Surah Hud

Surah Hud - Chewa Aya count 123

Alif-Lam-Ra. Ili ndi buku lomwe ndime zake zakonzedwa bwino ndipo zafotokozedwa mwatsatanetsatane kuchokera kwa Allah Mwini nzeru zakuya Wodziwa chilichonse.
(Wachita zimenezi) kuti musampembedze wina wake koma Allah yekha. Ndithudi ine kwa inu ndimchenjezi wochokera kwa Iye ndiponso wokuuzani nkhani zabwino.
۞ Ndipo palibe nyama iliyonse panthaka koma rizq lake lili kwa Allah; ndipo (Iye) akudziwa mbuto yake yamuyaya ndi mbuto yake yakungodutsapo (yomwe ndi pano padziko lapansi). Zonse zili m’buku lofotokoza chilichonse.[219]
Ndipo ngati titawachedwetsera chilango mpaka m’nthawi yodziwika (ndi kukhazikitsidwa ndi Ife), akunena (mwamwano): “Nchiyani chikumanga chilangocho (kuti chidze)? “Tamverani! Tsiku lomwe chidzawadzera, sichidzachotsedwa kwa iwo ndipo zomwe adali kuzichita mwachibwana zidzawazinga.
Ndipo munthu tikamulawitsa mtendere wochokera kwa Ife, kenako nkuuchotsa kwa iye, ndithu amakhala wotaya mtima kwambiri ndikukhala wosathokoza.
Koma ngati titamulawitsa mtendere pambuyo pa masautso omwe adamkhudza, amati: “Masautso andichoka,”(ndipo sakhala wotanganidwa ndi ntchito zabwino zosonyeza kuyamika Allah), ndithudi iye amakhala wosangalala, wodzitukumula.
Mwina usiya zina mwa zomwe zikuvumbulutsidwa kwa iwe ndikubanika nazo mchifuwa mwako chifukwa chakuti akunena: “Bwanji sizidatsitsidwe kwa iye nkhokwe za chuma kapena bwanji mngelo osadza pamodzi ndi iye?” Koma ndithu iwe ndiwe mchenjezi basi ndipo Allah ndiye muyang’aniri wa chinthu chilichonse.[221]
Kapena akunena kuti: “Waipeka Qur’an?” Nena: “Tabweretsani sura khumi zopekedwa zomwe zingafanane ndi iyi (Qur’an) ndipo aitaneni amene mungathe (kuwaitana) kupatula Allah. (Adze akuthandizeni kulemba bukulo) ngati mukunena zoona!”
Amene akufuna moyo wa dziko lapansi ndi zokometsera zake, tiwapatsa pompo pa dziko lapansi (malipiro a) zochita zawo mokwanira, ndipo iwo m’menemo sachepetseredwa chilichonse.
Nanga kodi munthu yemwe ali ndi chisonyezo choonekera chochokera kwa Mbuye wake (kotero kuti m’moyo mwake akuyenda molungama; yemwe ndi mneneri Muhammad {s.a.w}), ndipo Mboni ili naye pamodzi ikumtsata yochokera kwa Iye (Mbuye wake yomwe ndi Qur’an kapena Gaburiel), ndipo patsogolo pake padali buku la Mûsa lomwe lidali chitsanzo chabwino ndi mtendere, (wotereyu angafanane ndi yemwe ali mum’dima wa umbuli yemwenso sadziwa cholinga chakulengedwa kwake?) Awa (amene aongoka) akulikhulupirira (buku ili la Qur’an), ndipo amene ati asalikhulupirire m’magulu (a adani), Moto ndiwo malo awo alonjezo. Choncho, usakhale ndi chipeneko pa ichi; ndithudi ichi ndi choona chochokera kwa Mbuye Wako koma anthu ambiri sakhulupirira.
Ndipo palibe oipitsitsa kuposa yemwe wapeka bodza pakumnamizira Allah (kuti ali ndi mwana ndi athandizi). Iwo adzabweretsedwa kwa Mbuye wawo (tsiku la Qiyâma) ndipo mboni (zomwe ndi angelo) zidzanena: “Awa ndi omwe adapekera Mbuye wawo bodza. Mverani! Tembelero la Allah lili pa ochita zoipa.”
Fanizo la magulu awiriwa (okhulupirira ndi osakhulupirira), lili ngati (munthu) wakhungu ndi gonthi, ndi (munthu) wopenya ndi wakumva. Kodi awiriwa angakhale ofanana (pa chikhalidwe chawo)? Bwanji simukuganiza?[222]
Ndipo ndithu Ife tidamtuma Nuh (monga Mtumiki) kwa anthu ake (kuti akawauze): “Ine kwa inu ndine mchenjezi owonekera poyera.”
Ndipo pompo akuluakulu mwa omwe sadakhulupirire mwa anthu ake, adati: “Sitikukuona koma ndiwe munthu monga ife, ndipo sitikukuona koma kuti akutsata anthu a pansi pathu ofooka pa nzeru (omwe sadalingalire mozama za iwe). Ndipo sitikukuonani kuti muli ndi ulemelero ndi ubwino wochuluka kuposa ife. Koma tikukuganizirani kuti ndinu onama.”
(Iye) adati: “E inu anthu anga! Kodi muona bwanji ngati ndili ndi chisonyezo chowonekera chochokera kwa Mbuye wanga ndipo wandipatsa chifundo chochokera kwa Iye (monga uneneri), ndipo chabisika kwa inu, kodi tingakukakamizeni kuvomereza pomwe simukuchifuna?”
“Ndipo E inu anthu anga! Ine sindikukupemphani chuma pa uthengawu. Palibe malipiro anga, koma ali kwa Allah basi. Ndipo ine sindingathamangitse amene akhulupirira (monga momwe mudandipemphera kuti ndiwathamangitse anthu ofooka kuti inu mulowe m’malo mwawo), ndithu iwo adzakumana ndi Mbuye wawo, ndipo ine ndikukuonani monga anthu osazindikira (mbuli).”
“Ndipo ine sindikukuuzani kuti ndili ndi nkhokwe za chuma cha Allah kapena kuti ine ndikudziwa zinthu zamseli, ndiponso sindikunena kuti ndine m’ngelo. Ndiponso sindikunena kwa omwe maso anu akuwachepetsa kuti Allah sadzawapatsa chabwino. Allah akudziwa zam’mitima mwawo. (Ngati nditatero) ndiye kuti ine pamenepo ndili m’gulu la oipa.”
(Iwo) adati: “E iwe Nuh! Watsutsana nafe, ndipo wachulukitsa kutsutsana nafe. Choncho bweretsa kwa ife chimene ukutilonjezacho, ngati ulidi mwa onena zoona.
Adati: “Ndithu Allah achibweretsa kwa inu ngati afuna, ndipo inu simungathe kumulepheretsa (chimene wafuna).”
Kapena akunena (osakhulupirira a m’Makka kuti: “Muhammad) waipeka (Qur’an mwa iye yekha)?” Nena: “ngati ndayipeka ndiye kuti machimo ake (akupekawo) ali pa ine. Ndipo ine ndili kutali ndi zoipa zimene mukuchita.”
“Ndipo khoma chombo moyang’aniridwa ndi Ife, ndi ulangizi wathu (satha kukuchitira choipa), ndipo usandiyankhulitse za iwo amene achita zoipa (kuti ndiwakhululukire). Ndithudi, iwo amizidwa.”
Ndipo adayamba kukhoma chombo. Nthawi iliyonse akamdutsa akuluakulu a mwa anthu ake, adali kumchitira chipongwe. Naye ankanena (kuti): “Ngati inu Mukutichitira chipongwe, nafenso tidzakuchitirani chipongwe monga momwe mukutichitira chipongwe.”
Kufikira pamene lidadza lamulo lathu, madzi naphulika mu uvuni, (chomwe chidali chisonyezo cha Nuh chosonyeza kudza kwa lamulo loona kwa anthu ake) tidamuuza (kuti): “Kweza m’menemo (m’chombo) mtundu uliwonse (wa nyama), ziwiriziwiri, (yaikazi ndi yaimuna), ndi anthu a kubanja lako kupatula omwe chiweruzo (cha Allah) chatsimikizidwa pa iwo (kuti aonongeke), ndipo (atengenso onse) amene akhulupirira.” Komatu ndi ochepa kwambiri amene adakhulupirira pamodzi ndi iye.
Ndipo (Nuh) adati: “Kwerani m’menemo mwadzina la Allah mkuyenda kwake ndi mkukocheza kwake. Ndithu Mbuye wanga Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni zedi.”
Ndipo (chombocho) chidali kuyenda nawo m’mafunde onga mapiri, ndipo Nuh adaitana mwana wake yemwe adali patali (atakana kulowa m’chombo): “Mwana wanga! Kwera pamodzi ndi ife usakhale pamodzi ndi osakhulupirira.”
Ndipo (pambuyo poonongeka onse ndi zonse zomwe Allah adafuna kuti zionongeke), kudanenedwa: “E iwe nthaka! Meza madzi ako. Ndipo iwe thambo! Amange (madzi ako amvula).” Choncho, madzi adaphwa ndipo lamulo lidakwaniritsidwa (loononga anthu oipa). Ndipo (chombo) chidaima pamwamba pa (phiri lotchedwa) Judi, ndipo kudanenedwa: “Aonongeke onse ochita zoipa.”
Ndipo Nuh adafuulira Mbuye wake nati. “E Mbuye wanga! Ndithu mwana wanga ali mgulu la akubanja langa (akuonongedwa). Ndipo ndithu lonjezo lanu ndiloona, ndipo Inu Ndinu Woweruza mwachoonadi kuposa aweruzi onse.”
Kudanenedwa: “E iwe Nuh! Tsika (pa nthaka youma) mwamtendere wochokera kwa Ife, ndipo madalitso ambiri akhale pa iwe ndi pa anthu omwe ali nawe; ndipo kudzakhala mibadwo ina (yoipa pambuyo pako) yomwe tidzaisangalatsa, ndipo kenako chidzaikhudza chilango chowawa chochokera kwa Ife.”
Ndipo anthu (amtundu) wa Âdi, tidawatumizira m’bale wawo Hûd. Adati: “E inu anthu anga! Pembedzani Allah! (Siyani kupembedza mafano). Mulibe mulungu wina koma Iye. Inu simuli kanthu koma ndinu opeka bodza (m’kunena kwanu kwakuti mafano ndi anzake a Allah).”
“Ndipo E inu anthu anga! Pemphani chikhululuko kwa Mbuye wanu, (pa machimo omwe mwakhala mukuchita), kenako lapani kwa Iye. Akutumizirani mitambo yodzetsa mvula yambiri, ndipo akuonjezerani mphamvu pa mphamvu zanu (zomwe muli nazo). Choncho, musatembenuke kukhala oipa.”
(Iwo) adati: “E iwe Hûd! Sudatibweretsere chisonyezo chooneka (chosonyeza kuti ndiwe Mneneri), ndipo ife sitisiya (kupembedza) milungu yathu chifukwa cha zoyankhula zakozo. Ndipo ife sitikukhulupirira.”
“Sitinena kanthu, koma kuti (mwina) milungu yathu ina yakulodza misala.” (Iye) adati: “Ndithu ine ndikupereka umboni kwa Allah ndipo inunso perekani umboni kuti ine ndili kutali ndi zimene mukumphatikiza nazo (Allah pomazipembedza).”
“Kusiya Iye; (milungu yanuyo sindikuiopa ngati ili ndi mphamvu pamodzi ndi inu), tero ndichitireni chiwembu nonsenu, ndipo kenako musandiyembekezere (musandipatse nthawi).”
“Ndithu ine ndatsamira kwa Allah, Mbuye wanga yemwenso ali Mbuye wanu. Palibe chinyama chilichonse koma Allah wachigwira tsumba lake (ndikuchiyendetsa mmene akufunira). Ndithudi, Mbuye wanga Ngwachilungamo.”
“Ngati munyoza (kulandira chimene ndakuuzani palibe vuto kwa ine); ndithu ndafikitsa kwa inu chimene ndatumidwa. Ndipo Mbuye wanga (awaononga osakhulupirira, ndipo) abweretsa anthu ena m’malo mwanu, ndipo inu simungamusautse konse. Ndithu Mbuye wanga ndi Msungi wa chilichonse.”
Ndipo pamene lamulo lathu lidafika (lakuwaononga), tidampulumutsa Hûd ndi amene adakhulupirira pamodzi naye, mwachifundo Chathu, ndipo tidawapulumutsa kuchilango chokhwima.[223]
Ndipo kwa anthu (a mtundu) wa Samud, (tidatuma) m’bale wawo Swaleh. Adati: “E inu anthu anga! Lambirani Allah. Mulibe mulungu wina koma Iye Yekha. Iye adakuumbani ndi nthaka ndi kukukhazikani m’menemo. Ndipo mpempheni chikhululuko (pa zolakwa zanu), kenako tembenukirani kwa Iye. Ndithu Mbuye wanga ali pafupi (ndi akapolo Ake). Ndipo Ngovomera mapempho (aopempha).”
Iwo adati: “E iwe Swaleh! Ndithudi, udali woyembekezeka (kukhala mfumu kwa ife) patsogolo pa izi (usanabwere ndi izi). Ha! Kodi ukutiletsa kulambira zomwe makolo athu adali kulambira? Ndithu ife tili m’chikaiko chokaikira zomwe ukutiitanirazo.”
(Iye) adati: “E inu anthu anga! Mukuona bwanji ngati ndili ndi chisonyezo choonekera chochokera kwa Mbuye wanga (chosonyeza kuona kwa zimenezi), nandipatsanso chifundo chochokera kwa Iye. Nanga ndi yani angandipulumutse ku chilango cha Allah ngati nditamunyoza? Choncho, simungandionjezere china chake koma kutaika basi.”
Koma adaipha. Choncho (Swaleh) adati: “Sangalalani m’midzi yanuyi pamasiku atatu. (Kenako mulangidwa). Limenelo ndi lonjezo osati labodza.”
Choncho pamene lamulo Lathu lidadza (lakuononga midziyo), tidampulumutsa Swalih ndi anthu amene adakhulupirira naye, kukuyaluka kwa tsiku limenelo, mwa chifundo Chathu. Ndithu Mbuye wako ndi Mwini mphamvu, Ngopambana.
Ndipo amene adadzichitira okha zoipa phokoso lalikulu lidawaononga, tero kudawachera m’nyumba zawo ali lambilambi (atafa).
Ndipo ndithu atumiki athu (angelo) adadza kwa Ibrahim ndi uthenga wabwino. (Iwo) adati: “Mtendere!” (Iye) adayankha: “Mtendere (ukhale pa inu!)” Ndipo (Ibrahim) sadakhalitse (adafulumira) kudza nayo nyama yootcha ya thole (mwana wa ng’ombe).
Koma pamene adaona kuti manja awo sakuwatambasula kuchakudya adawadodoma, nadzadzidwa nawo mantha. (Iwo) Adati: “Usaope; ndithu ife tatumidwa kwa anthu a Luti (kuti tikawaononge ndiponso kukupatsa nkhani yabwino).”
Ndipo (m’menemo nkuti) mkazi wake (wa Ibrahim) ali chiimire, ndipo adaseka. Kenaka tidamuuza uthenga wabwino (wakubadwa kwa) Ishaq ndipo pambuyo pa Ishaq, Ya’qub.
(Iye) adati: “Kalanga ine! Ndibereka pomwe ine ndili nkhalamba, ndiponso uyu mwamuna wanga ndi nkhalamba? Ndithudi, ichi ndi chinthu chododometsa.”
Ndithu Ibrahim adali wodekha, wodandaulira Allah komanso wobwerera kwa Iye mwachangu (polapa).
Ndipo atumiki athu pamene adafika kwa Luti, iye anadandaula za iwo ndi kubanika nao mu mtima (chifukwa chosowa njira yowatetezera kwa anthu oipa pomwe iye sadadziwe kuti alendowo ndi angelo), nati: “Lino ndi tsiku lovuta.”
Ndipo anthu ake adadza akuthamangira kwa iye (ku nyumba kwake kuti adzachite zauve ndi alendowo). Ndipo kalenso ankachita zoipa zokhazokhazi, (Luti) adati: “E anthu anga! Nawa asungwana anga; ngoyenera kwa inu (kuwakwatira, osati amuna anzanu) choncho, opani Allah, ndipo musandiyalutse pamaso pa alendo anga. Kodi mwa inu mulibe munthu woongoka?”
(Iwo) adati: “Ndithu ukudziwa bwino kuti tilibe khumbo ndi atsikana ako. Ndipo ndithu iwe ukudziwa bwino chimene tifuna.”
(Iye) adati: “Ndikadakhala nayo mphamvu (yomenyana nanu) kapena kotsamira kolimba kwamphamvu (ndikadalimbana nanu kuti musachite zauve ndi alendowa).”
(Athengawa) adati: “E iwe Luti! Ife ndi athenga a Mbuye wako. Safika kwa iwe (ndi chilichonse choipa). Ndipo choka pamodzi ndi banja lako m’gawo la usiku, ndipo aliyense wa inu asatembenuke (kuyang’ana m’mbuyo akamva mkokomo wa kudza kwa chilangocho), kupatula mkazi wako; iye chimpeza chimene chiwapeze anthu enawo. Ndithu lonjezo lawo ndi m’mawa. Kodi m’mawa suudayandikire?”
Choncho, pamene lidadza lamulo lathu, tidaugadabula (m’zindawo) kumwamba kukhala pansi, pansi kukhala kumwamba, ndipo tidawavumbwitsira mvula ya sangalawe zopangika ndi dongo lotentheka ndi moto, zogwirana kwambiri.
(Sangalawezo) zokhala ndi zizindikiro kwa Mbuye wako. (Sangalawe iliyonse idali ndi mwini wake); ndipo chilango chimenechi sichili kutali ndi anthu oipa.
Ndipo, ku Madiyan tidamtuma m’bale wawo Shuaib, iye adati: “E inu anthu anga! Pembedzani Allah; mulibe mulungu wina koma Iye. Ndipo musachepetse mulingo wa mbale ndi wasikelo (powapimira anthu), ine ndikukuonani kuti ndinu opeza bwino, ndipo ndikukuoperani chilango cha tsiku (lalikulu) lomwe lidzakuzingani.”
“Ndipo E inu anthu anga! Kwaniritsani mulingo wa mbale ndi wasikelo mwachilungamo, ndipo musawachepetsere anthu zinthu zawo (mwachinyengo). Ndipo musafalitse zoipa pa dziko ndi cholinga chodzetsa chisokonezo.”
“Chuma chimene wakusiirani Allah (m’njira yovomerezeka) ndicho chabwino kwa inu ngati muli okhulupirira. Ndipo ine sindine msungi wanu.”
Adati: “E iwe Shuaib! Kodi mapemphero ako akukulamula (kuti utilamule) kuti tisiye zimene makolo athu ankapembedza, kapena kuti tisiye kuchita zimene tifuna pachuma chathu? (Adati mwachipongwe) ndithudi, iwe ndiwe wanzeru, ndi wolungama.”
(Iye) adati: “E inu anthu anga! Mukuona bwanji ngati ndili ndi umboni wowonekera wochokera kwa Mbuye wanga, ndipo nkundipatsa rizq labwino (lahalali) lochokera kwa Iye, (ndisiye zimenezi ndi kusankha njira yokhota)? Ndipo sindifuna kusiyana nanu pochita chimene ndakuletsani. Sindifuna china, koma kukonza mmene ndingathere; ndipo kupambana kwanga (pazimenezi) kuli kwa Allah. Kwa Iye ndatsamira, ndipo kwa Iye ndikutembenukira.”
“Ndipo mpempheni chikhululuko Mbuye wanu ndipo lapani kwa Iye (posiya machimo ndikuchita zabwino). Ndithu Mbuye wanga Ngwachisoni Ngwachikondi chochuluka (kwa anthu Ake).”
(Iwo) adati: “E iwe Shuaib! Sitikumvetsa zambiri mwa zomwe ukunena. Ndipo ife tikukuona wofooka mwa ife. Pakadapanda akubanja lako, tikadakugenda ndi miyala. Ndipo ulibe ulemelero pa ife (koma tikusunga ulemu wa anthu akubanja lako).”[225]
(Iye) adati: “E inu anthu anga! Kodi anthu akubanja kwanga ndiwo olemekezeka kwambiri kwa inu kuposa Allah? Ndipo mwamuyika Iye (Allah) kukhala kumbuyo kwa misana yanu. Ndithu Mbuye wanga zonse zimene mukuchita akuzidziwa bwinobwino.”
“Ndipo E anthu anga! Chitani (zimene mufuna) mmene mungathere; inenso ndichita chimodzimodzi (mmene ndingathere). Posachedwapa mudziwa ndani chimufike chilango chomsambula, ndipo ndani wabodza. Ndipo dikirani inenso ndidikira pamodzi ndi inu.”
Iwo adatsatizidwa ndi tembelero pano pa dziko lapansi ndipo pa tsiku la Qiyâma (adzatsatizidwanso). Taonani kuipa mphoto (yawo) yopatsidwa!
Ndipo sitidawachitire choipa (powaononga). Koma adadzichitira okha zoipa (pakusakhulupirira Allah ndi kupembedza mafano ndikuipitsa pa dziko), milungu yawo yomwe ankaipembedza kusiya Allah siidawathandize chilichonse pamene lidadza lamulo la Mbuye wako (la kuwaononga). Ndipo (milunguyo) siidawaonjezere (china chake) koma chionongeko basi.
Ndipo mmenemo ndi momwe kumakhalira kulanga kwa Mbuye wako pamene alanga anthu a m’mizinda akakhala oipa (pa makhalidwe). Ndithu kulanga kwake (Allah) nkowawa, nkwaukali.
Ndithu m’zimenezi muli lingaliro kwa yemwe akuopa chilango cha tsiku lachimaliziro. Limenelo ndi tsiku losonkhanitsidwa anthu. Ndipo limenelo ndi tsiku lochitiridwa umboni (ndi zolengedwa zonse).
Ndipo sitikulichedwetsa koma m’nthawi yowerengeka (kwa Allah, ngakhale kuti kwa anthu likuoneka kuti lili kutali.)
Tsiku lakudza (zoopsa zake), sadzayankhula aliyense koma mwachilolezo Chake (Allah). Ena adzakhala oipa, ndipo (ena) adzakhala abwino.
Tsono amene adzakhala oipa kobwerera kwawo nkumoto. Iwo adzakhala m’menemo akufuula potulutsa mawu ndi kuwabweza (monga kulira kwa bulu).
Tsono amene adzakhale abwino adzakhala m’Munda wamtendere. Adzakhala mmenemo nthawi yaitali momwe thambo ndi nthaka zidzakhalire, kupatula Mbuye wako akadzafuna; zopatsa (za Mbuye wako ndizo zopatsa) zosatha.
Ndipo ndithu tidampatsa buku Mûsa, koma kusiyana kudabuka mmenemo (pakatanthauzidwe ka bukulo pambuyo pa Mûsa). Pakadapanda mawu a Mbuye wako omwe adatsogola (oti sadzawalanga nthawi isanafike), ndithu kukadaweruzidwa pakati pawo. Ndipo ndithu iwo ali m’kukaika ndi kupeneka (kwakukulu) pa zimenezo.
Choncho (E iwe Mtumiki!) Pitiriza kulungama monga momwe akulamulira (iwe) pamodzi ndi omwe atembenukira (kwa Allah), ndipo musapyole malire. Ndithu Iye akuona zonse zimene muchita.[226]
Ndipo pirira (E iwe Mtumiki! Pokwaniritsa malamulo a Mbuye wako)! Ndithu Allah sataya malipiro a ochita zabwino.
Kupatula omwe Mbuye wako wawachitira chifundo; ndipo chifukwa cha chifundocho, adawalenga (koma okha akusankha zoipa). Ndipo mawu a Mbuye wako akwaniritsidwa (akuti): “Ndithudi, ndizadzadzitsa Jahannam ndi ziwanda ndi anthu onse pamodzi (omwe adali oipa).”
“Ndipo dikirani (chiweruzo cha Allah) nafenso tikudikira.”
Share