Surah An-Nahl ( The Bees )

Surah An-Nahl ( The Bees ) - Chewa Aya count 128

Lamulo la Allah lidzafika, (ndithu) choncho, musalifulumizitse; (ndipo khulupirirani kuti Iye ndi Allah) Woyera Wopatukana ndi mbiri zopunguka, ndipo watukuka ku zomwe akumphatikiza nazo.
Amatumiza angelo pansi pamodzi ndi chivumbulutso mwa lamulo Lake (Allah), kwa omwe wawafuna mwa akapolo Ake (powauza) kuti: “Achenjezeni (anthu zakuti): ‘Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Ine ndekha, choncho ndiopeni.”
Adalenga thambo ndi nthaka mwachoonadi (osati mwakungoseweretsa chabe) ndipo watukuka kuzimene akumphatikiza nazo (ophatikiza Allah ndi mafano).
Adalenga munthu kuchokera ku dontho la umuna. Ha! kenaka iye (munthuyo) wakhala wotsutsana naye (Allah) woonekera.[247]
Ndipo adalenga ziweto (monga ngamira, ng’ombe ndi mbuzi) mwa izo mukupeza zofunda, ndi zothandiza (zina zambiri), ndipo zina mwa izo mumazidya.
Ndipo mumakondwa ndi kunyadira chifukwa cha kukongola kwa izo mukamabwera nazo (kuchokera kubusa mimba zitakhuta), ndi popita nazo (kubusa zikuyenda mwandawala).
Ndipo zimasenza mitolo yanu (yolemera) kukafika nayo ku midzi yakutali komwe simumatha kukafikako popanda kuvutika kwambiri. Ndithu Mbuye wanu Ngodekha kwabasi, Ngwachisoni zedi.
(Adalenganso) akavalo, nyumbu ndi abulu kuti muzizikwera ndi kutinso zizikhala chokometsera chanu (cholowetsa chisangalalo m’mitima yanu); ndipo adzalenga (zokwera zina) zomwe simukuzidziwa.
Ndipo ndi udindo wa Allah kusonyeza njira yolungama (yomwe ingakufikitseni ku Munda wamtendere), koma zilipo njira zina zokhota (zomwe sizifikitsa ku choonadi). Ndipo Allah akadafuna, akadakuongolani nonsenu (mwa chifuniro chanu ndi mopanda chifuniro chanu. Koma Iye adakupatsani nzeru kuti musankhe nokha njira imene mufuna).
Iye ndi Amene akukutsitsirani madzi kuchokera ku mitambo, madziwo mumamwa (pothetsa ludzu lanu), ndipo ndi madziwo mitengo imamera; mitengo yomwe mumadyetsera ziweto (zanu).
Ndi madzi omwewo amakumeretserani mmera, (mitengo ya) mzitona, kanjedza, mphesa, ndi mitundu ina yonse ya zipatso. Ndithu kupezeka kwa zimenezi ndi chisonyezo (chosonyeza mphamvu za Allah) kwa anthu olingalira.[248]
Ndipo chifukwa cha inu adagonjetsa usiku ndi usana; dzuwa ndi mwezi; (zonse zidalengedwa kuti zibwere ndi zokomera inu). Nazo nyenyezi zidagonjetsedwa mwa lamulo Lake. Ndithu m’zimenezi muli zizindikiro kwa anthu anzeru.
Ndiponso ndi zimene adakulengerani m’nthaka (zinthu zododornetsa monga nyama, mmera, miyala yamtengo wapatali, zamoyo ndi zopanda moyo), zautoto wosiyanasiyana ndi maonekedwe osiyanasiyana; ndithu m’zimenezo muli zisonyezo kwa anthu olalikika.
Ndipo Iye ndi Yemwe adagonjetsa nyanja kuti mudye nyama yamatumbi (ya) m’menemo (nsomba) ndikuti mutulutse m’menemo zodzikongoletsera zomwe mumavala; ndipo uona zombo zikuluzikulu zikung’amba (mafunde) m’menemo kuti mufunefune zabwino zake (njira ya malonda), ndi kuti muthokoze (Mbuye wanu Allah).
Ndipo adaika panthaka mapiri ataliatali kuti (nthaka) isagwedezeke nanu; ndipo (adaika) mitsinje ndi misewu kuti muongoke (potsata njira yeniyeni ndikukafika komwe mukufuna).[249]
Ndipo (adaikanso) zizindikiro zina, ndiponso kupyolera m’nyenyezi, iwo amalondola njira.
Kodi Yemwe amalenga angalingane ndi omwe salenga? Kodi simungakumbukire (ndikudziwa kulakwa kwanu pomuyerekeza Allah ndi mafano)?
Ngati mutayesera kuwerengera mtendere wa Allah simungathe kuuwerengera (wonse); ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.
Mulungu wanu ndi Mulungu Mmodzi Yekha; koma amene sakhulupirira za tsiku la chimaliziro, mitima yawo ikukana (kukhulupirira umodzi wa Allah), ndipo iwo akudzitukumula.
Ndipo (osakhulupirira) akafunsidwa: “Kodi Mbuye wanu watumizanji (kwa Mneneri Muhammad {s.a.w})?” Akunena: “(Sadatumize chilichonse koma) nthano zabodza za anthu akale.”[250]
(Motero akuwasokeretsa anthu) kuti akasenze mitolo yawo (ya machimo) yokwanira pa tsiku la Qiyâma, ndiponso gawo lamitolo ya omwe akuwasokeretsa popanda kuzindikira (osokerawo). Tamverani! Ndi yoipa kwabasi mitolo yomwe azikaisenza!
Omwe angelo akutenga miyoyo yawo atadzichitira okha zoipa (ponyoza Allah). Choncho adzadzipereka (kwa angelowa, kuti atenge miyoyo yawo akunena:) “Sitidali kuchita choipa chilichonse.” (Angelo adzati:) “Zoona, palibe chikaiko, Allah akudziwa kwambiri zomwe munkachita.”
“Choncho, lowani makomo a ku Jahannam; mukakhala m’menemo nthawi yaitali.” Taonani kuipitsitsa kwa malo a anthu odzikweza!
Ndipo kukanenedwa kwa omwe akuopa Allah (kuti): “Kodi nchiyani watumiza Mbuye wanu?” Amati: “Zabwino.” Kwa omwe achita zabwino padziko ili lapansi, awapatsanso zabwino, ndipo Nyumba ya tsiku la chimaliziro njabwino kwambiri, ndipo taonani ubwino wa Nyumba ya oopa (Allah)!
Minda yamuyaya adzailowa, pansi pake padzakhala pakuyenda mitsinje (ndi patsogolo pake), chokhumba chilichonse akachipeza mmenemo (popanda kuchivutikira); umo ndi momwe Allah amawalipirira omuopa (iye).
Kodi akuyembekezera china, awa osakhulupirira, posakhala kuti angelo awadzere ndikuwaononga; kapena kuti liwadzere lamulo la Mbuye wako (lakuwalanga)? Momwemo ndi m’mene adachitiranso omwe adalipo patsogolo pawo. Koma Allah sadawachitire choipa koma adadzichitira okha choipa.
Ndipo aja amapembedza mafano akuti: “Allah akadafuna, sitikadapembedza chilichonse kusiya Iye, ife ngakhale makolo athu; ndiponso palibe chomwe tikadachiyesa choletsedwa popanda lamulo Lake.” Momwemo ndimo adachitiranso aja omwe adalipo patsogolo pawo. Kodi atumiki ali ndi udindo winanso, osati kufikitsa uthenga woonekera (womveka?)
Ndipo iwo adalumbilira m’dzina la Allah, kulumbilira kwawo kwamphamvu (kuti) Allah sadzaukitsa amene afa; nchotani (kuti asawaukitse?) Ili ndi lonjezo lokakamizika kwa Iye, (kuwaukitsa ndi kuwalipira); koma anthu ambiri sadziwa.
Ndithu liwu Lathu pa chinthu chimene tikuchifuna kuti chichitike ndikuchiuza basi kuti: “Chitika,” ndipo chimachitikadi.
Ndipo omwe adasamuka chifukwa cha Allah (kusiya midzi yawo) pambuyo poponderezedwa (kumeneko,) ndithu tiwakhazika mwaubwino pa dziko lapansi; ndipo malipiro a tsiku la chimaliziro (omwe akuwayembekezera), ngakulu zedi, akadakhala akudziwa (awa oipa).
Ndipo patsogolo pako (aneneri) omwe tidawatuma adalinso amuna, omwe tidawavumbulutsira chivumbulutso. Choncho afunseni eni chikumbumtima (za m’mabuku a Allah akale) ngati inu simukudziwa.
Kapena (Allah) kuwalanga mkuyenda kwawo kwa uku ndi uko? Pomwe iwo sangathe kumulepheretsa Allah kuchita chomwe wafuna pa iwo?
Kapena kuwalanga uku ali ndi mantha oyembekezera chilango (pakulanga m’modzim’modzi kufikira onse atatha)? Ndithu Mbuye wanu Ngodekha Ngwachisoni chosatha.
Kodi sadaone chinthu chilichonse (molingalira) m’zimene Allah adalenga zomwe zithuzi zake zimazungulira kudzanjadzanja ndi kumanzere, kulambira Allah uku zili zodzichepetsa kwa Iye? (Nanga iwo osakhulupirira akudzikweza chotani pamaso pa Allah?)
Ndipo mtendere wonse umene muli nawo udachokera kwa Allah (koma inu simuthokoza), ndipo masautso akakukhudzani Iye ndi amene mumamulilira.
Ncholinga choti akane mtendere umene tawapatsa, choncho sangalalani pang’ono, posachedwapa mudziwa (mapeto a zochita zanu).
Ndipo gawo la zomwe tawapatsa akuliikira (milungu yawo yabodza) yomwe siizindikira chilichonse. Tallahi, (ndikulumbira Allah,) ndithudi, mudzafunsidwa pa zimene munkapeka.
Ndipo (mwaumbuli) akumuikira Allah ana aakazi (ponena kuti adabereka ana aakazi) Subuhana! (Wayera Allah kuzimenezi!) Ndipo iwo (eni) amadzifunira amene amawakonda (omwe ndi ana achimuna)!
Ndipo mmodzi wawo akauzidwa nkhani ya (kuti wabereka) mwana wamkazi nkhope yake imada, ndipo amadzala ndi madandaulo.
Amadzibisa kwa anthu chifukwa chankhani yoipa imene wauzidwa (nayamba kulingalira): Kodi akhale naye pamodzi ndikuyaluka (pamaso pa anthu), kapena angomkwilira m’dothi (ali moyo)? Mverani! Ndi choipa kwabasi chiweruzo chawo.[251]
Ndipo Allah akadakhala akulanga anthu (mwachangu) pa zolakwa zawo, sakadasiya ngakhale nyama imodzi pamwamba pa nthaka; koma akuwachedwetsera (chilangocho) mpaka panthawi yoikidwa; ndipo ikadzadza nthawi yawoyo, sangathe kuichedwetsa ngakhale ola limodzi; ndiponso sangathe kuifulumizitsa (ngakhale ola limodzi.)
Ndipo akumuikira Allah zimene (iwo) akuzida (omwe ndi ana aakazi pomati Allah adabala ana aakazi), ndipo malirime awo akunena bodza kuti iwo adzapeza zabwino (kwa Allah); palibe chikaiko, ndithu Moto ndi wawo, ndipo iwo adzasiidwa (mmenemo).
Pali Mulungu! Ndithudi tidatumiza (atumiki) kumitundu yomwe idalipo patsogolo pako, koma satana adawakometsera zochita zawo (zoipa ankaziona kuti nzabwino napitiriza kuzichita). Choncho iye (satana) ndi bwenzi wawo lero, (koma pa tsiku la chimaliziro, adzadana naye kwambiri), ndipo iwo adzapata chilango chowawa.
Ndipo Allah watsitsa madzi kuchokera ku mitambo, ndipo akuipatsa moyo nthaka ndi madziwo (pomeretsa mbewu) pambuyo poti nthakayo idali yakufa; ndithu m’zimenezo muli chisonyezo (chosonyeza kukhoza kwa Allah) kwa anthu amene amamva.
Palibe chikaiko, m’ziweto muli phunziro ndi lingaliro kwa inu. Timakumwetsani zomwe zili m’mimba mwa izo, (zomwe zimatuluka) pakati pa ndowe ndi magazi, (omwe ndi) mkaka woyera, wabwino wokoma kwa oumwa.
Ndipo kuchokera ku zipatso za tende ndi mphesa, mumakonza zakumwa zoledzeretsa (zomwe nzoletsedwa) ndikupezanso rizq labwino (m’zipatsozo); ndithudi m’zimenezo muli lingaliro kwa anthu oganiza mwanzeru.
“Tsono idya zipatso zamtundu uliwonse ndikuyenda m’njira za Mbuye wako zimene wazifewetsa (kuziyenda).” Chimatuluka m’mimba mwake chakumwa cha utoto wosiyanasiyana (uchi), mwa icho muli kuchilitsa kwa anthu (kumatenda ochuluka), ndithu m’zimenezo muli zizindikiro kwa anthu oganiza (zinthu) mwakuya.
Ndipo Allah adakulengani, kenako akukupatsani imfa (nthawi ya moyo wanu ikatha); ndipo mwa inu alipo ena amene akubwezedwa ku moyo wonyozeka (waukalamba wogwa nkumina) kotero kuti asadziwe kanthu pambuyo pakudziwa (zambiri); ndithudi Allah Ngodziwa kwambiri Wokhoza (chilichonse chimene wafuna kuti chichitike).
Ndipo Allah wapereka zopereka Zake mochuluka kwa ena kuposa ena; ndipo amene apatsidwa mochulukawo sangagawire zopatsidwa zawo omwe manja awo adzanjadzanja apeza (akapolo awo) kuti akhale ofanana pa zopatsidwazo, (nanga bwanji inu mukuti Allah ngofanana ndi akapolo Ake pomwe inu simufuna kufanana ndi akapolo anu?) Nanga kodi mtendere wa Allah akuukana?
Allah akuponya fanizo la (anthu awiri: Wina ndi) kapolo wopatidwa (wokhala pansi pa ulamuliro wa munthu wina); yemwe alibe mphamvu pa chilichonse; ndi (munthu) yemwe tampatsa zabwino zochokera kwa Ife, ndipo iye nkupereka rizqlo mobisa ndi moonekera; kodi angafanane (awiriwa? Nanga bwanji mukufananitsa Allah ndi mafano?) Kuyamikidwa konse nkwa Allah. Koma ambiri aiwo sadziwa (kuyamika Allah).
Ndipo Allah waponyanso fanizo la anthu (ena) awiri: Mmodzi ndi bubu (wosatha kuyankhula), alibe mphamvu pa chilichonse; ndipo iye ndi mtolo wolemetsa chabe bwana wake; kulikonse kumene wamulunjikitsa, sabwerako ndi chabwino (chifukwa cha umbutuma wake). Kodi iye angafanane ndi yemwe akulamula mwa chilungamo, yemwenso ali pa njira yolunjika?
Ndipo chinsinsi cha (za) kumwamba ndi (za) pansi ncha Allah Yekha, (Iye ndiye amene akudziwa zochitika m’menemo, osati wina wake). Ndipo kuchitika kwa Qiyâma kuli ngati kuphetira kwa diso, kapena kufulumilirapo. Ndithudi, Allah Ngokhoza chilichonse.
Ndipo Allah adakuikirani nyumba zanu kuti zikhale mokhala (mwanu), ndiponso adakupangirani zikopa za ziweto (kukhala zotheka kuzikonza) kukhala nyumba, zomwe mumaziona kuti nzopepuka kuzitenga panthawi Ya ulendo wanu ndi panthawi ya kukhazikika kwanu (pamalo); ndipo kuchokera ku bweya wake wautaliutali ndi bweya wake wa manyunyu (ung’onoung’ono), ndi tsitsi lake (la ziwetozo,) mumakonza ziwiya (zovala) zosangalatsa, kwa kanthawi.
Ndipo mwa zina zomwe Allah adapanga, adakupangirani zodzetsa mthunzi; ndipo adakupangirani mokhala kumapiri (monga mapanga akuluakulu). Adakupangiraninso nsalu (zathonje ndi ubweya) zokutetezani ku kutentha (ndi kuzizira), ndiponso (adakupangirani) zovala (za chitsulo) zokutetezani pankhondo zanu. Umo ndi momwe akukukwaniritsirani chisomo Chake kuti mugonjere (Iye).
Koma ngati anyoza, basi palibe udindo wina pa iwe koma kufikitsa uthenga womveka (popanda kubisapo kalikonse).
Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe tidzautsa mboni mu mtundu uliwonse; kenako sikudzaloledwa, kwa amene sadakhulupirire, (kupereka madandaulo) ndipo iwo sadzauzidwa kuti afunefune chiyanjo cha Allah (koma chilango basi).
Ndipo amene achita zoipa akadzachiona chilango (ndikuyamba kudandaula ndi kulira), sichidzachepetsedwa kwa iwo (chilangocho), ndipo sadzapatsidwa mwayi wina.
Ndipo amene ankam’phatikiza Allah akadzawaona aphatikizi awowo adzati: “Mbuye wathu! Awa ndiaphatikizi athu omwe tidali kuwapembedza m’malo mwa Inu.” Ndipo (aphatikiziwo akadzamva mawu awa) adzawaponyera mawu awo (nkunena kuti): “Ndithu inu ndi abodza.”
Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe tidzautsa mboni mu mtundu uliwonse zochokera mwa iwo omwe adzawachitira umboni (pa zomwe zinkachitika ndi iwo); ndipo tidzakubweretsa iwe kukhala mboni pa awa (anthu ako); ndiponso takuvumbulutsira buku ili lomwe likufotokoza za chinthu chilichonse lomwenso ndi chiongoko ndi mtendere ndiponso ndinkhani yosangalatsa kwa ogonjera (Allah).
Ndipo musakhale monga mkazi yemwe adakhulula ulusi wake pambuyo pouluka mwamphamvu, mukukuchita kulumbira kwanu pakati panu kukhala kwa chinyengo, chifukwa chakuti gulu la mtundu wina nlochuluka kwambiri kuposa gulu la mtundu wina (powasiya omwe mudalonjezana nawo chifukwa chakuwaona kuchepa, ndi kukagwirizana ndi omwe simudalonjezane nawo chifukwa chakuwaona kuchuluka); ndithu Allah akukuyesani mayeso pa njira yotere; ndipo ndithu pa tsiku la Qiyâma adzakufotokozerani za zomwe mudali kusiyana.
Ndipo Allah akadafuna, ndithu akadakuchitani kukhala gulu limodzi, (nonsenu mukadamumvera monga momwe adawachitira angelo, koma adakupatsani ufulu kuti muchite chimene mufuna); komatu amamulekelera kusokera amene wamfuna, ndipo amamuongola wamfuna; ndipo, ndithu mudzafunsidwa pa zomwe munkachita.
Ndipo musakuchite kulumbira kwanu kukhala njira yonyengelerana pakati panu, kuopera kuti mwendo ungatelere (pa njira yolungama nkukagwera ku Moto) pambuyo pokhazikika mwendowo (pa njirapo) ndi kukazilawa zoipa chifukwa chakutsekereza kwanu (anthu) ku njira ya Allah, ndipo nkupeza chilango chachikulu (tsiku lachimaliziro).
Ndipo musagulitse mapangano a Allah ndi mtengo wochepa (wa zomwe mukupeza pano pa dziko lapansi). Chimene chili kwa Allah, ndicho chabwino kwa inu ngati mukudziwa.
Ndipo ukafuna kuwerenga Qur’an dzitchinjirize ndi Allah kwa satana wopirikitsidwa (ponena kuti Awudhu Billahi mina Shaitwani Rajim).
Ndithudi mphamvu zake zili pa amene akumusankha (amulola) kukhala bwenzi lawo (mlangizi wawo) ndiponso ndi omwe akumphatikiza iye (ndi Allah).
Nena: “Mzimu woyera (Gabriel) waitsitsa (Qur’an) kuchokera kwa Mbuye wako mwachoonadi kuti awalimbikitse nayo amene akhulupirira ndi kuti ikhale chiongoko ndi nkhani yabwino kwa amene alowa m’Chisilamu (amene agonjera Allah).
Amene akukana Allah, pambuyo pomukhulupirira, (chilango chachikulu chikumuyembekezera), kupatula yemwe adakakamizidwa, uku mtima wake utakhazikika pa chikhulupiliro; koma amene akutsekulira mtima wake kusakhulupirira, mkwiyo wa Allah uli pa iwo (ndipo anthu otere) adzapata chilango chachikulu.[252]
Iwo ndi omwe Allah adawadinda m’mitima mwawo, m’makutu mwawo, ndi m’maso mwawo (chifukwa cha kusimbwa kwawo). Ndipo iwo ngonyalanyaza (malamulo a Allah) kwambiri.
Ndithudi kenako Mbuye wako, kwa amene adasamuka pambuyo pakusautsidwa (kufikira adanena zosayenera) komanso nkuchita Jihâd ndikupirira (chifukwa cha chipembedzo), ndithu Mbuye wako pambuyo pa zimenezo, Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosantha.
(Akumbutse za) tsiku lomwe mzimu uliwonse udzadza ukudziteteza wokha (wosalabadira za mwana wake, mkazi wake ndi abale ake), ndipo mzimu uliwonse udzalipidwa molingana ndi zochita zake zimene unkachita, ndipo iwo sadzachitidwa chinyengo (pochepetsedwa mphoto yawo yoti alandire.)
Ndipo Allah waponya fanizo lamudzi womwe udakhala mwa mtendere mokhazikika, rizq lake (madalitso) linkaudzera mochuluka kuchokera malo aliwonse; koma (mudziwo) udakana mtendere wa Allah (pakusathokoza); choncho Allah adaulawitsa chovala cha njala ndi mantha chifukwa cha (zoipa) zomwe (anthu ake) adali kuchita.
Ndithu wakuletsani (kudya) zakufa zokha, magazi (liwende), nyama ya nkhumba ndi chimene chazingidwa posatchula dzina la Allah. Koma amene wasimidwa (nadya choletsedwa) mosafuna kapena kupyoza muyeso (Allah amkhululukira), ndithudi Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni.
Ndichisangalalo chochepa (cha m’dziko lapansi chimene chikuwachititsa zimenezo); ndipo iwo adzapata chilango chowawa.
Ndithu Ibrahim adali mtsogoleri (chitsanzo chabwino kwa anthu), womvera Allah, wopendekera ku choonadi ndipo sadali mwa omuphatikiza (Allah ndi mafano).
Kenako takuvumbulutsira (iwe Muhammad{s.a.w} mawu) akuti: “Tsatira njira (chipembedzo) ya Ibrahim (yemwe adali) wokwanira mkulungama, ndipo sadali mwa omuphatikiza (Allah ndi mafano.)”
Itanira (anthu) ku njira ya Mbuye wako mwanzeru ndi ulaliki wabwino; ndipo tsutsana nawo mkutsutsana kwabwino (osati motukwanana kapena monyozana). Ndithu Mbuye wako Iye Ngodziwa kwambiri za amene asokera ku njira Yake, ndiponso Iye Ngodziwa kwambiri za amene aongoka.
Ndipo ngati mukubwezera (choipa chimene mwachitiridwa), bwezerani cholingana ndi chimene mwachitiridwacho, koma ngati mutapirira (posiya kubwezera), ndithu kutero ndi ubwino kwa opirira.
Ndipo pirira. Kupirira kwakoko kusakhale pa china chake koma Allah basi. Ndipo usadandaule chifukwa cha iwo, (iwo akudzisokeretsa okha). Ndipo usakhale wobanika chifukwa cha chiwembu chomwe akuchita.
Share