Surah Taha

Surah Taha - Chewa Aya count 135

Tâ-Hâ [271]
Koma kuti ikhale ulaliki ndi chikumbutso kwa yemwe akuopa (ndikudzichepetsa kwa Allah).
(Iye ndi Allah), Wachifundo Chambiri; pa Arsh (Mpando wachifumu) adakhazikika, (kukhazikika koyenerana ndi ulemelero Wake kopanda kukufanizira ndi kukhazikika kwa chilichonse; pakuti Iye salingana ndi chilichonse pa chikhalidwe ndi mbiri Zake).
Ndipo ngati ulankhula mokweza mawu, (iwe munthu), ndithu Iye akudziwa zobisika ndi zobisika kwambiri (zomwe mwazibisa mu mtima mwanu).[272]
Allah! Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Iye ali ndi maina abwino (ndi mbiri zabwinonso).
Ndipo kodi yakufika nkhani ya Mûsa? (Yomwe njododometsa)?[273]
Koma pamene adaudzera motowo Anaitanidwa (kuti), “E, iwe Mûsa!
Ndipo Ine ndakusankha (kuti ukhale Mtumiki); choncho mvera zonse zomwe zikuvumbulutsidwa (kwa iwe).
Ndithu nthawi ya tsiku lachimaliziro idza; (choncho ikonzekere ndi ntchito zabwino); ndikuibisa dala (kwa anthu) kuti mzimu uliwonse udzalipidwe zimene udachita.[274]
Ndipo asakutsekereze (ku khulupirira) zimenezo yemwe saikhulupirira (Kiyamayo), ndipo akungotsata zilakolako za mtima wake; kuopa kuti Ungadzaonongeke.”
“Kodi nchiyani icho chili kudzanja Lako ladzanjadzanja, iwe Mûsa?”
(Mûsa) adati: “Iyi ndi ndodo yanga, ndimaitsamira (poyenda) ndi kuphopholera masamba a mbuzi zanga; ndiponso (m’ndodomo) muli zina zondithandiza.”[275]
Ndipo adaiponya; pompo idasanduka njoka yoyenda mothamanga. [276]
“Ndipo lipane dzanja lako m’khwapa mwako lituluka lili loyera (ngati kuwala kwadzuwa ndi mwezi). Osati mwamatenda, (ichi chikhala) chozizwitsa china.”[277]
“Kuti tikusonyeze zina mwa zozizwitsa zathu, zazikuluzikulu.”
(Mûsa) adati: “E Mbuye wanga! Nditsakulireni chifuwa changa.”
“Ndi kundifewetsera ntchito yangayi (imene mwandipatsa kuti uthengawu ndikaufalitse m’njira yoyenera).”
“Ndipo masulani mfundo yomwe ili ku lirime kwanga, (ndimasulireni kumangika kwa lirime langa kuti mawu anga akakhale opanda chibwibwi).”[278]
“Kuti (anthu) akamvetse mawu anga.”
“Ndipo ndipatseni nduna (mthandizi) yochokera kubanja langa.”
“M’bale wanga Harun.”
“Limbitsani nyonga zanga ndi iye.”
“Ndipo mphatikeni ku ntchito yangayi.”
“Ndithu inu (nthawi zonse) mumationa (ndi kutisunga).”
(Allah) adati: “Ndithu wapatsidwa zomwe wapempha, E, iwe Mûsa.”
“Ndipo ndithu tidakuchitira ubwino nthawi ina (popanda iwe kutipempha).”
“Pamene mayi wako tidamuzindikiritsa zimene tidamzindikiritsa (kuti azichite).”
(Kuti): “Mponye (mwanayo) m’bokosi ndipo ponya bokosilo mu mtsinje; ndipo mtsinje umponya m’mbali kuti amtenge mdani wanga ndi mdani wake (ndi kuti aleredwe mwaubwino ndi Farawo); ndipo ndidaika kukondeka pa iwe kochokera kwa Ine (kuti ukhale wokondedwa ndi anthu onse) ndikuti uleredwe moyang’aniridwa ndi Ine.”
(Kumbuka) pomwe mlongo wako ankayenda (kunka kubanja la Farawo) Ndipo adati: “Kodi ndikulondolereni munthu amene angathe kumlera?” Ndipo tidakubwezera kwa mayi wako kuti maso ake atonthole, ndipo asadandaule. Ndipo kenaka udapha munthu (mwangozi), ndipo tidakupulumutsa ku madandaulo; tidakuyesa ndi mayeso ambiri. Udakhala zaka zambiri ndi anthu a ku Madiyan. Kenaka wabwera (apa) monga mwachikonzero, E, iwe Mûsa![279]
Ndipo ndakusankha ndekha (kuti ukhale Mtumiki Wanga).
Pita iwe ndi m’bale wako ndi zozizwitsa Zanga, ndipo musatope (musasiye) kundikumbukira.
(Iwo) adati: “Mbuye wathu ndithu ife tikuopa kuti angatimbwandire kapena kutipyolera malire (tisananene kanthu).”
(Allah) adati: “Musaope. Ndithu Ine ndili nanu pamodzi. ndikumva, ndiponso ndikuona.”
Choncho mpitireni, ndikumuuza (kuti): “Ndithu ife ndife atumiki a Mbuye wako. Asiye ana a Israyeli achoke ndi ife, ndipo usawazunze; ndithu takudzera ndi chozizwitsa chochokera kwa Mbuye wako (chomwe ndi mboni yathu pa zomwe tikukuuzazi), ndipo mtendere ukhala pa yemwe atsate chiwongoko.”
“Ndithu zavumbulutsidwa kwa ife kuti chilango chiwapeza amene akutsutsa (zimenezi) ndikuzitembenukira kumbali.”
(Farawo) adati: “Kodi Mbuye wanu ndani, iwe Mûsa?”
(Mûsa) adati: “Mbuye wathu ndi yemwe adapatsa chinthu chilichonse chilengedwe chake, kenako adachiongolera (kutsata chimene chikulingana ndi chilengedwe chake).”
(Farawo) adati: “Nanga mibadwo yakale ili bwanji, (imene idapita iwe usadadze?”)
(Mûsa) adati: “Kudziwa kwa zimenezo nkwa Mbuye wanga, m’kaundula (Wake momwe mwasonkhanitsidwa chilichonse), Mbuye wanga sasokera, ndipo saiwala.
Kuchokera (m’nthaka) umu tidakulengani, ndipo momwemo tidzakubwezani, ndipo kuchokera m’menemo tidzakutulutsani nthawi ina (muli moyo).
Ndipo, ndithu tidamuonetsa (Farawo) zozizwitsa zathu zonse, koma adatsutsa ndipo adakana.
Choncho nafe tikubweretsera matsenga onga amenewo! Choncho ika lonjezo (la msonkhano) pakati pathu ndi iwe; lonjezo lomwe tisaliswe ife ndi iwe, (tidzakumane) pamalo poyenera.”
(Mûsa) adati: “Lonjezo lanu likhale pa tsiku lodzikongoletsa (tsiku la chikondwelero), ndipo anthu adzasonkhanitsidwe m’mawa.”
Ndipo Farawo adabwerera ndikusonkhanitsa matsenga ake, ndipo kenako adabwera (ndi amatsenga ake pa tsiku la chipanganolo).[280]
Choncho (amatsengawo) adakangana pakati pawo pa zinthu zawo ndipo adakambirana mwachinsinsi.
(Iwo) adati (mkunong’onezana kwawo): “Ndithu anthu awiriwa ndi amatsenga; kupyolera mmatsenga awo akufuna kukutulutsani m’dziko mwanu, ndikuchotsa chikhalidwe chanu chomwe chili chabwino.”
“Choncho sonkhanitsani matsenga anu (onse), kenako mudze (kwa iwo) mutandanda pamzere; ndithu lero, apambana amene akhale wapamwamba.”
(Iwo) adati: “E iwe Mûsa! Kodi ukhale ndiwe woyamba kuponya (matsenga ako), kapena tikhale oyamba ndife kuponya?”
(Mûsa) adati: “Koma inu ndinu muponye!” (Choncho adaponya matsengawo). Mwadzidzidzi zingwe zawo ndi ndodo zawo zamatsenga awo, zimaoneka pamaso pake (Mûsa) kuti zikuyenda mothamanga.
Tidati: “Usaope (zomwe ukuzionazi), ndithu iwe ukhala wopambana.”
“Ndipo ponya chimene chili kudzanja lako ladzanjadzanja (ndodo); chimeza zomwe apanga; ndithu iwo apanga matsenga a mfiti ndipo mfiti siingapambane paliponse pamene yadza.”[281]
(Farawo) adanena: “Ha! Mwamkhulupirira ndisadakupatseni chilolezo? Ndithu iye ndi mkulu wanu amene adakuphunzitsani matsenga! Choncho ndikudulani manja anu ndi miyendo yanu, mosemphanitsa:; (dzanja lakudzanjadzanja ndi mwendo wakumanzere. Pomwe wina, mkono wakumanzere ndi mwendo wakudzanjadzanja), ndipo kenako ndikupachikani pa mathunthu a mitengo ya kanjeza; ndithu mudziwa (panthawiyo) kuti ndani mwa ife, (ine kapena Mulungu wa Mûsa), wachilango chaukali ndi chopitilira.”[282]
(Amatsenga) adati: “Sitisankha iwe kusiya zomwe zatidzera; zisonyezo zachoonadi zoonekera poyera! Ndipo tikumlumbilira Yemwe adatilenga, (sitikusankha iwe), chita zomwe ufuna kuchita; ndithu iwe utha kupititsa chiweruzo chokhudzana ndi moyo uno wapansi, basi.”
Ndithu amene adzadze kwa Mbuye wake uku ali wamachimo, adzapeza moto wa Jahannam; sadzafa m’menemo, ndipo sadzakhalanso ndi moyo wabwino.
Minda yamuyaya, yomwe pansi pake (ndi patsogolo pake) pakuyenda mitsinje. Adzakhala mmenemo nthawi yaitali. Ndipo zimenezo ndi mphoto za yemwe wadziyeretsa.
Ndipo ndithu Mûsa tidamtumizira chivumbulutso, (tidamzindikiritsa kuti): “Yenda usiku ndi akapolo Anga (kutuluka m’dziko la Iguputo,) ndipo ukawapangire panyanja njira youma, ndipo usaope kukupeza adani ndiponso usaope (kumira).”
E inu ana a Israyeli! Ndithu tidakupulumutsani kwa mdani wanu, ndipo tidakulonjezani (kuti mudze) mbali yakudzanjadzanja ya phiri (kuti tikupatseni malamulo ndi zina), ndipo tidakutsitsirani Manna ndi Saluwa.
Ndipo ndithu Ine ndi Wokhululuka kwambiri kwa amene walapa ndi kukhulupirira, ndikuchita ntchito zabwino, kenako ndikutsata chiongoko mwaubwino.
“Nchiyani chakufulumizitsa (kudza kuno) kusiya anthu ako, E, iwe Mûsa?”[283]
Adati: “Iwo ali pambuyo panga akunditsata. Ndachita changu kudza kwa Inu, Mbuye wanga, kuti mundiyanje kwambiri.”
(Iwo) adati: “Sitidaswe lonjezo lako mwachifuniro chathu; koma tidasenzetsedwa mitolo ya zodzikometsera za anthu (ziwiya zagolide zomwe tidabwereka kwa akazi a chimisiri), ndipo tidaziponya (pa moto, ndipo zidasungunuka ndikupangidwa mwana wang’ombe.) Ndipo momwemonso Samiriyyu adaponya.”
Ndipo adawatulutsira (kuchokera m’golide wosungunukayo) mwana wang’ombe wokhala ndi thupi lokwanira, yemwe amatulutsa mawu (ngati kulira kwa ng’ombe), (iwo) adati: “Uyu ndi mulungu wanu ndiponso mulungu wa Mûsa, koma (Mûsa) wamuiwala, (choncho wapita kukamfuna ku phiri)!”
Ndipo ndithu Harun adawauza kale (kuti): “E inu anthu anga! Ndithu inu mwasokonezeka ndi (chinthu) ichi. Ndithu Mbuye wanu ndi (Allah) Wachifundo chambiri; choncho nditsateni, ndipo mverani lamulo langa, (siyani kupembedza fano ili).”
(Pamene Mûsa adabwerera) adati: “E iwe Harun! Nchiyani chidakuletsa pamene udawaona atasokera,”
(Harun) adati: E iwe mwana wa mayi anga! Usagwire ndevu zanga, ngakhale mutu wanga (poukoka chifukwa cha mkwiyo). Ndithu ine ndidaopa (kuchoka ndi ena, kusiya ena) kuti ungati: “Wawagawa ana a Israyeli, ndipo sudayembekezere mawu anga.”
(Mûsa) adati: “E iwe Samiriyyu! Nchiyani wachita?”
(Iye adati:) “Ndidaona zomwe sadazione (ena) ndipo ndidatapa pang’ono mapazi a Mtumiki (Gabriele) ndikuwaponya (mu fano la mwana wa ng’ombe). Ndipo zimenezi ndi zomwe zidakomera mtima wanga.”[285]
(Mûsa) adati: “ Choka, ndithu pa iwe (pali chilango) pa moyo (wako) choti uzingonena (kuti): “Musandikhudze musandikhudze.” (Ndipo palibe amene adzakuyandikira ndipo iwe sudzayandikira aliyense). Ndithu pa iwe pali lonjezo la (Allah) losaswedwa; ndipo muyang’ane mulungu wako, yemwe wakhala ukupitiriza kumpembedza. Timtentha, kenako chipala chakecho tichimwaza m’nyanja.
Ndithu wompembedza wanu, ndi Allah Yekha, Yemwe, palibe woti nkupembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Ndipo wakwanira pa chilichonse kuchidziwa ndi nzeru (Zake zopanda malire).
Umo ndi momwe tikukusimbira nkhani za (zinthu) zomwe zidatsogola (za aneneri). Ndithu takupatsa uthenga waukulu kuchokera kwa Ife (omwe ndi Qur’an).
Adzakhala m’menemo m’chilango. Ndipo ndi zoipa zedi (kwa anthu) kusenza mitolo (imeneyo) tsiku la Qiyâma,
(Kumbuka Mtumiki Muhammad {s.a.w}), tsiku lomwe lipenga lidzaimbidwa. Ndipo tidzasonkhanitsa oipa tsiku limenelo maso awo ali a buluu (blue, chifukwa cha mantha).
Adzanong’onezana pakati pawo (ponena kuti): “Simudakhalitse pa dziko lapansi koma masiku khumi okha basi.”
Ife tikudziwa kwambiri zimene azidzanena pamene abwino awo pamayendedwe azidzanena: “Inu simudakhale koma tsiku limodzi basi (poyerekeza ndi kuchuluka kwa masiku a ku Moto).”
Ndipo akukufunsa zamapiri (kuti adzatani tsiku la Qiyâma); auze: “Mbuye wanga adzawagumulagumula ndikuwaululutsa (ngati fumbi).”
“Ndipo adzaisiya (nthaka yonse) ngati bwalo losalazidwa myaa!”
“Sudzaona kukhota m’menemo ngakhale chitunda (chikweza).”
Tsiku limenelo adzamtsatira woitana; sadzatha kumpatuka, ndipo mawu (azolengedwa) adzatonthola (kuti chete) kwa (Allah) Wachifundo chambiri; ndipo sudzamva, koma kunong’ona basi (ndi mididi ya mapazi).
Tsiku limenelo chiombolo (cha aliyense) sichidzathandiza, kupatula yemwe wapatsidwa chilolezo ndi (Allah) Wachifundo chambiri, ndi kumuyanja kuti alankhule.
Ndipo nkhope (tsiku limenelo) zidzalobodoka pamaso pa (Allah) Wamoyo wamuyaya, Wochita chilichonse. Ndithu adzataika kwathunthu yense wochita zosalungama.
Ndipo momwemo taivumbulutsa (Qur’an) m’Chiarabu ndipo tafotokoza m’menemo mwatsatanetsatane za machenjezo (amtundu uliwonse), kuti aope (Allah), ndikuti nthawi iliyonse (Qur’aniyo), iwapatse chikumbutso chatsopano.
Chomwecho watukuka Allah, Mfumu ya choonadi, ndipo usaifulumizitse Qur’an (powerenga) chivumbulutso chake chisanamalizike kwa iwe, ndipo nena (popempha) kuti: “Mbuye wanga! Ndionjezereni nzeru (kuzindikira).”
Ndipo tidamulangiza (Mneneri) Adam kale, koma adaiwala. Ndipo sitidapeze Mwa iye kulimba mtima (potsatira lamulo Lathu loti asadye zipatso za mtengo woletsedwa).
Ndipo (kumbukirani) pamene tidauza angelo: “Muchitireni sajida (mugwadireni momulemekeza) Adam,” dipo adachita Sajida kupatula Iblis, adakana.
“Ndipo iwe sumva ludzu m’menemo, ndiponso sumva kutentha (kwa dzuwa).”
(Allah) adati: “Chokani nonsenu m’menemo, uku pali chidani pakati pa wina ndi mnzake, (padzakhala chidani pakati pa ana anu); koma chikadzakudzerani chiongoko kuchokera kwa Ine, tero amene adzachitsate chiongoko changacho, sadzasokera ndiponso sadzavutika.”
Ndipo amene anyozere ulaliki wanga, ndithu moyo wamavuto udzakhala pa iye ndipo tidzamuukitsa m’manda tsiku la chimaliziro ali wakhungu.”
Adzanena: “Mbuye wanga! Chifukwa ninji mwandiukitsa ndili wakhungu, pomwe ndidali wopenya?”
(Allah) adzanena: “Zimenezo nchifukwa chakuti zidakudzera Ayah zathu koma udaziiwala (chifukwa chosalabadira), momwemo lero uiwalidwa, (salabadilidwa).”
Ndipo umo ndimomwe tidzamulipirire aliyense wopyola malire, wosakhulupirira Ayah za Mbuye wake. Ndipo chilango cha tsiku la chimaliziro nchaukali, ndiponso chamuyaya.
Kodi sizidadziwikebe kwa iwo kuti ndi mibadwo ingati tidaiononga patsogolo pawo? Ndipo awa (osakhulupirira atsopano) akuyenda m’malo awo, (kodi saona zizindikiro zakuonongeka kwawo)? Ndithu m’zimenezo muli zisonyezo kwa eni nzeru.
Ndipo pakadapanda liwu lomwe lidatsogola kuchokera kwa Mbuye wako (lochedwetsera chilango) ndi nthawi yomwe idaikidwa, ndithu (chilango) chikadawafika (tsopano lomwe lino.)
Choncho pirira pa zomwe akunenazo, ndipo lemekeza Mbuye wako ndi kumtamanda, dzuwa lisanatuluke (popemphera swala ya Fajr), ndiponso lisanalowe (popemphera swala ya Asr); ndiponso nthawi za usiku umulemekeze (popemphera swala ya Magrib ndi Isha), ndi pansonga za masana (pakatikati pa usana popemphera swala ya Dhuhr); kuti udzakhale wokondwa (ndi malipilo amene azakupatse tsiku la Qiyâma).
Ndipo usazitong’olere maso ako (mozidololokera zinthu) zimene tawasangalatsa nazo ena mwa anthu pakati pawo; zimenezo nzokongoletsa za moyo wa pa dziko basi, kuti tiwayese mayeso pazimenezo; koma chopatsa cha Mbuye wako (chomwe nchololedwa ngakhale chikhale chochepa) nchabwino kwambiri ndiponso chokhalitsa.
Ndipo lamula banja lako kupemphera Swala ndi kuipirira iwe mwini Swalayo. Sitikukupempha rizq, (chakudya) koma Ife ndi amene tikukudyetsa ndipo malekezero abwino ali mukuopa (Allah).
Ndipo (osakhulupirira) adanena: “Chifukwa ninji sakutibweretsera chizizwa kuchokera kwa Mbuye wake?” Kodi sudawafike umboni woonekera wa zomwe zili m’mabuku akale? (Kodi sadakhutitsidwe ndi Qur’an chomwe ndi chizizwa chachikulu).”
Nena: “Aliyense (wa ife) akuyembekezera (mphoto yake); choncho yembekezerani. Posachedwapa mudziwa kuti kodi ndani mwini njira yolingana, ndipo ndani amene waongoka.”
Share