- Qaf ( The Letter Qaf ) 51- Adh-Dhariyat ( The Wind that Scatter ) 52- At-Tur ( The Mount ) 53- An-Najm ( The Star ) 54- Al-Qamar ( The Moon ) 55- Ar-Rahman ( The Most Graciouse ) 56- Al-Waqi'ah ( The Event ) 57- Al-Hadid ( The Iron ) 58- Al-Mujadilah ( She That Disputeth ) 59- Al-Hashr ( The Gathering ) 60- Al-Mumtahanah ( The Woman to be examined ) 61- As-Saff ( The Row ) 62- Al-Jumu'ah ( Friday ) 63- Al-Munafiqoon ( The Hypocrites ) 64- At-Taghabun ( Mutual Loss & Gain ) 65- At-Talaq ( The Divorce ) 66- At-Tahrim ( The Prohibition ) 67- Al-Mulk ( Dominion ) 68- Al-Qalam ( The Pen ) 69- Al-Haaqqah ( The Inevitable ) 70- Al-Ma'arij (The Ways of Ascent ) 71- Nooh 72- Al-Jinn ( The Jinn ) 73- Al-Muzzammil (The One wrapped in Garments) 74- Al-Muddaththir ( The One Enveloped ) 75- Al-Qiyamah ( The Resurrection ) 76- Al-Insan ( Man ) 77- Al-Mursalat ( Those sent forth ) 78- An-Naba' ( The Great News ) 79- An-Nazi'at ( Those who Pull Out ) 80- Abasa ( He frowned ) 81- At-Takwir ( The Overthrowing ) 82- Al-Infitar ( The Cleaving ) 83- Al-Mutaffifin (Those Who Deal in Fraud) 84- Al-Inshiqaq (The Splitting Asunder) 85- Al-Burooj ( The Big Stars ) 86- At-Tariq ( The Night-Comer ) 87- Al-A'la ( The Most High ) 88- Al-Ghashiya ( The Overwhelming ) 89- Al-Fajr ( The Dawn ) 90- Al-Balad ( The City ) 91- Ash-Shams ( The Sun ) 92- Al-Layl ( The Night ) 93- Ad-Dhuha ( The Forenoon ) 94- As-Sharh ( The Opening Forth) 95- At-Tin ( The Fig ) 96- Al-'alaq ( The Clot ) 97- Al-Qadr ( The Night of Decree ) 98- Al-Bayyinah ( The Clear Evidence ) 99- Az-Zalzalah ( The Earthquake ) 100- Al-'adiyat ( Those That Run ) 101- Al-Qari'ah ( The Striking Hour ) 102- At-Takathur ( The piling Up ) 103- Al-Asr ( The Time ) 104- Al-Humazah ( The Slanderer ) 105- Al-Fil ( The Elephant ) 106- Quraish 107- Al-Ma'un ( Small Kindnesses ) 108- Al-Kauther ( A River in Paradise) 109- Al-Kafiroon ( The Disbelievers ) 110- An-Nasr ( The Help ) 111- Al-Masad ( The Palm Fibre ) 112- Al-Ikhlas ( Sincerity ) 113- Al-Falaq ( The Daybreak ) 114- An-Nas ( Mankind )
Translations English English - Yusuf Ali English - Transliteration English - Rowwad Translation Center English - Ahmed Ali English - Ahmed Raza Khan English - Arberry English - Daryabadi English - Hilali & Khan English - Talal Itani English - Maududi English - Mubarakpuri English - Pickthall English - Qarai English - Qaribullah & Darwish English - Sarwar English - Shakir English - Wahiduddin Khan Français Español Spanish Cortes Spanish Garcia Português Deutsch German Bubenheim & Elyas German Khoury German Zaidan Italiano Nederlands Dutch Leemhuis Dutch Siregar Русский Russian Абу Адель Russian Аль-Мунтахаб Russian Крачковский Russian Кулиев Russian Османов Russian Порохова Russian Саблуков Română Greek Svenska Shqip Shqip Feti Mehdiu Shqip Sherif Ahmeti Bosanski Bosnian Mlivo Български České České Nykl Norwegian Türkçe Turkish Alİ Bulaç Turkish Çeviriyazı Turkish Diyanet İşleri Turkish Diyanet Vakfı Turkish Edip Yüksel Turkish Elmalılı Hamdi Yazır Turkish Öztürk Turkish Suat Yıldırım Turkish Süleyman Ateş Polski Croatian Georgian Српски українська Macedonian Lithuanian Azəri Azerbaijani Məmmədəliyev & Bünyadov اردو Urdu Maududi Urdu Ahmed Raza Khan Urdu Jalandhry Urdu Qadri Urdu Jawadi Urdu Junagarhi Urdu Najafi 日本語 한국어 中文 Chinese (Traditional) Hindi Hindi Muhammad Farooq Khan മലയാളം Malayalam Karakunnu & Elayavoor தமிழ் Melayu Indonesian Indonesian Quraish Shihab Indonesian Tafsir Jalalayn বাংলা জহুরুল হক فارسى كوردی Pashto Тоҷикӣ Татарча ไทย ئۇيغۇرچە Ўзбек Uzbek Mikhailo Yakuboych ދިވެހި Sindhi অসমীয়া Bisayan Iranun Maguindanaon Dari Hebrew қазақ тілі Khmer Marathi Hausa soomaali Swahili Afar N'ko Akan Chewa Dagbani Kinyarwanda Lingala Luganda Luhya Malagasy Mõõré Yaw Amazigh Amharic
Your browser does not support the audio element. E inu anthu! Opani Mbuye wanu (ndipo kumbukirani tsiku la Kiyâma). Ndithu kugwedezeka kwa Kiyâma ndichinthu chachikulu (kwabasi).
Tsiku limene mudzaione (Qiyâmayo), mkazi aliyense woyamwitsa adzaiwala (mwana wake) womuyamwitsa, ndipo (mkazi) aliyense wapakati adzataya pakati pake; ndipo udzawaona anthu ataledzera, pomwe sadaledzere; koma ndi chilango chaukali cha Allah (chimene chawapeza).
Ndipo alipo ena mwa anthu amene akutsutsa za Allah popanda kuzindikira, ndipo akutsatira satana aliyense wolakwa.
(Za satana), kwalembedwa kuti amene amsankhe kukhala bwenzi lake, ndithu iye amsokeretsa ndi kumtsogolera ku chilango cha Moto.
E inu anthu! Ngati muli m’chikaiko za kuuka ku imfa, (ndipo mukuona kuti nzosatheka, yang’anani mmene tidakulengerani). Ndithu Ife tidakulengani ndi dothi, ndipo (timakulengani) ndi dontho la umuna, komanso (umunawo udasanduka) gawo lamagazi, kenako gawo la mnofti woumbidwa (chithunzi cha munthu) ndi wosaumbidwa, kuti tikulongosolereni (kukhoza Kwathu;) ndipo Ife timachikhazikitsa mchiberekero; chimene tifuna kufikira nthawi yake yoyikidwa kenako timakutulutsani muli khanda, (tsono timakulerani) kuti mufike pa nsinkhu wanu. Ndipo ena mwa inu amamwalira (asanakule), pomwe ena mwa inu amabwezedwa ku moyo wofooka (waukalamba) kotero kuti asadziwe chilichonse pambuyo pakuti adali wodziwa. Ndipo umaiona nthaka ili chetee, koma tikatsitsa madzi pamwamba pake, imagwedezeka ndi kufufuma, ndi kumeretsa mtundu uliwonse wa mmera wokongola.[287]
Zimenezo (monga kulenga munthu ndi kumeretsa mmera, ndi umboni wosonyeza) kuti Allah Woona alipo; ndikuti Iye amaukitsa akufa, ndiponso Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse.
Ndipo, ndithu Qiyâma idza; palibe chikaiko pa zimenezi, ndipo ndithu Allah adzawatulutsa amene ali m’manda.
Ndipo alipo mwa anthu amene akutsutsa za Allah popanda kuzindikira, ngakhale chiongoko, ngakhalenso buku lounika, (koma makani basi ndi kungotsata zimene akuziganizira).[288]
(Yemwe) akupinda khosi lake (chifukwa chodzikuza) kuti asokereze (anthu powachotsa) kunjira ya Allah; pa iye pali chilango choyalutsa pa moyo uno, ndipo patsiku la Qiyâma tikamulawitsa chilango cha Moto wotentha.
(Tidzamuuza kuti): “Izi ndi zomwe manja ako adatsogoza; ndithu Allah siwachinyengo kwa akapolo (Ake).”
Ndipo alipo wina mwa anthu amene akupembedza Allah cham’mphepete (mwachipembedzo). Chabwino chikampeza amatonthola nacho; koma masautso akamufika, amatembenuka ndi nkhope yake (posiya chikhulupiliro mwa Allah. Choncho) waluza moyo wa dziko lapansi ndi moyo wa tsiku la chimaliziro; kumeneko ndiko kuluza koonekera.[289]
M’malo mwa Allah, amapembedza zomwe sizingampatse masautso (ngati ataleka kuzipembedza), ndiponso zomwe sizingampatse chithandizo (akamazipembedza), ndipo kumeneko ndiko kusokera konka nako kutali.
Akupembedza omwe masautso awo ali pafupi zedi poyerekeza ndi zabwino zawo, taonani kuipa atetezi ndiponso ndi abwenzi oipa.
Ndithu Allah adzawalowetsa ku Minda yamtendere amene akhulupirira ndikuchita zabwino, mitsinje ikuyenda pansi (pa mindayo). Ndithu Allah amachita chimene wafuna.
Amene akuganiza kuti Allah samthangata (Mtumiki Wake) pa dziko lapansi ndi patsiku la chimaliziro, amange chingwe kudenga, kenako adzipachike (ngati safuna kuona Chisilamu chikufala); ndipo aone kuti kodi ndale zakezo zichotsa zimene zamkwiitsazo?
Momwemonso taivumbulutsa (Qur’an) kuti ikhale mawu omveka; ndipo ndithu Allah amaongola amene wamfuna.
Ndithu amene akhulupirira, ndi amene ali m’chipembedzo cha Chiyuda, ndi chipembedzo cha Sabia; ndi Akhrisitu, ndi Maajusi (opembedza moto), ndi ophatikiza Allah ndi mafano, ndithu Allah adzaweruza pakati pawo tsiku la chiweruziro (Qiyâma). (Osokera adzaponyedwa ku Moto ndipo olungama adzawalowetsa ku Munda wamtendere). Ndithu Allah ndi Mboni pa chinthu chilichonse.
Kodi suona kuti Allah zikumulambira zimene zili kumwamba ndi zimene zili m’nthaka, kudzanso dzuwa, mwezi, nyenyezi mapiri, mitengo, nyama ndi anthu ambiri. Koma ambirinso chilango chatsimikizika pa iwo. Ndipo amene Allah wamuyalutsa, palibe amene angampatse ulemelero; ndithu Allah amachita chimene wafuna.
Awa ndi magulu awiri amene akangana pa za Mbuye wawo (pa zomwe zili zomuyenera, ndi zosamuyenera, ndipo ena sadakhulupirire.) Choncho amene sadakhulupirire, adzawadulira nsalu za ku Moto ndi kuwaveka; ndipo pamwamba pa mitu yawo padzathiridwa madzi otentha.
Chifukwa cha madziwo zidzasungunuka zomwe zili m’mimba mwawo ndiponso makungu (awo).
Ndipo (kuonjezera pa zimenezi) adzakhala nazo nyundo zachitsulo (zowamenyera).
Nthawi iliyonse akafuna kutuluka m’menemo, chifukwa chakumva kupweteka, adzabwezedwa momwemo (ndipo angelo uku akuwamenya ndi nyundo), ndi (kuwauza): “Chilaweni chilango chootcha.”
Ndithu Allah adzalowetsa amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, ku Minda ya mtendere komwe mitsinje ikuyenda pansi (ndi pasogolo) pake; m’menemo akavekedwa (ndi angelo) zibangili za golide ndi ngale; ndipo zovala zawo m’menemo zidzakhala za silika.
Ndipo adzatsogozedwa (kupita kumalo) kokamba mawu abwino okhaokha; ndiponso adzatsogozedwa ku njira ya Mwini kutamandidwa (kunjira yonkera ku Jannah).
Ndithu. amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake) ndipo nkumatsekereza ena ku njira ya Allah, (ndiponso nkumatsekereza kulowa) mu Msikiti Wopatulika umene tidauchita kuti ukhale wa anthu onse mofanana kwa amene akukhala m’menemo ndi kwa alendo, (anthu otere tidzawalanga ndi chilango chaukali), ndipo aliyense wofuna kuchita zopotoka m’menemo mosalungama, timulawitsa chilango chowawa zedi.
Ndipo (kumbukira) pamene tidamkhazika Ibrahim (ndi kumlondolera) pamalo pa Nyumba (yopatulikayo; tidamuuza kuti): “Usandiphatikize ndi chilichonse; ndipo iyeretse nyumba yanga chifukwa cha amene akuizungulira ndi kumakhala pompo (pochita mapemphero awo); ndi omwe amawerama ndi kugwetsa nkhope zawo pansi.[290]
Ndipo (tidamuuza): “Lengeza kwa anthu za Hajj; akudzera (ena) oyenda ndi mapazi, ndipo (ena ali) pamwamba pa chiweto choonda (chifukwa chamasautso a paulendo); adza kuchokera kunjira zamtalimtali.
Kuti adzaone zabwino zawo, ndikuti (achulukitse) kutchula dzina la Allah m’masiku odziwika (ubwino wake), kupyolera m’zimene wawapatsa monga ziweto za miyendo inayi. Ndipo idyani ina mwa nyamayo ndi kum’dyetsa wovutika, wosauka.
Kenako adziyeretse kuzitakataka zawo, ndipo akwaniritse naziri (malonjezo) zawo ndikuzungulira nyumba yakale.
Umo ndi momwe zikhalire; ndipo amene alemekeze zinthu zopatulika za Allah kutero ndi bwino kwa iyeyo pamaso pa Mbuye wake. Ndipo ziweto za miyendo inayi nzovomerezeka kwa inu kuzidya, kupatula zomwe zatchulidwa kwa inu (m’Qur’an kuti nzoletsedwa); choncho upeweni uve wa mafano, ndiponso pewani mawu abodza.
Uku mutapendekera kwa Allah Yekha, osati kum’phatikiza (Allah). Ndipo amene akuphatikiza Allah ndi mafano, ali ngati wogwa kuchokera kumwamba, kenako mbalame nkumuwakha, kapena mphepo kukamtaya malo akutali.
Zimenezo ndikuti amene alemekeze zizindikiro za chipembedzo cha Allah, kutero ndichinthu choonetsa kuopa Allah m’mitima.
(Ziweto zimene mukutumiza ku Makka monga nsembe) muli nazo zithandizo mmenemo (monga kukwera ndi kukama mkaka) kufikira nthawi yodziwika, (yomwe ndi nthawi yozizingira); kenako malo ozizingira ndi pafupi ndi Nyumba yakalekaleyo.
Ndipo mpingo uliwonse tidaupangira malo ozingira nsembe zamapemphero kuti atchule dzina la Allah pa zomwe wawapatsa monga ziweto zamiyendo inayi. Choncho mulungu wanu ndi Mulungu m’modzi Yekha; gonjerani kwa Iye; ndipo odzichepetsa auze nkhani yabwino.
Omwe Allah akatchulidwa, mitima yawo imanjenjemera ndiponso amapirira pa zomwe zawapeza, ndipo amapemphera Swala moyenera ndi kupereka chopereka kuchokera m’zomwe tawapatsa.
Ndipo ngamira (ng’ombe, mbuzi ndi mbelere) tadzichita kwa inu kuti zikhale mwa zizindikiro za chipembedzo cha Allah; m’zimenezo muli zabwino kwa inu; choncho litchuleni dzina la Allah pa izo pamene zikuima mondanda (uku mukuzizinga,) ndipo zikagwa cham’nthiti, idyani (nyama yake) ndikumdyetsa yemwe akungozungulirazungulira, wosapempha ndi wopempha yemwe. Momwemo tazigonjetsa kwa inu (pochita kuti zikugonjereni) kuti muthokoze.
(Nyamazo) Allah siimfika minofu yake ngakhale magazi ake, koma kuopa kuchokera mwa inu ndiko kumene kumamfika; momwemo wazichita (nyamazo) kukhala zogonjera inu kuti mumlemekeze Allah chifukwa cha kukuongolaniku. Auze nkhani yabwino ochita zabwino.
Ndithu Allah amawateteza amene akhulupilira, ndithu Allah sakonda aliyense wachinyengo, wosathokoza.
Chaperekedwa chilolezo kwa (Asilamu) amene akuputidwa (ndi adani awo kuti abwezere) chifukwa chakuti iwo achitiridwa zoipa; ndipo ndithu Allah ngokhoza kuwathandiza.
Omwe atulutsidwa m’nyumba zawo popanda chilungamo, koma pachifukwa chakuti akunena: “Mbuye wathu ndi Allah.” Ndipo pakapanda Allah kukankha anthu ena kupyolera mwa ena, (popatsa ena mphamvu kuti agonjetse ena), ndiye kuti Masinagogi, Matchalitchi, nyumba zina zopempheleramo ndi Misikiti momwe dzina la Allah likutchulidwa mochuluka zikadagumulidwa. Ndithu Allah am’thangata amene akuthangata chipembedzo Chake; ndithu Allah Ngwanyonga, Wogonjetsa chilichonse.[291]
Omwe akuti tikawakhazika pa dziko mwa ubwino, amachita mapemphero a Swala moyenera ndi kupereka Zakaat, ndi kulamula zabwino ndi kuletsa zoipa; ndipo mabwelero a zinthu nkwa Allah basi.
Ndipo ngati akukuyesa wabodza, (awa Akafiri, sizachilendo), ndithu adatsutsanso (aneneri awo) patsogolo pawo anthu a Nuh, Aadi, a Samudu.
Anthu a Ibrahim, anthu a Luti.
Ndi anthu a ku Madiyan; nayenso Mûsa adayesedwa wabodza (adamkana). Ndipo osakhulupirira ndidawapatsa nthawi, kenako ndidawathira m’dzanja. Nanga chidali bwanji chilango changa.
Ndi midzi ingati tidaiononga yomwe inkachita zoipa? Zipupa zitagwera pa madenga ake. Ndipo ndi zitsime (zingati) zomwe zidasiidwa, ndi nyumba zikuluzikulu zomwe zidali zolimba?
Kodi sayendayenda pa dziko kuti akhale ndi mitima (yanzeru) yowazindikiritsa ndi makutu omvera? Ndithu maso sagwidwa khungu, (khungu loononga chipembedzo), koma mitima yomwe ili m’zifuwa ndi imene imagwidwa khungu (loononga chipembedzo).
Ndipo akukufulumizitsa kuti udzetse chilango. Komatu Allah sadzaswa lonjezo Lake (limene adaliika lakuti chilango chenicheni chidzakhala patsiku la chimaliziro). Ndipo ndithu tsiku limodzi kwa Mbuye wako lili ngati zaka chikwi chimodzi mukawerengedwe kanu.
Kodi ndi (anthu a) midzi ingati amene ndidawapatsa nthawi pomwe ankachita zoipa? Kenako ndidawathira m’dzanja. Ndipo kwa Iye nkobwerera.
Nena: “E inu anthu! Ndithu ine kwa inu ndine Mchenjezi woonekera.”
“Tsono amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, chikhululuko ndi rizq laulemu zili pa iwo.”
“Ndipo amene akulimbikira kulimbana ndi Ayah Zathu, iwowo ndi anthu a ku Moto.”
Ndipo palibe pamene tidatuma mtumiki ngakhale m’neneri patsogolo pako, koma akamawerenga, satana amaponya (zosokoneza) m’kuwerenga kwakeko; koma Allah amachotsa zomwe satana akuponya; kenako nkuzilongosola Ayah Zake. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri, Wanzeru zakuya.
(Izi zimachitika) kuti achichite chimene satana akuponya kukhala mayeso kwa omwe m’mitima mwawo muli matenda ndi ouma mitima yawo; ndithu osalungama ali m’kusiyana komwe kuli kutali (ndi choonadi).
Ndipo kuti adziwe amene apatsidwa kuzindikira kuti chimenechi n’choonadi chochokera kwa Mbuye wako ndi kuchikhulupirira ndikuti mitima yawo idzichepetse kwa Iye; ndithu Allah ndi Woongolera ku njira yolunjika amene akhulupirira.
Ndipo amene sadakhulupirire apitilira kukhala m’chikaiko ndi chimenecho (wadza nachocho) kufikira tsiku la chimaliziro liwadzera mowatutumutsa, kapena chiwadzera chilango pa tsiku lopanda chabwino (kwa iwo).
Ufumu tsiku limenelo ngwa Allah; adzaweruza (mwachilungamo) pakati pawo; choncho amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, adzakhala m’Minda yamtendere.
Ndipo amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake) ndikutsutsa Ayah Zathu, iwo adzapeza chilango choyalutsa.
Ndipo amene asamuka chifukwa cha chipembedzo cha Allah, kenako ndikuphedwa kapena kufa, ndithu Allah adzawapatsa (patsiku la chiweruziro) zopatsa zabwino. Ndithu Allah Ngwabwino popatsa kuposa opatsa.
Ndithu adzawalowetsa pamalo pomwe adzapayanja. Ndithu Allah Ngodziwa; Ngodekha.
Zimenezi zili chonchi, ndipo yemwe akubwezera kulanga molingana ndi momwe iye adalangidwira; kenakonso nkuchitidwa mtopola, ndithu Allah amthangata; Allah Ngofufuta uchimo; Wokhululuka kwambiri.
Zimenezo nchifukwa chakuti Allah amalowetsa usiku mu usana ndikulowetsa usana mu usiku, ndi chifukwanso chakuti ndithu Allah Ngwakumva Ngopenya.
Zimenezo nchifukwa chakuti Allah ndi Wowona (alipo;) ndipo zimene akuzipembedza kusiya Iye, nzachabe. Ndipo Allah Ngwapamwambamwamba Ngwamkulu.
Kodi suona kuti Allah amatsitsa madzi kuchokera ku mitambo, ndipo nthaka imakhala yobiriwira? Ndithu Allah Ngodziwa zobisika ndiponso Ngodziwa zoonekera.
Zakumwamba ndi zapansi zonse ndizake; ndithu Allah Ngwachikwanekwane; Wotamandidwa.
Kodi sudaone kuti Allah wakufewetserani zonse zam’nthaka ndi zombo zomwe zikuyenda panyanja mwa lamulo Lake? Ndipo wagwira thambo kuti lisagwe panthaka koma kupyolera m’chilolezo Chake; ndithu Allah Ngodekha kwa anthu Ngwachifundo.
Ndipo Iye ndi Amene adakupatsani moyo; kenako adzakupatsani imfa, ndipo kenako adzakuukitsani; ndithu munthu ngosathokoza.
Mpingo uliwonse tidauikira machitidwe amapemphero omwe akuwatsata; choncho asatsutsane nawe pachinthu ichi, ndipo itanira anthu ku chipembedzo cha Mbuye wako. Ndithu iwe uli pachiongoko changwilo.
Ndipo ngati atsutsana nawe, nena: “Allah Ngodziwa koposa zimene mukuchita.”
“Allah adzaweruza pakati panu tsiku la Qiyâma pa zimene mudali kusiyana.”
Kodi sudziwa kuti Allah akudziwa zakumwamba ndi zapansi? Ndithu zonsezo zili m’kaundula (Wake), ndithu (kudziwika kwa) zimenezo kwa Allah nzosavuta.
Ndipo akupembedza milungu yabodza, kusiya Allah, yomwe (Allah) sadaitumizire umboni wakuti (ipembedzedwe) yomwenso iwo sakuidziwa bwino. Ndipo anthu osalungama sadzakhala ndi owathandiza.
Koma Ayah Zathu zomveka zikawerengedwa kwa iwo, uona kunyansidwa pankhope za amene sadakhulupirire. Ndipo amakhala pafupi kuwamenya amene amawawerengera Ayah Zathu. Nena: “Kodi ndikuuzeni zoipa kwambiri kuposa izi? Ndi Moto (wa Allah) umene wawalonjeza amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake) amenewo ndi mabwelero oipa zedi.”
E inu anthu! Fanizo laperekedwa; choncho limvereni. Ndithu amene mukuwapembedza m’malo mwa Allah, sangathe kulenga ntchentche ngakhale Atasonkhana (kuti athandizane) pachimenechi. Ndipo ngati ntchenche itawalanda chinthu, sangathe kuchilanda kuntchentcheyo. Wafooka kwenikweni wopempha ndi wopemphedwa.
Sadamlemekeze Allah, kulemekeza komuyenera. Ndithu Allah Ngwamphamvu Ngogonjetsa chilichonse.
Allah amasankha atumiki mwa angelo ndi mwa anthu. Ndithu Allah Ngwakumva; Ngopenya.
Akudziwa zimene zili patsogolo pawo ndi zimene zili pambuyo pawo; kwa Allah Yekha ndiko kobwerera zinthu.
E inu amene mwakhulupirira! Weramani ndikugwetsa nkhope zanu pansi ndipo mpembedzeni Mbuye wanu ndikuchita zabwino kuti mupambane.
Ndipo menyerani chipembedzo cha Allah, kumenyera kwa choonadi; Iye ndi Amene adakusankhani (kuti mukhale mpingo wabwino;) ndipo sadaike pa inu zinthu zolemera pa chipembedzo, ndi chipembedzo cha tate wanu Ibrahim. Iye (Allah) adakutchani Asilamu kuyambira kale (m’mabuku akale) ndi mu iyi, (Qur’an) kuti Mtumiki akhale mboni pa inu, inunso kuti mukhale mboni pa anthu. Choncho pempherani Swala moyenera, perekani Zakaat ndipo gwirizanani chifukwa cha Allah. Iye ndiye Mbuye wanu, Mbuye wabwino zedi, ndi Mthandizi wabwino zedi.