Surah Al-Kahf ( The Cave )

Surah Al-Kahf ( The Cave ) - Chewa Aya count 110

Kutamandidwa konse kwabwino nkwa Allah, Yemwe adavumbulutsa kwa kapolo Wake (Mtumiki Muhammad{s.a.w}), buku (ili lopatulika), ndipo sadalikhotetse (koma m’menemo muli zoona zokhazokha.)
Adzakhalamo (mumtendere wosathawo) muyaya.
Ndithu Ife tazichita zomwe zili pamwamba pa nthaka kukhala zokometsera nthakayo, ndikuti (mwa izo) tiwayese mayeso kuti (ndani) mwa iwo ali wochita zabwino kwambiri.
Ndipo ndithu Ife ndi Amene tidzazichita zomwe zili pamenepo kukhala monga nthaka yoguga (yopanda mmera).
Kodi ukuganiza kuti eni phanga ndi eni nkhani zomwe zidalembedwa m’mabuku, adali mwa zizindikiro zathu zododometsa kwambiri? (Iyayi, zilipo zododometsa kwabasi kuposa zimenezo.)
Tidagonthetsa makutu awo, (ndikugona kosamva nako kanthu) kwa zaka zambirimbiri m’phanga.
Kenako tidawautsa, kuti tiwayese (kuti) ndani mwa magulu awiriwa amadziwa kuwerengera nthawi imene (anyamatawa) adakhala (m’phangamo).
Ife tikusimbira (iwe mtumiki{s.a.w}) nkhani zawo mwachoonadi; ndithu iwo adali anyamata amene adakhulupirira Mbuye wawo, ndipo tidawaonjezera chiongoko.
Ndipo tidalimbikitsa mitima yawo pa chikhulupiliro pamene adaimilira (pamaso pa mfumu yawo yosakhulupirira) ndikunena: “Mbuye wathu ndi Mbuye wa thambo ndi nthaka. Sitipembedza mulungu wina m’malo mwa Iye. Ngati titatero ndiye kuti tanena zoipa zopyola muyeso.
(Zidali tere) ukadakhala ukuliona dzuwa pamene linkatuluka (ndikuyamba kukwera), ukadaliona likulambalala kumbali kwa phanga lawo mbali yakudzanjadzanja, ndipo pamene linkalowa limawadutsa mbali yakumanzere (popanda kuwalunjika) pomwe iwo adali pamtetete mmenemo. Zimenezo ndi zina mwa zisonyezo za Allah (zosonyeza kukhoza Kwake). Amene Allah wamuongola iyeyo ndiye woongoka; ndipo amene wamulekelera kuti asokere, simungampezere mtetezi kapena muongoli.
Ndipo momwemonso tidawautsa kuti afunsane pakati pawo (zanthawi imene akhala ali chigonere). Adanena wonena mwa iwo: “Kodi mwakhala nthawi yotani muli mtulo?” Adati: “Takhala tsiku limodzi kapena gawo la tsiku.” (Ena) adati: “Mbuye wanu akudziwa kwambiri za nyengo imene mwakhala. Choncho mtumeni mmodzi wa inu ndindalama zanuzi za siliva kumudzi ndipo akayang’ane chakudya chake nchotani chomwe chili choyera bwino, ndikubwerera nacho chakudyacho; koma izi akachite mochenjera ndipo asamzindikiritse aliyense za inu.”[257]
“Ndithu iwo akakudziwani (pamene mulipa), akugendani ndi miyala; apo ai akubwezerani ku chipeinbedzo chawo (chopotoka), zikatero ndiye kuti simudzapambananso mpaka kalekale.”
(Koma anthu anazindikira pamene adaona ndalama yakale), momwemonso tidawazindikiritsa (kwa anthu) kuti adziwe kuti lonjezo la Allah (loukitsa ku imfa zolengedwa) nloona, ndikuti nthawi ya chimaliziro njosakaikitsa, (ndipo kumbukani) pamene adakangana pakati pawo pa chinthu chaochi, ena adati: “Mangani chomanga pa iwo (kuti anthu asamadze kudzawasuzumira), Mbuye wawo za iwo akudziwa bwino, koma amene adapambana paganizo lawolo adanena: “Ndithu ife timanga Msikiti wa iwowa (pa phanga lawoli).”
(Ena) akhala akunena (kuti) adali anthu atatu, wachinayi ndi galu wawo; ndipo (ena) akuti adali asanu, wachisanu ndichimodzi ndigalu wawo. (Akunena) mwakungoganizira chabe zomwe sakuzidziwa; ndipo (ena) akuti adali asanu ndi awiri, ndipo wachisanu ndi chitatu ndi galu wawo. Nena: “Mbuye wanga ndiye akudziwa bwinobwino za chiwerengero chawo. Palibe amene akudziwa (za iwo) koma ndi ochepa chabe.” Choncho usatsutsane nawo za iwo, kupatula kutsutsana kwa pa zinthu zodziwika, ndipo usamfunse aliyense mwa iwo za iwo.
“Koma (utsogoze liwu lakuti): Insha Allah, (Allah akafuna!)” Ndipo mukumbuke Mbuye wako ukaiwala ponena kuti: “Mwina Mbuye wanga anditsogolera pa njira yapafupi pachiongoko kuposa iyi.”[258]
Ndipo adakhala m’phanga lawolo (ali mtulo) zaka zikwi zitatu (300) ndikuonjezera zisanu ndi zinayi (9).
Nena: “Allah akudziwa bwinobwino nyengo imene (iwo) adakhala; zobisika za kumwamba ndi za pansi nza Iye (Allah basi); taona Allah kuonetsetsa! Taona Allah kumvetsetsa! (Allah Ngoona chilichonse, ndipo Ngwakumva chilichonse). Ndipo iwo alibe mtetezi popanda Iye (Allah); ndipo Iye sagawira aliyense udindo Wake wakulamula.
Ndipo werenga zomwe zavumbulutsidwa kwa iwe za m’buku la Mbuye wako, palibe amene angathe kusintha mau Ake, ndipo nawe sungapeze potsamira ndi pothawira (kuti Allah asakupeze.)
Ndipo dzikakamize kukhala pamodzi ndi amene akupempha Mbuye wawo m’mawa ndi madzulo uku akufunafuna nkhope Yake (chiyanjo Chake), ndipo maso ako asachoke pa iwo ndi (kuyang’ana ena) ncholinga chofuna zokongoletsa za moyo wa dziko lapansi; ndipo usamumvere amene mtima wake tauiwalitsa kutikumbukira ndikumangotsatira zilakolako zake, ndipo zinthu zake nkukhala zotaika (zosalongosoka).[259]
Ndipo nena (kwa osakhulupirirawo, kuti): “Ichi ndi choonadi chimene chachokera kwa Mbuye wanu.” Choncho amene afuna, akhulupirire; ndipo amene afuna (kusachikhulupirira) asakhulupirire. Ndithu achinyengo tawakonzera Moto, womwe mipanda yake ikawazinga. Ndipo akakapempha chithandizo (chifukwa cha ludzu loopsya lomwe likawapeza), akathandizidwa popatsidwa madzi (otentha kwambiri) monga madzi a chitsulo chosungunuka, omwe adzasupula nkhope zawo. Taona kuipa chakumwa! ndi kuipa malo wotsamira!
Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita ntchito zabwino, (tidzawalipira pa ubwino wawowo), ndithu Ife sitisokoneza malipiro a amene wagwira ntchito yabwino.
Ndipo iye adali ndi chuma (china) nati kwa mnzakeyo mokambirana naye: “Ine ndili ndi chuma chambiri kuposa iwe, (ndilinso) ndi mphamvu zambiri chifukwa cha onditsatira (omwe ndili nawo).”
Ndipo adalowa m’munda mwake uku akudzichitira yekha zoipa. Adati: “Sindiganiza ngakhale mpang’ono pomwe kuti (munda) uwu udzaonongeka.”
“Ndiponso sindiganiza kuti Qiyâma (chimaliziro) idzachitikadi. Ngati (itapezekadi Kiyamayo), ine nkubwezedwa kwa Mbuye wanga, ndithu ndikapeza malo abwino wobwererako kuposa awa. (Monga momwe ndapezera mwayi kuno, ukonso ndikapeza, ngati Kiyamayo ilikodi).”
“Koma ine ndikukhulupirira kuti Iye ndi Mulungu Mbuye wanga, ndipo sindiphatikiza aliyense ndi Mbuye wanga.”
“Ndipo pamene umalowa m’munda wako ukadanena kuti izi ndi zimene wandifunira Allah, mphamvu sizikadapezeka koma kupyolera mwa Allah (zikadakhala zabwino kwa iwe). Ngati ukundiona ine kuti ndili ndi chuma chochepa ndi ana ochepa kuposa iwe (koma sindisiya kutamanda Allah).”
Tsono mliri unagwa pa zipatso zakezo (ndikuziononga motheratu), ndipo adayamba kutembenuza manja modandaulira zomwe adaonongera m’menemo; (mindayo) mitengo yake itagwera pansi. Ndipo adati: “Kalanga ine! Ndikadapanda kumphatikiza Mbuye wanga ndi aliyense (zoterezi sizikadachitika.)”
Pamalo potere chitetezo chimakhala cha Allah Yekha Woona. Iye Ngolipira bwino, ndiponso Wabwino (pakudza) ndi malekezero abwino.
Ndipo apatse fanizo la moyo wadziko lapansi, uli ngati madzi amene tikutsitsa kuchokera kumitambo kenako (madziwo) amasakanikirana ndi mmera wa m’nthaka (ndikuyamba kumera mokongola), kenako (mmerawo) nkukhala masamba ouma odukaduka omwe mphepo ikuwaulutsa uku ndi uku. Ndipo Allah ali ndi mphamvu pachilichonse.
Ndipo (akumbutse) tsiku lomwe tidzayendetsa mapiri (powaulutsa ngati ubweya mu mlengalenga), ndipo udzaiona nthaka ili tetetee, (itatambasuka yosakhwinyata ndi mapiri kapena zitunda), ndipo tidzawasonkhanitsa (tsiku limenelo), ndipo sitidzasiya aliyense mwa iwo (oyamba ndi omaliza).
Ndipo adzabwera nawo kwa Mbuye wako atandanda m’mizere (ndikuuzidwa): “Ndithu mwatidzera monga tidakulengerani pachiyambi (opanda nsapato, amaliseche ndiponso opanda chilichonse chuma ndi ana). Koma mumaganiza kuti sitikuikirani lonjezo (ili louka ku imfa ndi kuweruzidwa).”
Ndipo kaundula adzaikidwa (pamaso pawo), ndipo udzaaona oipa ali oopa chifukwa cha zomwe zili m’menemo, ndipo adzanena: “Kalanga ife taonongeka! Ngotani kaundula uyu, sasiya chaching’ono ngakhale chachikulu, koma zonse kuzilemba.” Ndipo adzapeza zonse zimene adazichita zitalembedwa m’menemo. Ndipo Mbuye wako sapondereza aliyense (pomusenzetsa zomwe sizake, kapena kumchitira zomwe sizikumuyenera).
Ndipo (kumbuka) pamene tidawauza angelo: “Mchitireni sijida Adam (mugwadireni momulemekeza).” Onse adachitadi sijida kupatula Iblis. Iye adali mmodzi wa ziwanda, ndipo adatuluka m’chilamulo cha Mbuye wake. Kodi iye ndi mbumba yake mukuwalola kukhala abwenzi (anu) kusiya Ine, pomwe iwo ndiadani anu? Taonani kuipa kusintha kwa anthu oipa!
Ndipo (kumbukani) tsiku lomwe (Allah) adzanena: “Aitaneni aja omwe munkandiphatikiza nawo omwe munkati (ndi milungu inzanga).” Choncho, adzaiitana koma siidzawayankha; ndipo tidzaika chionongeko pakati pawo (ndipo sadzakumananso).
Ndipo palibe chimene chaletsa anthu kukhulupirira (tsopano) pamene chiongoko choonadi chawadzera ndikupempha chikhululuko kwa Mbuye wawo, koma akuyembekezera kuti chiwadzere chikhalidwe cha anthu oyamba, kapena chiwadzere chilango masomphenya.
Ndiponso sitituma atumiki (ndi cholinga choti adzetse chilango), koma kuti akhale onena nkhani zabwino ndi ochenjeza. Ndipo amene sadakhulupirire, akuchita makani ndi chabodza kuti kupyolera m’chabodzacho achotse choonadi, ndipo Ayah Zanga ndi zomwe achenjezedwa nazo, akuzichitira chipongwe!
Ndindani woipitsitsa kwabasi woposa yemwe akukumbutsidwa ndi Ayah za Mbuye wake, koma iye nkuzinyoza, ndipo nkuiwala (zoipa) zimene manja ake adatsogoza? Ndithu Ife taika m’mitima mwawo zitsekelero kuti asazizindikire. Ndiponso m’makutu mwawo mwalemedwa ndi ugonthi. Ndipo ukawaitanira kuchiongoko (choonadi), salola kuongoka ngakhale pang’ono.
Ndipo Mbuye wako Ngokhululuka kwambiri mwini chifundo. Ndipo akadawathira m’dzanja pa zoipa zomwe akhala akuchita, ndiye kuti ndithu akadawapatsa chilango mwachangu; koma iwo ali nalo lonjezo ndipo sadzapeza pothawira paliponse ndikulipewa.
Ndipo imeneyo ndi midzi tidawaononga (okhalamo) pamene adadzichitira zoipa; ndipo tidawaikira lonjezo la nthawi yoikidwa la kuonongeka kwawo.
Ndipo (kumbukani) pamene Mûsa adanena kwa mnyamata wake (Yusha’ Ibn Nun): “Ndipitiriza kuyenda kufikira ndikafike pamajiga pa nyanja ziwiri, kapena ndizingoyenda zaka ndi zaka (kufikira nditakumana naye amene ndikumfunayo).”
Choncho pamene adafika pamajiga (pa nyanja ziwirizo) adaiwala nsomba yawo yomwe idatenga njira yake kunka m’nyanja ngati una (Mûsa adaiwala kumfunsa mnyamata wake za nsombayo; naye mnyamata adaiwala kumfotokozera Mûsa zomwe zidachitika ndi nsoinbayo).
Pamene adapita patsogolo, adauza mnyamata wake, (kuti): “Tipatseni chakudya chathu chammawa; ndithu pa ulendo wathuwu takumana ndi zotopetsa.”
(Mnyamata) adati: “Kodi mwaona pamene tidapumula paja, pathanthwe ndipomwe ndidaiwala (kuti ndikuuzeni) za nsombayo ndipo palibe wandiiwalitsa koma satana basi, kuti ndisaikumbukire. Iyo idatenga njira yake kunka m’nyanja, mododometsa.”
(Mûsa) adati : “Pamenepo ndi pomwe timafuna.” Choncho adabwerera m’mbuyo potsatira njira yawo (yomweyo).
Ndipo adampeza kapolo (Khidwiri) yemwe ndi m’modzi wa akapolo athu amene tidampatsa chifundo chochokera kwa Ife, (yemwenso) tidamphunzitsa maphunziro ambiri kuchokera kwa Ife.
Adati: “Ndithu iwe siutha kupirira nane! (Uwona zomwe sungathe kupirira nazo).”
Choncho onse awiri adanyamuka kufikira pamene adakakwera m’chombo adachiboola. (Mûsa) adati: “Kodi wachiboola kuti uwamize ali m’menemo? Ndithu wachita chinthu chachikulu choipa.”[260]
(Mûsa) adati: “Usandidzudzule chifukwa chakuiwala kwanga, ndipo usandipatse zovuta kwambiri pa khumbo langali (lofuna kukutsata).”
Ndipo adanyamuka; mpaka pomwe adakumana ndi mnyamata wochepa, ndipo (mneneri Khidir) adamupha. Mûsa adati: “Ha! Wapha munthu wopanda cholakwa, pomwe sadaphe munthu mnzake? Ndithu wachita chinthu choipitsitsa.”
(Mûsa) adati: “Ngati ndikufunsanso chilichonse pambuyo pa ichi, usandilole kutsagana nawe. Ndiye kuti wakwaniritsa dandaulo lako pa ine.”
Choncho adamuka; kufikira pamene adawapeza eni mudzi ndipo adawapempha eni mudziwo chakudya, koma adakana kuwalandira monga alendo. Ndipo adapezamo khoma lili pafupi kugwa, (ndipo Khidhiriyo) adaliimika. (Mûsa) adati: “Ngati ukadafuna, ukadalandira malipiro (pa ntchitoyi kuti tigulire chakudya).”
“Ndipo mnyamata uja, makolo ake adali okhulupirira, ndipo tidaopera kuti angawachititse zoipa (makolo akewo) ndi za kusakhulupirira (mwa Allah).
Choncho tidafuna kuti Mbuye wawo awasinthire ndi wabwino kuposa iye pa kuyera, ndi wachifundo chapafupi (kwa makolo ake.)”
“Tsopano chipupa chija, chidali cha ana awiri amasiye mu mzindamo; ndipo pansi pake padali chuma chawo (chimene adawasiira bambo wawo) ndipo tate wawo adali munthu wabwino choncho Mbuye wako adafuna kuti akule misinkhu yawo ndipo adzadzitulutsire chuma chawocho; ichi ndi chifundo chochokera kwa Mbuye wako. Ndipo ine sindidachite zinthu zimenezi mwandekha. Limenelo ndilo tanthauzo la zomwe sudathe kupirira nazo.”[262]
(Iye) adati: “Zomwe Mbuye wanga wandipatsa ndi zabwino. Choncho ndithandizeni ndi mphamvu zanu (zonse pantchito imeneyi) ndiika chotchinga cholimba pakati panu ndi pakati pawo.”
“Ndipatseni zidutswa za zitsulo.” Kufikira pamene adadzaza ndi zitsulozo mpata umene udalipo pakati pa mapiri awiriwo, adati: “Pemelerani (moto).” Mpaka (chitsulocho) chidafiira monga moto, adati: “Ndibweretsereni mtovu wosungunuka ndiuthire pamwamba pake (pa chitsulocho).”
(Iye) adati: “Ichi ndi chifundo chochokera kwa Mbuye wanga; koma likadzafika lonjezo la Mbuye wanga (kudza kwa Qiyâma), adzachiswanyaswanya; ndipo lonjezo la Mbuye wanga nloona.”
Ndipo patsiku limenelo tidzawasiya ena a iwo (oipa) akuchita chipolowe pa ena; ndipo lidzaimbidwa lipenga. Pamenepo tidzawasonkhanitsa onse pamodzi.
Iwowo ndi amene sadakhulupirire zisonyezo za Mbuye wawo, ndipo (sadakhulupirire) zakukumana Naye. Choncho zochita zawo zaonongeka (zapita pachabe), ndipo pa tsiku la chiweruziro sitidzawaikira sikelo.
Zimenezo, mphoto yawo ndi Jahannam chifukwa cha kusakhulupirira kwawo, ndipo Ayah Zanga ndi atumiki Anga adazichitira chipongwe.
Nena: “Ngakhale nyanja ikadakhala inki yolembera mawu a Mbuye wanga, nyanjayo ikadatha mawu a Mbuye wanga asadathe, ngakhale tikadabweretsa nyanja ina ndikuionjezera pa iyo (nyanjazo zikadatha, mawu a Allah akalipobe).”
Share