Surah Yusuf (Joseph )

Surah Yusuf (Joseph ) - Chewa Aya count 111

Alif-Lâm-Ra. Izi ndi Ayah (ndime) za m’buku lomwe likuonetsera poyera (chilichonse chofunika).
Kumbuka pamene (abale a Yûsuf) adati: “Ndithu Yûsuf ndi m’bale wake (Binyamini) ngokondeka zedi kwa bambo wathu kuposa ife pomwe ife ndife gulu lamphamvu. Ndithu bambo wathu ali mkusokera koonekera (sadziwa yemwe ali ndi chithandizo chokwanira).”
“Mupheni Yûsuf kapena mukamponye ku dziko (lakutali), kuti nkhope ya bambo wanu ikutembenukireni (pakuti nthawi imeneyo Yûsuf sadzakhalapo, yemwe akumkonda kwambiriyo); ndipo pambuyo pake (mutalapa tchimoli) mdzakhala abwino, (kwa Allah).”[229]
(Pambuyo pogwirizana paganizo lomuponya m’chitsime chakuya adapita kwa bambo wawo) anati: “E bambo wathu! Kodi bwanji simutikhulupirira pa Yûsuf, pomwe ife timamfunira zabwino?”
Mperekeni mawa pamodzi ndi ife (kubusa) kuti akadye mokondwa ndi kusewera; ndithudi, ife tikamsamala.”
(Iwo) adati: “Ngati mimbulu itamudya pomwe ife ndife gulu lanyonga kwambiri, ndiye kuti tidzakhala otaika.”
Ndipo pamene adanka naye ndi kugwirizana pakati pawo kuti amuike mchitsime chakuya, (adamuikadi). Ndipo tidamzindikiritsa iye (Yûsuf): “Ndithu udzawauza chinthu chawochi (chimene akuchitirachi) pomwe iwo sakudziwa.”
Akunena: “E bambo wathu! Tidapita kokapikisana (kuthamanga), ndipo tidamsiya Yûsuf pomwe padali ziwiya zathu; choncho mimbulu yamudya koma inu simutikhulupirira (pa zimene tikukuuzanizi) ngakhale kuti tikunena zoona.”
Ndiponso adabwera ndi mkanjo wake (wa Yûsuf) uli ndi magazi abodza. (Bambo wawo pamene adauona mkanjowo uli wosang’ambika) adati: “Koma mitima yanu yakukometserani chinthu (chomwe mwamchitira mnzanu mwa chifuniro chanu; ndipo chimene ine ndingachite ndi) kupirira kwabwino; ndipo Allah ndi Wopemphedwa chithandizo pa zimene mukunenazi.”
Ndipo aulendo adadza (pafupi ndi chitsimecho) ndipo adatuma wotunga madzi wawo, choncho iye adaponya ndowa yake (m’chitsime, ndipo akukoka ndowa ija adaona mwana) nati: “Eee, chisangalalo changa! Aka kamwana kakamuna!” Pomwepo iwo (amene adalipo pa chitsimepo) adam’bisa (kwa a paulendo anzawo) monga katundu wamalonda (yemwe adamgula). Koma Allah ankadziwa zimene adali kuchita (ndipo adanka naye ku Iguputo).[230]
Ndipo adamgulitsa pa mtengo wochepa ndi ndalama zapang’ono, zowerengeka (poopa kuti angawadzere eni mwanayo). Ndipo sadalabadire za iye.
Ndipo pamene (Yûsuf) adafika pa nsinkhu wozindikira zinthu, tidampatsa kuweruza ndi nzeru. Umo ndi momwe timawalipirira ochita zabwino.
Ndipo mkazi uja yemwe m’nyumba mwake mudali iye adamlakalaka (Yûsuf) popanda iye kufuna. Ndipo (mkaziyo) adatseka zitseko nati: “Bwera kuno.” (Yûsuf) adati: “Ndikudzitchinjiriza ndi Allah (kuchita tchimolo). Ndithu iye (mwamuna wako) ndi bwana wanga. Wandikonzera bwino pokhala panga (m’nyumba mwakemu, ndipo sindichita chinyengo chotere). Ndithu achinyengo siziwayendera bwino.”
Ndipo (mkaziyo) adaikira mtima pa iye (kuti achite naye kanthu), ndipo naye (Yûsuf) adaikira mtima pa iye (kuti ammenye). Pakadapanda kuona chisonyezo cha Mbuye wake (chakumzindikiritsa kuti asatero, akadammenya. Koma adamthawa). Tidachita izi kuti timchotsere chinthu choipa ndi chauve; ndithudi, iye adali mwa akapolo athu oyeretsedwa.[231]
Ndipo (onse awiri) adathamangitsana kukhomo (uku Yûsuf akuthawa) ndipo (mkaziyo) adang’amba mkanjo wake chakumbuyo. Ndipo awiriwa adampeza bwana wake (wa mkaziyo yemwe ndimwamuna wake) pakhomo; mkaziyo adati (kwa mwamuna wake mwaugogodi): “Palibe mphoto kwa yemwe akufuna kuchita choipa ndi mkazi wako koma kumponya kundende, kapena kupatsidwa chilango chowawa.”
(Yûsuf) adati (podziteteza): “(Mkazi) uyu ndi yemwe wandifuna popanda ine kumufuna.” Ndipo mboni yochokera ku banja la mkaziyo idaikira umboni; (idati): “Ngati mkanjo wake wang’ambidwa cha kutsogolo, ndiye kuti (mkazi uyu) akunena zoona, ndipo iye (Yûsuf) ndi mmodzi mwa onena zabodza.”
“Koma ngati mkanjo wake wang’ambidwa chakumbuyo ndiye kuti (mkazi uyu) wanena bodza ndipo iye (Yûsuf) ndi mmodzi mwa onena zoona.”
Choncho (mwamuna uja) pamene adaona mkanjo wake (wa Yûsuf) utang’ambidwa chakumbuyo, (adadziwa kuti Yûsuf ndi amene amafuna kugwiliridwa), adati: “Ndithudi, izi ndi ndale zanu akazi. Ndithu ndale zanu ndi zazikulu (iwe mkazi wanga ndi amene udatsimikiza kuchita choipa ndi mnyamatayu).”
“Yûsuf! Zisiye izi (usauze aliyense). Ndipo (iwe mkazi) pempha chikhululuko ku tchimo lako. Ndithu iwe ndiwe mmodzi mwa olakwa!”
Ndipo akazi a mu mzindamo (ataimva nkhaniyi) anati: “Mkazi wa nduna akulakalaka m’nyamata wake popanda kulakalakidwa ndi iye; ndithu chikondi chamufooketsa zedi; ndithudi, ife tikumuona (mkaziyu kuti) ali m’kusokera koonekera.”
Ndipo (mkazi wa nduna) pamene adamva kunyogodola kwawo, adawaitana (kuti adzaone kukongola kwa Yûsuf kuti adziwe kuti yemwe wathedwa nzeru polakalaka Yûsuf ngosayenera kudzudzulidwa). Ndipo adawakonzera phwando ndikupatsa aliyense wa iwo mpeni; kenaka adamuuza (Yûsuf): “Tuluka ndi kubwera pamaso pa iwo.” Choncho pamene (akazi aja) adamuona, adaona kuti nchinthu chachikulu zedi ndipo adadzicheka manja awo (ndi mipeni ija. Sadazindikire kuti akudzicheka chifukwa cha chidwi ndi kukongola kwa Yûsuf), ndipo adati: “Hasha Lillah! (tikudzitchinjiriza kwa Allah) uyu simunthu, uyu sichina koma ndi mngelo wolemekezeka.”
Kenako kudaoneka kwa iwo, (nduna ndi anthu ake) pambuyo poona zizindikiro (zonse zakuyeretsedwa kwa Yûsuf) kuti akamponye kundende kwa nthawi yochepa (pofuna kumusungira ulemu mkazi wa nduna).
(Yûsuf) adati: “(Kupyolera mu uneneri umene ndapatsidwa ndingathe kukumasulirani maloto anuwa ndi zinthu zina zobisika kwa inu), sichikudzerani chakudya cha mtundu uliwonse choti mungapatsidwe koma ndikhala nditakumasulirani tanthauzo lake chisanakufikeni; (ngati mukufunadi ndikuchitirani zimenezi). Izi ndi zina mwa zomwe Mbuye wanga wandiphunzitsa. Ndithudi, ine ndasiya njira za anthu osakhulupirira Allah ndiponso omwe akukana za tsiku la chimaliziro.”
“E inu anzanga awiri a m’ndende! Kodi milungu yambiri yosiyana ndiyo yabwino (kupembedzedwa), kapena Allah Mmodzi Mwini mphamvu (pachilichonse)?”
“E inu anzanga awiri a m’ndende! Tsono mmodzi wa inu (abwerera ku ntchito yake) azikamwetsa mowa bwana wake (monga zidalili poyamba); koma winayo aphedwa mopachikidwa, ndipo mbalame zidzadya mmutu wake. Chiweruzo chaweruzidwa kale (kwa Farawo) pa chinthu chomwe mudali kufunsa.”
Ndipo (Yûsuf) adauza yemwe adamdziwa kuti apulumuka mwa awiriwo: “Ukandikumbuke ponditchula pamaso pa bwana wako (Farawo; ukamuuze kuti ndamangidwa popanda tchimo).” Koma satana adamuiwalitsa kumkumbutsa bwana wake. Tero (mneneri Yûsuf) adakhala m’ndende zaka zingapo.
Ndipo (tsiku lina) mfumu (Farawo adalota) nati (kwa nduna zake): “Ndithudi, ine ndalota ng’ombe zisanu ndi ziwiri zonenepa zikudyedwa ndi ng’ombe zisanu ndi ziwiri zowonda ndiponso ndalota ngala zisanu ndi ziwiri zaziwisi ndi zina (zisanu ndi ziwiri) zouma. E inu akuluakulu! Ndimasulireni maloto angawa, ngati inu mumatha kumasulira maloto.”
(Iwo) adati: “Amenewa ndi maloto osakanikirana (simaloto omveka)! Ndipo ife sitili odziwa kumasulira maloto amtundu umenewu.”
Pamenepo amene adapulumuka mwa awiri aja adanena atakumbukira (pempho la Yûsuf) patapita nyengo (yaitali), adati: “Ine ndikuuzani tanthauzo lake. Choncho nditumeni (kuti ndikakufunireni tanthauzo lake).”
(Adanka kundende ndikumpempha Yûsuf chikhululuko chifukwa cha kuiwala kwake. Ndipo adati): “Yûsuf! E iwe woona! Tiuze za ng’ombe zisanu ndi ziwiri zonenepa zikudyedwa ndi zisanu ndi ziwiri zoonda, ndi ngala zisanu ndi ziwiri zaziwisi ndi zina zouma; kuti ine ndibwelere kwa anthu kuti akadziwe.”
(Yûsuf) adati: “Mudzalima zaka zisanu ndi ziwiri mondondozana ndi mwakhama ndipo zimene mwakolola zisiyeni m’ngala zake, kupatula zochepa zimene muzidzadya (kuti zam’ngalazo mudzadye mzaka zanjala).”
“Kenako pambuyo pake zidzadza zaka zisanu ndi ziwiri za masautso zomwe zidzadya zimene mudasunga m’mbuyo, kupatula zochepa zimene muzidzazisunga (mobisa kuti zidzakhale mbewu.)”
“Kenako pambuyo pa izi chidzadza chaka chomwe anthu m’menemo adzapulumutsidwa (ndi Allah), ndipo m’menemo adzafinya (zakumwa).”
Ndipo mfumu idati: “M’bweretseni iye kwa ine.” Koma pamene mthenga (wa Mfumu) adamfika (Yûsuf, iye) adati: “Bwerera kwa bwana wako ndipo ukamfunse nkhani ya akazi omwe ankadzicheka manja awo. Ndithu Mbuye wanga akudziwa bwino ndale zawo. (Koma ndikufuna Mfumu kuti idziwe za kuyera kwanga kuti andiyeretsere maganizo ndipo asandiope).”
(Mfumu idasonkhanitsa akazi aja ndipo) idati: “Kodi nkhani yanu njotani pamene mudamulakalaka Yûsuf pomwe iye sakufuna?” Adati: “Hasha Lillah! (Tikudzitchinjiriza kwa Allah)! Ife sitidadziwe choipa chilichonse kwa iye. (Tidayesayesa kuti achite nafe choipa koma sadalole).” (Nayenso) mkazi wa nduna adati: “Tsopano choonadi chatsimikizika; ine ndine amene ndidamulakalaka pomwe iye sakufuna. Ndithu iye ndi mmodzi mwa owona.”
(Yûsuf adati): “Zimenezo (zofuna kuti afunsidwe chonchi) n’chifukwa chakuti (nduna) idziwe kuti ine sindidaichitire zoipa iyo kulibe, ndi kuti Allah saongolera ndale za anthu achinyengo (kuti zipambane).”
۞ “Ndipo ine sindikuyeretsa mtima wanga. Ndithu mtima uliwonse umalamulira kwambiri ku zoipa kupatula umene Mbuye wanga wauchitira chifundo. Ndithudi, Mbuye wanga Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.”
Choncho Mfumu idati: “Mubwere naye kwa ine kuti ine mwini ndimsankhe.” Ndipo pamene adayankhula naye, (Mfumu) idati: “Ndithu iwe lero kwa ife wakhala wolemekezeka, wokhulupirika.”
(Yûsuf) adati: “Ndiikeni kukhala muyang’aniri wa nkhokwe za dzinthu zam’dziko lonse. Ndithudi, ine ndine msungi wodziwa.”
Ndipo motero tidampatsa ulemelero Yûsuf m’dziko (la Iguputo); amakhala m’menemo paliponse pamene wafuna. Timam’bweretsera chifundo Chathu amene tamfuna, ndipo sitisokoneza malipiro a ochita zabwino.
Ndithudi malipiro a tsiku la chimaliziro ngabwino zedi kwa amene akhulupirira ndipo adali kumuopa (Allah).
Ndipo adadza abale (ake) a Yûsuf (kukafuna chakudya kumeneko pamene ku Kenani kudagwa chilala chadzaoneni) ndikulowa kwa iye, ndipo (iye) adawazindikira pomwe iwo sankamzindikira.
Ndipo pamene adawakonzera chakudya chawo, adati: “(Ngatimudzabwereranso kachiwiri) mudzabwere ndi m‘bale wanu wa kumbali ya bambo anu, kodi simuona kuti ine ndikukwaniritsa muyeso, ndipo ndine wabwino kwambiri polandira (alendo)?”
“Koma ngati simudzandibweretsera iye, simudzakhala ndi mulingo (wachakudya) kwa ine, ndipo musadzandiyandikire.”
(Iwo) adati: “Tikayesetsa kuwanyengelera bambo wake za iye (kufikira akatipatse). Ndithu ife tikachita zimenezi.”
Ndipo pamene adabwerera kwa bambo wawo, adati: “E bambo wathu! Tikamanidwa muyeso wa chakudya (pa ulendo wachiwiri pokhapokha titsagane ndi m’bale wathuyu). Choncho mtumizeni m’bale wathu pamodzi ndi ife kuti akatipimire (mlingo wokwana); ndithu ife tikamsunga.”
(Ya’qub) adati: “Kodi ndingakukhulupirireni pa iye kuposa momwe ndidakukhulupirirani pa m’bale wake kale (yemwe mudamsokeretsa)? Koma Allah ndi Yemwe ali Wabwino posunga, Ndipo Iye Ngwachifundo zedi kuposa achifundo onse.”
Ndipo pamene adatsekula katundu wawo, adapeza chuma chawo chabwezedwa kwa iwo. Adati: “E bambo wathu! Tingafunenso chiyani (kwa munthu waufuluyu)? Ichi chuma chathu chabwezedwa kwa ife; ndipo tikabweretsa chakudya chothandizira mawanja athu; ndipo m’bale wathu tikamsunga; tikapezanso muyeso wangamira imodzi yoonjezera. Umenewu ndi mlingo wochepa (kwa mfumu ya ufuluyo).”
(Ya’qub) adati: “Sindingamtumize pamodzi ndi inu pokhapokha mundipatse lonjezo m’dzina la Allah kuti ndithudi mudzambweza kwa ine pokhapokha nonsenu mutazingidwa (ndi zoopsa).” Ndipo pamene adapereka lonjezo lawo, (iye) adati: “Allah ndiye Muyang’aniri (mboni) pa zimene tikunenazi.”
Ndipo pamene adalowa monga momwe bambo wawo adawalamulira, sikudawathandize chilichonse kwa Allah kupatula khumbo lomwe lidali mu mtima mwa Ya’qub (ndilomwe) adalikwaniritsa, (Ya’qub adali kufuna Yûsuf ndi m’bale wake akumane mwamseri; ndipo adakumanadi). Ndithu iye (Ya’qub) adali wanzeru chifukwa chakuti tidamphunzitsa. Koma anthu ambiri sadziwa.
Ndipo pamene adalowa kwa Yûsuf (ndikumuona m’bale wake atalowa payekha), adamkumbatira m’bale wakeyo nati: “Ndithu ine ndine m’bale wako; choncho usadandaule pa zimene (abale athu) akhala akuchita.”
(Onse abale ake a Yûsuf) pamene adawacheukira, adati: “Kodi mukusowa chiyani?”
Adati: “Tikusowa muyeso wa Mfumu; ndipo amene aubweretse, alandira mtolo wangamira yathunthu.” (Ndipo Mneneri Yûsuf adati): “Ndipo ine ndine muimiliri pa zimenezi.”
Adati: “Mphoto (chilango) yake ikhala yotani ngati mukunena bodza?”
Adati: “Mphoto yake ndi yemwe (chikhocho) chapezeka mu mtolo wake, iye ndiye mphoto yake. (Agwidwe monga kapolo kwa chaka chimodzi).” Umu ndi momwe timawalipirira anthu achinyengo.
Ndipo (mneneri Yûsuf) adayamba kufufuza m’mitolo mwawo asanafufuze mu mtolo wa m’bale wake; kenako adachitulutsa mu mtolo wa m’bale wake. Umu ndi momwe tidamlinganizira ndale Yûsuf (kuti ampeze m’bale wake). Mwachilamulo cha mfumu (ya m’dzikolo) sakadamutenga m’bale wake (monga kapolo) koma mmene Allah adafunira (powaonetsa abale ake za chilamulo cha kwawo chomuika mu ukapolo munthu wakuba). Timawakwezera pa ulemelero amene tawafuna. Ndipo pa wodziwa aliyense pali wodziwanso kuposa iye.
(Iwo) adati: “Ngati waba, m’bale wakenso adabapo kale.” (Uku kudali kumunamizira Yûsuf bodza pomwe iwo sankadziwa kuti yemwe akuyankhula nayeyo ndiye Yûsuf). Koma Yûsuf adabisa (mawu awa) mu mtima mwake, (chifukwa chowamvera chisoni) ndipo sadawaululire. Adati: “Inu muli ndi chikhalidwe choipa ndipo Allah akudziwa zomwe mukunena!”
(Yûsuf) adati: “Ha! tikudzitchinjiriza mwa Allah, sitingagwire wina koma yemwe chuma chathu tachipeza ndi iye, kuopa kuti tingakhale ochita zoipa.”
Choncho, pamene adataya mtima za iye, adapita pambali kukanong’onezana. Wamkulu wawo adati: “Kodi simudziwa kuti bambo wanu adatenga lonjezo kuchokera kwa inu m’dzina la Allah (kuti mudzam’bweza iyeyo?) ndiponso kale mudalakwa (pa mapangano anu) pa za Yûsuf. Choncho sindichoka dziko lino kufikira atandilola bambo (kutero) kapena Allah andilamule (zondichotsa kuno pomasulidwa m’bale wangayu); Iye Ngwabwino polamula kuposa olamula.”
“Bwererani kwa bambo wanu ndipo mukawauze (kuti): “E bambo wathu! Ndithu mwana wanu waba. Ndipo ife sitidaikire umboni (wakuti wakuba achitidwe ukapolo) koma pa zomwe tidazidziwa (kuti mwa ife mulibe wakuba), ndipo sitidali kudziwa zamseri.”
Ndipo adawachokera ndikunena (kuti): “Ha! kudandaula kwanga za Yûsuf!” Ndipo maso ake adayera chifukwa cha kudandaula ndipo iye adadzazidwa ndi chisoni.
(Iwo) adati: “Tikulumbira Allah! Simusiya kumkumbukira Yûsuf (ndikulira) mpaka mufika podwala, kapena mukhala mwa owonongeka (ndi imfa).”
(Iye) adati: “Ndithu ine ndikusuma dandaulo langa ndi kukhumata kwanga kwa Allah, ndipo ndikudziwa kupyolera mwa Allah zomwe simukudziwa.”
(Ndipo adapita ku Iguputo). Choncho pamene adalowa kwa iye (Yûsuf), adati: “E inu olemekezeka! Masautso atikhudza, ife ndi maanja athu; choncho tabwera ndi chuma chopanda pake. Tidzadzireni mlingo (ngakhale chuma chathucho chili chopanda pake), ndipo tithandizeni mwaulere. Ndithu Allah amawalipira othandiza mwaulere.”
Ndipo aulendo pamene adamuka (kubwerera kwawo). Bambo wawo (yemwe adali ku Kenani) adati: “Ndikumva fungo la Yûsuf pakadapanda kuti muli ndi chikhulupiliro choti ndasokonezeka nzeru, (mukadandikhulupirira)”
(Iwo) adati: “Tikulumbira Allah! Ndithu muli mkusokera kwanu kwa kale (pokonda Yûsuf kuposa ife).”
Choncho pamene adadza wotenga nkhani yabwino, adauponya (mkanjo wa Yûsuf) pankhope pake, ndipo pompo adapenya. Adati: “Kodi sindinakuuzeni kuti ine ndikudziwa kupyolera mwa Allah zomwe inu simukuzidziwa?”
(Iye) adati: “Posachedwapa (ndikamuona Yûsuf) ndikupempherani chikhululuko kwa Mbuye wanga. Ndithu Iye Ngokhululuka zedi, Ngwachisoni chosatha.”
Ndipo (pamene adafika kwa Yûsuf), (iye) adawakweza makolo ake ndikuwaika pa chimpando (chake) chachifumu, ndipo onse adagwa kumlambira (monga mwachizolowezi chawo nthawi imeneyo). Ndipo (Yûsuf) adati: “E inu bambo wanga! Ili ndilo tanthauzo (lenileni) la maloto anga akale. Palibe chipeneko Mbuye wanga wawatsimikiza (malotowo). Ndipo adandichitira zabwino ponditulutsa kundende ndi pokubweretsani inu kuchokera kumidzi (Kenani), pambuyo pokhwirizira (chidani) satana pakati pa ine ndi abale anga. Ndithudi Mbuye wanga amadziwa kwambiri chinsinsi cha zomwe wakonza kuti zichitike. Ndithu Iye Ngodziwa, Ngwanzeru.
(Kenako adathokoza ndi kupempha Allah kuti): “E Mbuye wanga! Ndithu mwandipatsako ufumu ndi kundiphunzitsako kumasulira nkhani (maloto). E Inu Mlengi wa thambo ndi nthaka! Inu ndiye Mtetezi wanga pa dziko lapansi ndi tsiku la chimaliziro. (Ndipo nthawi ya imfa yanga) mudzandipatse imfa ndili Msilamu ndipo kandikumanitseni ndi ochita zabwino.”
Nena: “Iyi ndi njira yanga. Ndikuitanira kwa Allah mwa nzeru zokwanira, ine ndi omwe akunditsata. Ndithu Allah wapatukana (ndi mbiri zopunguka). Ndipo ine sindili mwa ophatikiza (Allah ndi zinthu zina).”[235]
Ndipo sitidatume (mtumiki aliyense) patsogolo pako koma adali amuna amene tidawavumbulutsira (chivumbulutso); ochokera mwa anthu a m’mizinda. Kodi sadayende (iwo osakhulupirira) pa dziko nkuona momwe mathero a oipa omwe adalipo patsogolo pawo (momwe adalili)? Ndipo nyumba ya tsiku la chimaliziro njabwino kwa owopa Allah. Kodi mulibe nzeru?
Ndithu m’nkhani zawo izi muli phunziro kwa eni nzeru. (Qur’aniyi) simawu opekedwa, koma (iyi Qur’an) ndi chitsimikizo cha zomwe zidalipo patsogolo pake (m’mabuku ena a Allah), ndi kumasulira kwa tsatanetsatane pa chilichonse ndiponso chiongoko ndi mtendere kwa anthu okhulupirira.
Share